Malifalensi a Kabuku ka Umoyo ndi Utumiki
© 2024 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MARCH 3-9
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 3
Muzionetsa kuti Mumadalila Yehova
Miyambo 3:5, 6—“Usamadalile Luso Lako Lomvetsa Zinthu”
“Uzikhulupilila Yehova ndi mtima wako wonse.” Timaonetsa kuti timakhulupilila Mulungu tikamacita zinthu mmene iye akufunila. Tifunika kukhulupilila Mulungu ndi mtima wathu wonse. M’Baibulo mawu akuti mtima nthawi zambili amanena za munthu wamkati, zimene ziphatikizapo mmene munthu amamvela, zolinga zake, mmene amaganizila, komanso mmene amaonela zinthu. Conco, kukhulupilila Mulungu ndi mtima wonse kumaphatikizapo zambili kuposa cabe mmene timamvela. Ndi cisankho cimene timapanga tili otsimikiza kuti Mlengi wathu adziwa zomwe zili zabwino kwa ife.—Aroma 12:1.
“Usamadalile luso lako lomvetsa zinthu.” Popeza ndife opanda ungwilo, tiyenela kudalila Mulungu m’malo modalila luso lathu la kuganiza. Tikamadzidalila kapena kumangocita zinthu potengela mmene tikumvela, tingapange zisankho zomwe poyamba zingaoneke zabwino koma zotsatila zake zingakhale zoipa. (Miyambo 14:12; Yeremiya 17:9) Nzelu za Mulungu n’zapamwamba kwambili kuposa zathu. (Yesaya 55:8, 9) Tikamatsogoleledwa ndi maganizo ake, zinthu zidzatiyendela bwino pa umoyo.—Salimo 1:1-3; Miyambo 2:6-9; 16:20.
Miyambo 3:5, 6—“Usamadalile Luso Lako Lomvetsa Zinthu”
“Uzimukumbukila mʼnjila zako zonse.” Tifunika kudziwa maganizo a Mulungu pa nkhani iliyonse yofunika pa umoyo wathu komanso popanga zisankho zofunika kwambili. Timacita izi tikamamupempha kuti atitsogolele komanso tikamacita zimene amatiuza m’Mawu ake, Baibulo.—Salimo 25:4; 2 Timoteyo 3:16, 17.
“Iye adzawongola njila zako.” Mulungu amawongola njila zathu mwa kutithandiza kuti tizitsatila mfundo zake zolungama pa umoyo wathu. (Miyambo 11:5) Zimenezi zimatithandiza kuti tisakumane ndi mavuto omwe tingathe kuwapewa ndipo timakhala ndi cimwemwe coculuka pa moyo wathu.—Salimo 19:7, 8; Yesaya 48:17, 18.
be-CN 76 ¶4
Khalani Womapitabe Patsogolo
Munthu akaona zambiri m’moyo, angalingalire kuti: ‘Zimenezi sizachilendo kwa ine. Ndikudziŵa zochita.’ Kodi imeneyi ingakhale nzeru? Miyambo 3:7 imachenjeza kuti: “Usadziyese wekha wanzeru.” Inde, kudziŵa zambiri kuyeneradi kutithandiza kuona mbali zosiyanasiyana pochita ndi mikhalidwe ina m’moyo. Koma ngati tikupita patsogolo mwauzimu, kudziŵa kwathu zambiri kuyenera kuthandizanso maganizo athu ndi mitima yathu kudziŵa kuti tifunikira thandizo la Yehova kuti tipambane. Choncho, taona kuti kupita kwathu patsogolo kumaonekera osati mwa kudzidalira tokha pochita ndi mikhalidwe, koma mwa kutembenukira kwa Yehova mwachangu kuti atitsogolere m’miyoyo yathu. Kumaonekera mwa kukhala ndi chidaliro chakuti palibe chingatheke popanda chilolezo chake. Kumaonekeranso mwa kusunga unansi wathu wokhulupirira Atate wathu wakumwamba ndi kumukonda.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06-CN 9/15 17 ¶7
Mfundo Zazikulu za M’buku la Miyambo
3:3. Tiyenera kuona kuti kukhala wokoma mtima mwachikondi ndi wachoonadi ndi makhalidwe amtengo wapatali, ndipo tiyenera kuwasonyeza ngati mmene tingachitire ndi mkanda wa pakhosi womwe uli wokwera mtengo. Tikufunikiranso kukhomereza makhalidwe amenewa pamtima pathu, kuwachititsa kukhala mbali yaikulu ya moyo wathu.
MARCH 10-16
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 4
“Uteteze Mtima Wako”
Kodi Tingauteteze Bwanji Mtima Wathu?
4 Pa Miyambo 4:23, liwu lakuti “mtima” litanthauza umunthu wa mkati. (Welengani Sal. 51:6, komanso mawu a m’munsi.) M’mawu ena, “mtima” uphatikizapo zimene timaganiza, mmene timamvelela, zolinga zathu, komanso zimene timalaka-laka. “Mtima” ni umunthu wathu weni-weni wa mkati, osati cabe maonekedwe akunja.
Kodi Tingateteze Bwanji Mtima Wathu?
10 Kuti tikwanitse kuteteza mtima wathu, tifunika kudziŵa zimene zingauwononge na kucitapo kanthu mwamsanga kuti tiucinjilize. Liwu lakuti ‘kuteteza’ pa Miyambo 4:23 litikumbutsa za nchito ya mlonda. M’nthawi yakale, mlonda anali kukhala pamwamba pa mpanda wa mzinda, ndipo akaona kuti kukubwela adani, anali kucenjeza anthu. Kuganizila zimene alonda anali kucita, kungatithandize kudziŵa zimene tifunika kucita kuti tisalole Satana kuipitsa maganizo athu.
11 M’masiku akale, mlonda anali kuseŵenza mothandizana ndi alonda a pa geti ya mzinda. (2 Sam. 18:24-26) Capamodzi, iwo anali kuteteza mzinda wawo mwa kuonetsetsa kuti mageti onse ni otseka ngati kukubwela adani. (Neh. 7:1-3) Cikumbumtima cathu cophunzitsidwa Baibo naconso cimagwila nchito ngati mlonda wathu. Cimaticenjeza ngati Satana afuna kuwononga mtima wathu wophiphilitsa. M’mawu ena, cimaticenjeza ngati Satana afuna kutisonkhezela kukhala na maganizo oipa, zolinga, kapena zilakolako zoipa. Conco, nthawi zonse cikumbumtima cathu cikaticenjeza, tifunika kumvetsela na kutseka geti ya mtima wathu, titelo kukamba kwake.
Kodi Tingateteze Bwanji Mtima Wathu?
14 Kuti titeteze mtima wathu, tifunika kuutseka kuti musaloŵe zinthu zimene zingauipitse. Koma nthawi zina tiyenela kumautsegula kuti muloŵe zinthu zabwino. Ganizilaninso za citsanzo ca mzinda wokhala na mpanda. Mlonda wa pa geti anali kutseka geti ya mzinda kuti adani asaloŵe. Koma nthawi zina, anali kuitsegula pofuna kupeleka mpata woloŵetsa zakudya na zinthu zina mu mzindawo. Cikanakhala kuti mageti sanali kutsegulidwa, sembe anthu anali kufa na njala. Mofananamo, tifunika kumatsegula mtima wathu kaŵili-kaŵili kuti maganizo a Mulungu azititsogolela.
w12-CN 5/1 32 ¶2
“Tetezani Mtima Wanu!”
N’chifukwa chiyani tiyenera kuteteza mtima wathu wophiphiritsira? Mulungu anauzira Mfumu Solomo kulemba kuti: “Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa, pakuti mumtimamo ndiye muli akasupe a moyo.” (Miyambo 4:23) Kuti tikhale ndi moyo wabwino panopo komanso kuti tidzapeze moyo wosatha m’tsogolo zimadalira mmene mtima wathu wophiphiritsira ulili. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Mulungu amaona zimene zili mumtima mwathu. (1 Samueli 16:7) Mulungu akafuna kudziwa kuti ndife munthu wotani amayang’ana “munthu wobisika wamumtima” kapena kuti zimene zili mumtima mwathu.—1 Petulo 3:4.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Kodi Mudzayembekezela Yehova Moleza Mtima?
4 Miyambo 4:18 imatiuza kuti, “njila ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezeleka mpaka tsiku litakhazikika.” Lembali, lionetsa bwino mmene Yehova amathandizila anthu ake kumvetsa colinga cake mwa pang’ono-pang’ono. Limagwilanso nchito poonetsa mmene Mkhristu amapitila patsogolo kuuzimu. Kukula mwauzimu safulumizitsa, kumatenga nthawi. Tiyenela kuŵelenga Mawu a Mulungu mwakhama na kuseŵenzetsa malangizo ake, komanso ocokela ku gulu lake. Tikatelo, pang’ono-m’pang’ono tidzayamba kukulitsa makhalidwe amene Khristu anali nawo. Kuwonjezela apo, cidziŵitso cathu ponena za Mulungu cidzawonjezeleka. Onani mmene Yesu anamveketsela mfundo imeneyi.
MARCH 17-23
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 5
Thawani Ciwelewele
w00-CN 7/15 29 ¶1
Mukhoza Kudzisunga M’dziko Lachiwerewereli
M’mwambiwu, munthu wopulupudza akusonyezedwa monga “mkazi wachiwerewere.” Mawu amene amakopa nawo anthu amene amagona nawo ndi otsekemera monga chisa cha uchi ndi osalala kuposa mafuta a azitona. Kodi kunyengererana zachiwerewere nthaŵi zambiri sikuyamba moteremu? Mwachitsanzo, talingalirani zimene zinachitikira mlembi wina wokongola wa zaka 27 wotchedwa Amy. Iye anati: “Mwamuna ameneyu kuntchito kwathu amachita zinthu zambiri zosonyeza kuti amandifuna ndipo amanditamanda nthaŵi iliyonse. N’zosangalatsa kuti ena amakuganizira. Koma ndikutha kuona bwino lomwe kuti akusangalala nane kokha kuti adzagone nane. Sindinganyengeke ndi zochita zakezo.” Mawu osyasyalika a mwamuna kapena mkazi wokopa ena kaŵirikaŵiri amakhala abwino pokhapokha ngati tazindikira pamenedi akuchokera. Pa chifukwachi tikufunika kugwiritsa ntchito luso lathu la kulingalira.
w00-CN 7/15 29 ¶2
Mukhoza Kudzisunga M’dziko Lachiwerewereli
Zotsatira za chiwerewere n’zoŵaŵa monga chivumulo ndipo n’zakuthwa monga lupanga lakuthwa konsekonse—n’zopweteka ndiponso n’zakupha. Kuvutika mumtima, kutenga mimba yosaifuna, kapena matenda opatsirana mwakugonana kaŵirikaŵiri ndizo zotsatira zoŵaŵa za khalidwe loterolo. Ndipo talingalirani za kuvutika maganizo kwakukulu kumene amakhala nako mnzake wa muukwati wa munthu wosakhulupirikayo. Kachitidwe ka kusakhulupirika kamodzi kokha kangachititse mabala akuya kwambiri oti angakhale kwa moyo wonse. Inde, chiwerewere chimavulaza.
w00-CIN 7/15 29 ¶5
Mukhoza Kudzisunga M’dziko Lachiwerewereli
Tifunika kutalikirana kwambiri monga momwe tingathere ndi anthu achiwerewere omwe angatisonkhezere. Kodi n’kudziyanikiranji pa njira zawo mwa kumvetsera nyimbo zolaula, kuonerera zosangalatsa zoipa, kapena kumaona zithunzi zolaula? (Miyambo 6:27; 1 Akorinto 15:33; Aefeso 5:3-5) Ndipotu n’kupusa kwambiri kukopa chidwi chawo mwa kuseŵera nawo kapena mwa kusakhala wachikatikati m’kavalidwe ndi podzikongoletsa!—1 Timoteo 4:8; 1 Petro 3:3, 4.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w00-CN 7/15 29 ¶7
Mukhoza Kudzisunga M’dziko Lachiwerewereli
Motero Solomo akunenetsa mavuto aakulu ogwera m’chiwerewere. Chigololo ndi kutaya ulemu, kapena kudzilemekeza, zimayendera pamodzi. Kodi si zochititsadi manyazi kuti munthu ungokhala chabe wokhutiritsa chilakolako chako choipa cha kugonana kapena cha munthu wina? Kodi sizisonyeza kusadzilemekeza kugonana ndi munthu wina amene sitinakwatirane naye?
MARCH 24-30
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 6
Kodi Tingaphunzile Ciyani Kwa Nyelele?
it-1-E 115 ¶1-2
Nyelele
‘Nzelu Zacibadwa.’ ‘Nzelu’ za nyelele zisimabwela cifukwa cakuti nyelele zimaganiza mocitila zinthu, koma n’zacibadwa ndipo ndi mmene Mlengi anazipangila. Baibulo imanena kuti nyelele ‘zimakonza cakudya cawo m’cilimwe ndipo zimasonkhanitsa cakudya cawo pa nthawi yokolola.’ (Miy. 6:8) Mtundu wina wa nyelele umene umapezeka kwambili m’dziko la Palestine, wochedwa harvester ant, kapena kuti nyelele zokolola, zimasonkhanitsa cakudya coculuka m’nyengo ya cilimwe ndi m’nyengo yotentha. Ndipo zimadya cakudya cimeneco m’nyengo zina, kuphatikizapo nyengo yozizila pamene cakudya cimakhala covuta kupeza. Nyelele zimenezi zimakhala kumalo opunthila, kumene mbewu zimakhala zoculuka. Ngati m’nyontho wa mvula wafika pamene pali mbewuzo, nyelele zimenezi zimatenga mbewuzo n’kuziika pa dzuwa kuti ziume. Nyelele zimenezi zimadziwikanso kuti zimadya mtima wa mbewu kuti mbewuzo zisamele pamene zili mu malo osungilako cakudya. Nyelele zimenezi zimadziwikanso mosavuta cifukwa zimadzela njila imodzimodzi ndipo zimasiya makoko a mbewu polowela m’dzenje.
Makhalidwe Amene Tingatengele. Conco, kudziwako zocepa zimene nyelele zimacita kumapeleka mphamvu ku cenjezo lakuti: “Pita kwa nyelele waulesi iwe, ukaone mmene imacitila zinthu kuti ukhale wanzelu.” (Miy. 6:6) Nyelele sizimangodziwika kuti zimakonzekelatu zamtsogolo, koma zimadziwikanso kuti n’zolimbikila pa nchito. Nthawi zambili zimanyamula zinthu zolemela kuposa mphamvu zawo, ndipo zimacita zonse zotheka kuti zikwanitse nchito ina yake, ndipo sizileka ngakhale zitagwa kapena kugubuduka pa malo otsetseleka. Cina cocititsa cidwi n’cakuti nyelele zimacita zinthu mogwilizana kwambili. Motelo zimasunga zisa zawo zili zaukhondo ndipo zimasamalilana. Nthawi zina zimathandizila nyelele yovulala, kapena yotopa kubwelela ku cisa.
w00-CN 9/15 26 ¶3-4
Tetezani Dzina Lanu
Mofanana ndi nyelele, kodi nafenso sitifunikira kuchita khama? Kugwira ntchito molimbika ndi kuyesetsa kuti tichite bwino pantchito yanthu n’kwabwino kwa ife kaya pali wotiyang’anira kapena ayi. Inde, kusukulu, kuntchito kwathu, komanso pogwira ntchito zauzimu ndi anzathu, tiyenera kuchita bwino koposa. Monga momwe nyerere zimapindulira ndi khama lawo, momwemonso Mulungu akufuna kuti ‘tione zabwino m’ntchito zathu zonse.’ (Mlaliki 3:13, 22; 5:18) Chikumbumtima chabwino ndi chikhutiro ndizo mphoto ya kugwira ntchito molimbika.”—Mlaliki 5:12.
Pogwiritsa ntchito mafunso aŵiri odzutsa chidwi, Solomo akuyesa kugalamutsa waulesi kuti asachite zala lende, akumati: “Udzagona mpaka liti, waulesi iwe? Udzauka ku tulo tako liti?” Mwa kuyerekezera kulankhula kwa munthu waulesi, mfumuyo ikupitiriza kuti: “Tulo ta pang’ono, kuodzera pang’ono, kungomanga manja pang’ono, ndi kugona; ndipo umphaŵi wako udzafika ngati mbala, ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa [“msilikali,” NW].” (Miyambo 6:9-11) Pamene waulesi akadagona, umphawi umam’fikira mofulumira ngati wakuba, ndipo kusauka kumam’kantha ngati munthu wonyamula lupanga. Minda ya munthu waulesi siichedwa kumera thengo ndi khwisa. (Miyambo 24:30, 31) Bizinesi yake imaloŵa pansi pa kanthaŵi kochepa. Kodi wolemba anthu ntchito angalekerere waulesi kwautali wotani? Ndipo kodi wophunzira amene n’ngwaulesi n’kuŵerenga angayembekezere kuchita bwino kusukulu?
Kufufuza Cuma Cauzimu
w00-CN 9/15 27 ¶3
Tetezani Dzina Lanu
Zinthu zisanu ndi ziŵiri zomwe miyambo akutchula ndizo zikuluzikulu ndipo zikuphatikizamo pafupifupi mitundu yonse ya machimo. “Maso akunyada” ndi “mtima woganizira ziŵembu zoipa” ndi machimo omwe amachitidwa m’maganizo. “Lilime lonama” ndi “mboni yonama yonong’ona mabodza” ndiwo machimo apakamwa. “Manja akupha anthu osachimwa” ndi “mapazi akuthamangira mphulupulu mmangummangu” ndizo machitachita onyansa. Ndipo chomwe Yehova amadana nacho kwambiri ndicho mthirakuŵiri yemwe amakondwera kwambiri kuyambanitsa anthu omwe akanatha kukhalira limodzi mwamtendere. Kuwonjezeka kwa chiŵerengerocho kuchoka pa zisanu ndi chimodzi kufika pa zisanu ndi ziŵiri kukusonyeza kuti ndandandayo sinafike kumapeto, chifukwa chakuti anthu akupitirizabe kuwonjezera zoipa zomwe amachita.
MARCH 31–APRIL 6
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 7
Pewani Zinthu Zimene Zingakugwetseleni M’mayeselo
w00-CN 11/15 29 ¶5
“Sunga Malangizo Anga, Nukhale ndi Moyo”
Zenera lomwe Solomo ankasuzumira linali ndi made—mwachionekere made ameneŵa anali amatabwa ndipo mwinamwake ozokotedwa mwaukatswiri. Pamene cheza cha dzuŵa lamadzulo chikuchepa, mdima wausiku ukugwa m’msewumo. Ndiyeno akuona mnyamata yemwe akuonekeratu kuti ali pangozi. Mopanda luntha, kapena kuti mosalingalira bwino, akuchita mopanda nzeru. N’zodziŵikiratu kuti akudziŵa bwino zochitika za m’dera lomwe wapitalo ndi zomwe zingam’chitikire kumeneko. Mnyamatayu akuyandikira “mphambano ya pa mkaziyo,” yomwe ili m’njira yopita kunyumba ya mkaziyo. Kodi mkaziyu ndani? Nanga akuchita chiyani?
w00-CN 11/15 30 ¶4-6
“Sunga Malangizo Anga, Nukhale ndi Moyo”
Mkazi ameneyu ali m’pakamwa pochenjeretsa. Kankhope kali gwaa! Alankhula mawu akewo molimba mtima. Chilichonse chimene akunena, akuchinena mochenjera kwambiri kuti akope mnyamatayo. Mwa kunena kuti wapereka nsembe yoyamika tsiku lomwelo, ndi kuchita choŵinda chake, akufuna kudzionetsa ngati ndi wachilungamo, kutsimikizira kuti mkhalidwe wake wauzimu ndi wabwino. Nsembe zoyamika ku kachisi wa ku Yerusalemu zinkaphatikizapo nyama, ufa, mafuta, ndi vinyo. (Levitiko 19:5, 6; 22:21; Numeri 15:8-10) Popeza kuti wopereka nsembe amatha kutenga chigawo china cha nsembe yoyamika ndi kukadya limodzi ndi banja lake, choncho mkaziyu akufotokoza kuti kunyumba kwake kuli zakudya ndi zakumwa zochuluka. Mfundo yake n’njodziŵikiratu, iye akutanthauza kuti: Mnyamatayo akasangalala kwambiri kumeneko. Wachoka kunyumba kwakeko kwenikweni kudzafunafuna iyeyu basi. Komatu munthu atati akhulupirire nkhani imeneyo ingam’gwire mtima kwabasi koma angalembe m’madzi. Katswiri wina wodziŵa za Baibulo anati: “N’zoona kuti anatuluka kukafunafuna winawake, koma kodi anatuluka kukafuna mnyamata wake ameneyu yekha basi? Wopanda nzeru—mwinamwake mnyamata ameneyu—ndi amene angam’khulupirire mkaziyu.”
Atadzikometsera ndi zovala zake, ndi mngoli wa timawu take tosyasyalika, ndi mmene anam’kumbatirira mnyamatayu, komanso mmene anam’mpsompsonera, mkazi wonyengerera ameneyu akufuna am’kope pogwiritsa ntchito zonunkhira. Akuti: “Ndayala zopfunda pakama panga, nsalu zamaŵangamaŵanga za thonje la ku Aigupto, ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhira a mvunja ndi chisiyo ndi mtanthanyerere.” (Miyambo 7:16, 17) Wayala kama wake mwaukatswiri ndi nsalu zokongola za ku Aigupto ndi kuthirapo mafuta onunkhira apamtima pake a mvunja, chisiyo, ndi mtanthanyerere.
“Tiye tikondwere ndi chikondano mpaka mamaŵa,” iye akupitiriza motero, “tidzisangalatse ndi chiyanjano,” [“tisangalatsane ndi chikondi,” NW]. Akumuitanira zinazake osati chakudya chokoma chokha cha anthu aŵiri. Akum’lonjeza kukasangalala mwa kugonana. Kwa mnyamatayu, pempholitu n’lochititsa chidwi ndi losangalatsa! Popitiriza kum’nyengerera, akunena kuti: “Pakuti mwamuna kulibe kwathu, wapita ulendo wa kutali; watenga thumba la ndalama m’dzanja lake, tsiku lowala mwezi adzabwera kwathu.” (Miyambo 7:18-20) Akum’tsimikizira kuti palibe aliyense adzawapezerera, chifukwa chakuti mwamuna wake wachoka wapita kukachita bizinesi ndipo akakhala kumeneko kwakanthaŵi ndithu asanabwerere kunyumba. N’katswiridi pokopa mnyamata ndi mawu onyengerera! “Am’kakamiza ndi kukoka kwa mawu ake, am’patutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yake.” (Miyambo 7:21) Munthu wanzeru ndi wakhalidwe labwino ngati Yosefe, ndi yekhayo angathe kupeŵa mawu onyengerera ngati ameneŵa. (Genesis 39:9, 12) Kodi mnyamata uyu angathe kupeŵa mkhalidwewu?
w00-CN 11/15 31 ¶2
“Sunga Malangizo Anga, Nukhale ndi Moyo”
Pempholi linali losapeŵeka kwa mnyamata ameneyu. Mopanda nzeru, akutsatira mkaziyu ‘monga ng’ombe yopita kukaphedwa’. Monga momwe mwamuna womangidwa unyolo m’miyendo sangathe kuthaŵa chilango, momwemonso mnyamatayo akukokedwera m’tchimo. Sakuona kuopsa kwake kufikira pamene ‘muvi upyoza chiŵindi chake,’ kapena kuti mpaka pamene walandira chilonda chomwe chingathe kumupha. Angafedi chifukwa chakuti angatenge matenda akupha opatsirana mwa kugonana. Chilondacho chingamuphenso mwauzimu; ‘angawononge moyo wake.’ Umunthu wake wonse ndi moyo wake womwe zili pangozi yaikulu, ndipo wachimwira kwambiri Mulungu. Chotero athamangira m’msampha wa imfa monga mbalame yothamangira m’msampha!
Kufufuza Cuma Cauzimu
w00-CN 11/15 29 ¶1
“Sunga Malangizo Anga, Nukhale ndi Moyo”
“Uwamange [malangizo anga] pa zala zako, uwalembe pamtima pako.” (Miyambo 7:3) Monga zala zomwe timaziona mosavuta ndikuti zimatithandiza pochita zomwe tikufuna, momwemonso zimene timaphunzira m’malangizo a m’Malemba kapena popeza chidziŵitso cha m’Baibulo ziyenera kumatikumbutsa nthaŵi zonse ndi kutitsogolera pa chilichonse chomwe timachita. Tilembe malangizoŵa pamtima pathu, kuwapanga kukhala chotisonkhezera.
APRIL 7-13
CUMA COPEZEA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 8
Mvelani Yesu Amene Amachedwa Nzelu
cf-CN 131 ¶7
“Ndimakonda Atate”
7 Mu vesi 22, nzeru ikunena kuti: “Ine ndinali woyamba kulengedwa ndi Yehova, ndinali woyambirira pa zinthu zonse zimene anapanga kalekale kwambiri.” Lembali silikungonena za nzeru zenizeni chifukwa nzeru sizinachite “kulengedwa.” Nzeru zilibe chiyambi chifukwa Yehova wakhala alipo kuyambira kalekale ndipo nthawi zonse ndi wanzeru. (Salimo 90:2) Koma Mwana wa Mulungu ali ndi chiyambi chifukwa ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” Iye anachita kupangidwa kapena kuti kulengedwa ndipo ndi woyamba pa zonse zimene Yehova analenga. (Akolose 1:15) Mwanayu analipo Mulungu asanalenge dziko lapansi komanso kumwamba ngati mmene buku la Miyambo likufotokozera. Monga Mawu, kapena kuti wolankhula m’malo mwa Mulungu, iye anasonyeza bwino kwambiri nzeru zimene Yehova ali nazo.—Yohane 1:1.
cf-CN 131-132 ¶8-9
“Ndimakonda Atate”
8 Kodi Mwanayu ankachita chiyani pa nthawi yonse imene anali kumwamba asanabwere padziko lapansi? Vesi 30 likusonyeza kuti Yesu anali pambali pa Mulungu monga “mmisiri waluso.” Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Lemba la Akolose 1:16 limanena kuti: “Kudzera mwa iye, Mulungu analenga zinthu zina zonse kumwamba ndi padziko lapansi . . . Analenga zinthu zina zonse kudzera mwa iye ndiponso chifukwa cha iye.” Choncho Yehova, yemwe ndi Mlengi, anagwiritsa ntchito Mwana wake, amene ndi Mmisiri Waluso, polenga zinthu zonse monga angelo kumwamba, zinthu zonse zakuthambo, dziko lapansi ndi zinthu zonse zodabwitsa monga zomera komanso nyama. Analenganso munthu, yemwe ndi wapamwamba kuposa chinthu chilichonse padziko lapansi. Mgwirizano wa Atate ndi Mwana wakeyu tingauyerekezere ndi wa katswiri wolemba mapulani a nyumba ndi mmisiri wake amene amatsatira mapulaniwo pomanga nyumba. Tikamachita chidwi ndi zinthu zosiyanasiyana zachilengedwe, kwenikweni timakhala tikutamanda Yehova, Katswiri Wamkulu Wolemba Mapulani. (Salimo 19:1) Komanso tingakumbukire mgwirizano wabwino umene unalipo kwa nthawi yaitali pakati pa Mlengi ndi ‘mmisiri wake waluso’ ameneyo.”
9 Anthu awiri opanda ungwiro akamagwira ntchito limodzi nthawi zina amasemphana maganizo. Koma si mmene zinalili pakati pa Yehova ndi Mwana wake. Mwanayu anagwira ntchito limodzi ndi Atate wake kwa nthawi yaitali kwambiri ndipo iye ananena kuti: “Ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.” (Miyambo 8:30) Iye ankasangalala kukhala ndi Atate wake ndipo ankakondana kwambiri. Mwanayu anayamba kuchita zinthu mofanana kwambiri ndi Atate wake ndipo anatengera makhalidwe ake. Mpake kuti Atate ndi Mwanayu anayamba kukondana kwambiri. Choncho tinganene motsimikiza kuti palibe amene amakondana kwambiri kuposa Atate ndi Mwana wakeyu. Iwo anayamba kukondana kalekale.
w09-CN 4/15 31 ¶14
Kuzindikira Yesu Monga Davide Wamkulu Ndiponso Solomo Wamkulu
14 Ndi munthu mmodzi yekha amene anali ndi nzeru kuposa Solomo. Munthu ameneyu anali Yesu Khristu. Iye anadzitcha kuti “wina woposa Solomo.” (Mat. 12:42) Mawu a Yesu anali “mawu amoyo wosatha.” (Yoh. 6:68) Chitsanzo cha zimenezi ndi mfundo zimene iye ananena mu ulaliki wapaphiri. Mfundo zimenezi zimafotokoza bwino lomwe zinthu zimene Solomo ananena m’miyambi yake ndipo zimatithandiza kumvetsa miyambiyo. Solomo anafotokoza zinthu zosiyanasiyana zimene zingawathandize atumiki a Yehova kukhala osangalala. (Miy. 3:13; 8:32, 33; 14:21; 16:20) Yesu anatsindika mfundo yakuti zimene zimabweretsa chisangalalo chenicheni ndi zinthu zokhudza kulambira Yehova komanso kukwaniritsidwa kwa malonjezo ake. Iye ananena kuti: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, popeza ufumu wa kumwamba ndi wawo.” (Mat. 5:3) Anthu amene amagwiritsa ntchito mfundo zimene Yesu anaphunzitsa amakhala pa ubwenzi ndi Yehova, yemwe ndi “chitsime cha moyo.” (Sal. 36:9; Miy. 22:11; Mat. 5:8) Zoonadi, Khristu ndi “nzeru za Mulungu.” (1 Akor. 1:24, 30) Monga Mfumu Mesiya, Yesu Khristu ali ndi “mzimu wanzeru.”—Yes. 11:2.
Kufufuza Cuma Cauzimu
g-CN 5/14 16
‘Nzeru Ikufuula’ Kodi Inuyo Mukuimva?
▪ Buku lina linanena kuti: “Baibulo ndi buku lomwe lafalitsidwa komanso kumasuliridwa kambirimbiri m’zinenero zambiri kuposa buku lililonse.” (The World Book Encyclopedia) Baibulo lonse kapena mbali yake likupezeka m’zinenero pafupifupi 2,600. Izi zikusonyeza kuti anthu 90 pa 100 alionse angathe kukhala nalo m’chinenero chawo. Pamenepatu tingati nzeru ikufuula.
▪ Koma nzeru ‘imafuula mokweza’ m’njira inanso. Lemba la Mateyu 24:14 limati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto [a dziko loipali] adzafika.”
APRIL 14-20
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 9
Khalani Munthu Wanzelu, Osati Wonyoza
“Mvela Mawu a Anthu Anzelu”
4 Kukamba zoona, cingativute kulandila uphungu umene wapelekedwa mwacindunji. Tingafike ngakhale pokhumudwa. Cifukwa ciani? Olo kuti timavomeleza kuti ndife opanda ungwilo, cingativute kulandila uphungu munthu akatichulila mbali ina yake imene tinalakwitsa. (Ŵelengani Mlaliki 7:9.) Tingayambe kupeleka zifukwa zodzilungamitsa. Komanso tingakaikile zolinga za wopeleka uphunguyo, kapena tingakhumudwe na mmene waupelekela. Tingafike ngakhale pa kumupeza zifukwa, n’kumadziuza kuti: ‘Ameneyu sanganipatse uphungu, nayenso ali n’zolakwa zake.’ Ndipo ngati tiona kuti uphungu umene tapatsidwa si wotiyenelela, tingaunyalanyaze, kapena tingafunsile kwa ena amene tikudziŵa kuti adzatipatsa uphungu umene tingakonde.
“Mvela Mawu a Anthu Anzelu”
12 N’ciani cingatithandize kulandila uphungu? Kudzicepetsa. Tizikumbukila kuti ndife anthu opanda ungwilo, ndipo nthawi zina tingacite zinthu mopanda nzelu. Yobu amene tachula uja, anali na maganizo olakwika. Koma pambuyo pake iye anawongolela maganizo ake, ndipo Yehova anam’dalitsa. Cifukwa ciani? Cifukwa Yobu anali wodzicepetsa. Kudzicepetsa kwake kunaonekela pamene analandila uphungu kwa Elihu, ngakhale kuti Elihu anali wocepelepo kwa iye. (Yobu 32:6, 7) Mofananamo, kudzicepetsa kudzatithandiza nafenso kuseŵenzetsa uphungu ngakhale pamene taona kuti sitinafunikile kupatsidwa uphunguwo, kapena ngati amene watipatsa uphunguwo ni wocepelapo kwa ife. Mkulu wina ku Canada anati: “Popeza sitimadziona mmene ena amationela, tingapite bwanji patsogolo popanda wina wotipatsa uphungu?” Ndani wa ife safuna kupita patsogolo pokulitsa zipatso zimene mzimu woyela umabala, komanso pocita utumiki wathu wacikhristu?—Ŵelengani Salimo 141:5.
13 Tiziona uphungu kukhala cikondi ca Mulungu pa ife. Yehova amatifunila zabwino. (Miy. 4:20-22) Iye akatipatsa uphungu kupitila m’Mawu ake, m’zofalitsa zozikika pa Baibo, kapena Mkhristu wokhwima mwauzimu, ndiye kuti amatikonda. Iye “amatilanga kuti tipindule,” malinga n’kunena kwa Aheberi 12:9, 10.
14 Ikani maganizo pa uphunguwo osati mmene aupelekela. Nthawi zina, tingaone kuti uphungu umene tapatsidwa sunapelekedwe m’njila yabwino. N’zoona kuti aliyense wopeleka uphungu, ayenela kuupeleka m’njila yakuti zisakhale zovuta kuulandila. (Agal. 6:1) Koma ngati ndife tikupatsidwa uphungu, tingacite bwino kusumika maganizo pa phindu la uphunguwo, ngakhale pamene taona kuti sunapelekedwe m’njila yabwino. Tingadzifunse kuti: ‘Ngakhale kuti sin’nakonde mmene uphungu wapelekedwela, kodi pali cina cake cimene niphunzilapo pa uphunguwo? Kodi sininganyalanyaze zophophonya za wopeleka uphunguwo n’colinga cakuti nipindule nawo?’ N’cinthu canzelu kwa ife kuona mmene tingaseŵenzetsele uphunguwo kuti tipindule.—Miy. 15:31.
w01-CN 5/15 30 ¶1-2
‘Ndi Nzeru Masiku Athu Adzachuluka’
Munthu wanzeru amaona kudzudzulidwa mosiyana ndi mmene wonyoza amakuonera. Solomo anati: “Dzudzula wanzeru adzakukonda. Ukachenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yake.” (Miyambo 9:8b, 9a) Munthu wanzeru amadziŵa kuti “chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwe[re]tsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.” (Ahebri 12:11) Ngakhale uphungu ukhale wopweteka, kodi pali chifukwa chochitira ukali kapena kuukana ngati kuulandira kudzatiwonjezera nzeru?
“Ukaphunzitsa wolungama adzawonjezera kuphunzira,” ikupitiriza motero mfumu yanzeru. (Miyambo 9:9b) Aliyense ayenera kupitiriza kuphunzira kaya wanzeru kwambiri kapena wokalamba kwambiri. N’zosangalatsa kwambiritu kuona ngakhale okalamba akulandira choonadi ndi kudzipatulira kwa Yehova! Nafenso tiyeni tiyesetse kukhalabe ndi mtima wofuna kuphunzira ndi kugwiritsa ntchito ubongo wathu.
w01-CN 5/15 30 ¶5
‘Ndi Nzeru Masiku Athu Adzachuluka’
Ndi udindo wa aliyense kuyesetsa kupeza nzeru. Ponenetsa mfundo imeneyi, Solomo anati: “Ukakhala wanzeru, si yakoyako nzeruyo? Ndipo ukanyoza udzasauka wekha.” (Miyambo 9:12) Munthu wanzeru amapindula nayo yekha, koma wonyoza adzavutika yekha. Ndithudi, timakolola zomwe tinafesa. Tsono tiyenitu ‘titchere makutu athu ku nzeru.’—Miyambo 2:2.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06-CN 9/15 17 ¶5
Mfundo Zazikulu za M’buku la Miyambo
9:17—Kodi “madzi akuba” n’ciyani,” Ndipo n’cifukwa ciyani ‘amatsekemera’? Popeza kuti Baibulo limayerekezera kusangalala ndi kugonana kumene kumachitika muukwati ndi kumwa madzi otsitsimula otungidwa pachitsime, madzi akuba akuimira kuchita zachiwerewere mobisa. (Miyambo 5:15-17) Maganizo ochita zachiwerewere popanda kugwidwa ndiwo amene amachititsa kuti madzi oterowo azioneka ngati otsekemera.
APRIL 21-27
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 10
Tingatani Kuti Tikhale Ndi Cimwemwe Ceniceni?
w01-CN 7/15 25 ¶1-3
‘Madalitso Ali pa Wolungama’
Wolungama amapindulanso m’njira ina. “Wocita ndi dzanja laulesi amasauka; koma dzanja la akhama lilemeletsa. Wokolola m’malimwe ndi mwana wanzelu; koma wogona pakututa ndi mwana wocititsa manyazi.”—Miyambo 10:4, 5.
Mawu a mfumuŵa akutanthauza zambiri makamaka kwa ogwira ntchito yotuta. Nthaŵi yotuta si nthaŵi yogona. Ndi nthaŵi yogwira ntchito mwakhama kwa maola ochuluka. Ndithudi imeneyi imakhala nthaŵi yofunika kuchita changu.
Pamene Yesu anali kulingalira za kututa anthu osati zokolola zakumunda, anauza ophunzira ake kuti: “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta [Yehova Mulungu] kuti akokose antchito kukututa kwake.” (Mateyu 9:35-38) M’chaka cha 2000, anthu oposa 14 miliyoni anafika pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu; kuŵirikiza kaŵiri chiŵerengero cha Mboni za Yehova. Motero ndani angatsutse kuti ‘m’minda mwayera kufikira kumweta’? (Yohane 4:35) Olambira oona amapempha Mwini ntchito kuti atumize antchito ena. Akamatero amakhalanso akudzipereka zolimba m’ntchito yopanga ophunzira mogwirizana ndi mapemphero awowo. (Mateyu 28:19, 20) Ndipotu Yehova wadalitsa khama lawo mosaneneka! M’chaka chautumiki cha 2000, munabatizidwa anthu atsopano oposa 280,000. Ameneŵanso amayesetsa kukhala aphunzitsi a Mawu a Mulungu. Tikhaletu achimwemwe ndi okhutira panthaŵi yotuta ino mwa kugwira nawo mokwanira ntchito yopanga ophunzira.
w01-CN 9/15 24 ¶3-4
Yendani ‘M’njira Yoongoka’
Solomo akufotokoza kufunika kwa chilungamo. Anati: “Chuma cha wolemera ndi mudzi wake wolimba; koma umphaŵi wawo uwononga osauka. Ntchito za wolungama zipatsa moyo; koma phindu la oipa lichimwitsa.”—Miyambo 10:15, 16.
Chuma chingatchinjirize kumavuto ena amene angagwe mwadzidzidzi, monga momwe tauni yam’mpanda nthaŵi zina imatchinjirizira anthu amene akukhalamo. Ndipo umphaŵi ungakhale wopweteka pakagwa vuto mwadzidzidzi. (Mlaliki 7:12) Komabe, mfumu yanzeruyo inalangizanso za ngozi zokhudza chuma ndi umphaŵi womwe. Munthu wolemera angamakhulupirire chuma chake chokha basi, n’kumaganiza kuti zinthu zamtengo wapatali zimene ali nazozo ndizo “khoma lalitali.” (Miyambo 18:11) Nayenso munthu wosauka angamaganize molakwika kuti alibe tsogolo lililonse chifukwa cha umphaŵi wakewo. Motero, onsewo amalephera kukondweretsa Mulungu.
it-1-E 340
Dalitso
Yehova Kudalitsa Anthu. “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeletsa munthu, ndipo popeleka madalitsowa Mulungu sawonjezelapo ululu.” (Miy. 10:22) Yehova amadalitsa anthu amene amawayanja mwa kuwateteza, kucititsa kuti zinthu ziwayendele bwino, kuwatsogolela, kuwapatsa cipambano, komanso kuwapatsa zofunikila zawo. Ndipo zotulukapo zake zimakhala zowapindulila.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06-CN 5/15 30 ¶18
Ubwino Woyenda Mwangwiro
18 “Madalitso a Yehova” ndiwo akuthandiza anthu ake kuti zinthu ziziwayendera bwino mwauzimu. Ndipo akutitsimikizira kuti “sawonjezerapo chisoni.” (Miyambo 10:22) Ndiyeno n’chifukwa chiyani ambiri mwa anthu okhulupirika a Mulungu amakumana ndi mavuto ndiponso mayesero, omwe amachititsa kuti azivutika kwambiri? Timavutika chifukwa cha zinthu zitatu makamaka. (1) Zochita zathu zauchimo. (Genesis 6:5; 8:21; Yakobo 1:14, 15) (2) Satana ndi ziwanda zake. (Aefeso 6:11, 12) (3) Dziko loipa. (Yohane 15:19) Ngakhale kuti Yehova amalola kuti zinthu zoipa zizitichitikira, sikuti iye ndiye amachititsa zinthuzo. Ndipotu, “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko.” (Yakobo 1:17) Madalitso a Yehova sabweretsa mavuto.
APRIL 28–MAY 4
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 11
Zimene Simuyenela Kukamba
w02-CN 5/15 26 ¶4
Kuongoka Mtima Kumatsogolera Olungama
Kuwongoka mtima kwa olungama ndiponso zimene woipa amachita zimakhudzanso anthu ena. Mfumu ya Israyeli inati: “Wonyoza Mulungu awononga mnzake ndi m’kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziŵa.” (Miyambo 11:9) Kodi alipo angatsutse zoti bodza, miseche, mawu otukwana, ndi njerengo zachabe zimavulaza ena? Kusiyana ndi zimenezi, wolungama amalankhula zabwino, amaganiza kaye asanalankhule, ndiponso amaganizira ena. Wolungama amapulumuka mwa zimene akudziŵa chifukwa kuwongoka mtima kwake kumam’thandiza kukhala ndi umboni wofunika kusonyeza kuti anthu amene akumuimba mlandu ndi abodza.
w02-CN 5/15 27 ¶2-3
Kuongoka Mtima Kumatsogolera Olungama
Anthu amene amachita zinthu zolungama pamudzi amalimbikitsa mtendere ndi moyo wabwino ndiponso amalimbikitsa ena. Motero, amakuza mudzi, zinthu zimayenda bwino pamudzipo. Amene amalankhula zojeda anzawo, zokhumudwitsa, ndiponso zinthu zachabe amayambitsa chisokonezo, chisoni, kusagwirizana ndi mavuto. Zimenezi zimakhala choncho makamaka ngati amene akuchita zimenezo ndi anthu amene ali ndi udindo pamudzipo. Pamudzi wotero pamakhala chisokonezo, katangale, makhalidwe oipa ndiponso mwina mavuto a zachuma.
Mfundo ya pa Miyambo 11:11 imagwiranso ntchito chimodzimodzi kwa anthu a Yehova akamasonkhana pamodzi m’mipingo yawo yonga midzi. Anthu auzimu—amene amatsatira kuwongoka mtima—akamatsogolera mpingo, anthu mumpingomo amakhala achimwemwe, okangalika ndiponso amakhala othandiza. Zimenezi zimalemekeza Mulungu. Yehova amadalitsa mpingowo, ndipo umayenda bwino mwauzimu. Nthaŵi zina, anthu ochepa odandaula ndi osakondwa, omwe amapeza anzawo zifukwa ndipo amalankhula moipidwa ndi mmene zinthu zikuyendera, ali ngati ‘muzu woŵaŵa’ umene ungafalikire ndi kuipitsa anthu ena amene poyamba analibe maganizo otero. (Ahebri 12:15) Nthaŵi zambiri anthu oterowo amafuna mpando ndi kutchuka. Amayambitsa mphekesera zakuti mumpingomo kapena akulu sakuchita chilungamo, pali kusankhana mafuko, kapena zinthu zina. Pakamwa pawo pangagaŵanitsedi mpingo. Kodi si bwino kusamvera zimene akunena ndi kuyesetsa kukhala anthu auzimu amene tingalimbikitse mtendere ndi mgwirizano mumpingo?
w02-CN 5/15 27 ¶5
Kuongoka Mtima Kumatsogolera Olungama
Inde, munthu wosazindikira, kapena ‘wosoŵa nzeru’ amayambitsa mavuto aakulu. Kulankhula kwake kosadziletsa amafika nako pochita miseche kapena kuchita chipongwe. Akulu oikidwa ayenera kuthetsa zinthu zoipa ngati zimenezi mwamsanga. Kusiyana ndi ‘wosoŵa nzeru,’ munthu wozindikira amadziŵa pamene afunikira kutonthola. Amabisa mawu, m’malo mowanditsa zinsinsi. Munthu wozindikira amakhala “wokhulupirika mtima” chifukwa amadziŵa kuti lilime lingavulaze kwambiri ngati salilamulira. Amakhulupirika kwa okhulupirira anzake ndipo saulula nkhani zachinsinsi zimene zingawaike pangozi. Anthu oongoka mtima ameneŵa amapindulitsa mpingo!
Kufufuza Cuma Cauzimu
g20.1 11, bokosi
Zimene Mungacite Kuti Muthane na Nkhawa
“KUKOMA MTIMA KUNGAKUTHANDIZENI KUCEPETSA NKHAWA”
“Munthu wosonyeza kukoma mtima kosatha amapindulitsa moyo wake, koma munthu wankhanza amacititsa kuti thupi lake linyanyalidwe.”—MIYAMBO 11:17.
Buku lakuti Overcoming Stress lili na mutu wakuti, “Kukoma Mtima Kungakuthandizeni Kucepetsa Nkhawa.” Malinga na zimene mlembi wina, Dr. Tim Cantopher anakamba, kucita zinthu mokoma mtima ndi ena, kungathandize munthu kukhala na thanzi labwino komanso wacimwemwe. Kumbali ina, munthu wankhanza ndi wopanda cifundo sakhala wacimwemwe cifukwa ena samukonda ndipo amamupewa.
Tifunikanso kucita zinthu modziganizila kuti ticepetse nkhawa. Mwacitsanzo, tisadzipanikize kucita zinthu zimene sitingakwanitse. Komanso, sitifunika kudziona kuti ndife acabe-cabe kapena osafunika. Yesu Khristu anati: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.”—Maliko 12:31.