Malifalensi a Kabuku ka Umoyo ndi Utumiki
© 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MAY 5-11
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 12
Kugwila Nchito Mwakhama Kumapindulitsa
Khalidwe la Mtengo Wapatali Kuposa Dayamondi
Akhristu ena amavutika kwambili kuti apeze zofunika pa moyo. Koma m’malo mocita cinyengo, amagwila nchito mwakhama. Apa amasonyeza kuti kukhala ndi makhalidwe a Yehova monga kuona mtima, n’kofunika kwambili kuposa ciliconse.—Miy. 12:24; Aef. 4:28.
Kodi Mungatani Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yanu?
Kuganizila funso lomalizali n’kothandiza kwambili cifukwa cakuti munthu amasangalala kwambili ndi nchito yake ngati akuona kuti ikupindulitsa anthu ena. Yesu anati: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” (Machitidwe 20:35) Tikamagwila nchito, pali anthu amene amapindula monga makasitomala ndiponso anthu amene anatilemba nchito. Kuonjezela pamenepa, palinso anthu ena amene amapindula ndi nchito imene timagwila. Anthu amenewa ndi a m’banja lathu ndiponso anthu ena ovutika.
Anthu a m’banja lanu. Mwamuna amene amagwila nchito mwamphamvu kuti asamalile banja lake amathandiza anthu a m’banjalo m’njila ziŵili. Coyamba, amawapezela zinthu zofunika monga cakudya, zovala, ndi malo ogona. Mwanjila imeneyi, iye amakwanilitsa udindo wake wocokela kwa Mulungu wosamalila “anthu amene ndi udindo wake kuwasamalila.” (1 Timoteyo 5:8) Caciŵili, munthu amene amasamalila banja lake mwakhama amathandiza a m’banja lake kuona kuti kugwila nchito mwamphamvu n’kofunika. Shane, amene tamuchula m’nkhani yapita, anati: “Atate anga ndi munthu wolimbikila nchito kwambili. Iwo ndi munthu woona mtima amene wakhala akugwila nchito mwamphamvu nthawi zonse, ndipo nchito imene agwila kwa nthawi yaitali ndi ya ukalipentala. Cifukwa ca citsanzo cao, ndaphunzila kuti ndiyenela kugwila nchito mwamphamvu kuti ndicite zinthu zimene zingathandize ena.”
Anthu ena ovutika. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu anzake ‘kugwila nchito molimbikila . . . kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.’ (Aefeso 4:28) Kunena zoona, ngati tigwila nchito mwamphamvu timapeza zosowa zathu ndi za banja lathu, ndipo tingathandizenso anthu ena ovutika. (Miyambo 3:27) Conco kugwila nchito mwamphamvu kungatithandize kukhala wosangalala kwambili ngati timathandizanso ena.
Kufufuza Cuma Cauzimu
ijwyp-CN nkhani 95 ¶10-11
Kodi Ndine Wopirira?
● Muziona mavuto anu moyenera. Muzitha kusiyanitsa pakati pa mavuto aakulu ndi mavuto aang’ono. Baibulo limanena kuti: “Munthu amene amasonyeza mkwiyo wake tsiku lomwelo ndi wopusa, koma wochenjera akachitiridwa chipongwe, amangozinyalanyaza.” (Miyambo 12:16) Choncho si mavuto onse amene ayenera kukusowetsani mtendere.
“Kusukulu, anzanga ambiri amakonda kudandaula pa zinthu zosafunika n’komwe. Ndiye anzawo akakawachemerera pa intaneti, amaganiza kuti akuchita bwino, m’malo moti aone zinthu moyenera n’kupeza njira yothetsera vutolo.”—Joanne.
MAY 12-18
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
MIYAMBO 13
Musapusitsidwe ndi “Nyale ya Anthu Oipa”
w03-CN 9/15 24 ¶5-6
“Malamulo A Wanzeru” Ndiwo Kasupe wa Moyo
Nyali ikuimira chomwe timadalira kuti tiŵalitse njira yathu m’moyo. ‘Mawu a Mulungu ndiwo nyali ya ku mapazi kwa wolungama, ndi kuunika kwa panjira yake.’ (Salimo 119:105) M’mawuwo muli zinthu zambiri ndiponso nzeru zosaneneka za Mlengi. Pamene timamvetsa bwino zolinga ndi zofuna za Mulungu, m’pamenenso kuunika kwauzimu kumene kumatitsogolera kumaŵala kwambiri. N’zosangalatsatu kwambiri zimenezi! Ndiyeno kodi palinso chifukwa chosokonezekera ndi nzeru za dzikoli kapena zinthu zimene anthu amanama kuti ndi nzeru?—1 Akorinto 1:20; Akolose 2:8; 1 Timoteyo 6:20.
Kwa woipa, zilibe kanthu kuti nyali yake ingaoneke yoŵala bwino motani ndiponso kuti akuoneka kuti zinthu zikumuyendera bwino motani, nyali yake idzazima. Mapeto ake adzakhala mumdima, momwe angathe kuphunthwa. Komanso, “sadzalandira mphoto.”—Miyambo 24:20.
w12-CN 7/15 12 ¶3
Tumikirani Mulungu Amene Amapereka Ufulu
Ngati Satana anakwanitsa kunyengerera anthu awiri angwiro komanso angelo ena kuti akane ulamuliro wa Mulungu, ifenso akhoza kutinyengerera. Satana sanasinthe. Iye amayesetsa kutipusitsa kuti tiziganiza zoti mfundo za Mulungu ndi zolemetsa ndipo zimatiletsa kusangalala. (1 Yoh. 5:3) Anthu ambiri amaganiza choncho ndipo ngati timacheza nawo kwambiri, nafenso tikhoza kutengera maganizo amenewa. Mlongo wina wa zaka 24, amene anachita chiwerewere, anati: “Ndinayamba kutengera maganizo oipa a anzanga chifukwa chakuti sindinkafuna kuoneka wosiyana nawo.” Mwina nanunso mumavutika kukhala osiyana ndi anzanu.
w04-CN 7/15 31 ¶6
“Yense Wochenjera Amachita Mwanzeru”
Munthu wanzeru ndiponso woongoka mtima amene amachita zinthu mozindikiradi amadalitsidwa. Solomo anatitsimikizira kuti: “Wolungama adya nakhutitsa moyo wake; koma mimba ya oipa idzasoŵa.” (Miyambo 13:25) Yehova amadziŵa zimene zingatipindulitse m’njira zosiyanasiyana pa moyo wathu, kaya n’zokhudza moyo wathu wa m’banja, ubwenzi wathu ndi ena, utumiki wathu, kapenanso kupatsidwa malangizo. Ndipo tikachita mwanzeru potsatira malangizo a m’Mawu ake, ndithu tidzakhala ndi moyo wosangalala kwambiri.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w08-CN 4/1 14 ¶4
Kulera Bwino Ana M’dziko Lolekererali
N’chifukwa chake lemba la Miyambo 13:24, limati: “Wolekerera mwana wake osam’menya amuda; koma wom’konda am’yambize kum’langa.” Palembali, chilango chikutanthauza njira ina iliyonse imene makolo angagwiritse ntchito powongolera ana awo. Makolo amayesetsa kulangiza ana awo mwachikondi powongolera zolakwa zawo. Koma ngati angawalekerere, anawo angazolowere khalidwe loipalo ndipo lingadzawalowetse m’mavuto. Choncho, n’zoonekeratu kuti ngati makolo akulekerera ana, ndiye kuti sakuwakonda.
MAY 19-25
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 14
Muzicita Zinthu Mosamala Panthawi ya Tsoka
Yamikilani Mphatso ya Mulungu ya Moyo
Koma pali zocitika zina zosaletseka zoika moyo pa ciopsezo, monga ngozi zacilengedwe, milili, komanso nkhondo. Ngakhale n’telo, zinthu zimenezi zikacitika, timacita zotheka kuti tidziteteze potsatila malangizo omwe boma limapeleka. (Aroma 13:1, 5-7) Koma matsoka ena n’zotheka ndithu kuwakonzekela pasadakhale. Conco, cingakhale canzelu kutsatila malangizo alionse a boma otithandiza kukonzekela matsokawo. Mwacitsanzo, cingakhale cothandiza kusungilatu madzi na cakudya cosawonongeka msanga, komanso kabokosi ka mankhwala ogwilitsa nchito munthu akadwala mwadzidzidzi.
Kodi tiyenela kucita ciyani ngati matenda oyambukila akufalikila m’dela lathu? Tiyenela kumvela malangizo a boma amene angapelekedwe, monga okhudza kusamba m’manja, kukhala motalikilana, kuvala mamasiki, na kubindikilitsidwa. Kutsatila malangizo ngati amenewa kumaonetsa kuti timayamikila kwambili mphatso ya moyo imene Mulungu anatipatsa.
Matsoka akacitika, nthawi zina timamva nkhambakamwa zambili kwa mabwenzi athu, maneba athu, komanso m’nkhani zofalitsidwa. M’malo mongokhulupilila “mawu alionse” amene tamvela, tingacite bwino kukhulupilila zimene a boma komanso zimene madokotala odalilika anena. (Ŵelengani Miyambo 14:15.) Bungwe Lolamulila na maofesi a nthambi amacita zonse zotheka kuti akhale na cidziŵitso colondola asanapeleke citsogozo pa nkhani yokhudza misonkhano ya mpingo na nchito yolalikila. (Aheb. 13:17) Tikatsatila citsogozo cimene angapeleke, timadziteteza komanso kuteteza ena. Izi zingathandizenso kuti mpingo ukhale na mbili yabwino m’dela lathu.—1 Pet. 2:12.—1 Pet. 2:12.
Khalani Wolimba Mtima Monga Zadoki
Kodi tingakhale bwanji olimba mtima monga Zadoki, akatipempha kuti tithandize abale m’nthawi yovuta? (1) Tsatilani malangizo. Pa nthawi zovuta ngati zimenezo tifunikila tizikhalabe ogwilizana. Tsatilani malangizo ocokela ku ofesi ya nthambi. (Aheb. 13:17) Akulu nthawi zonse ayenela kumabwelelamo m’malangizo kuti azikhala okonzeka komanso odziŵa mocitila tsoka likagwa. (1 Akor. 14:33, 40) (2) Khalani olimba mtima komabe osamala. (Miy. 22:3) Ganizilani mofatsa musanacitepo kanthu. Musaike moyo wanu pa ciopsezo mwadala. (3) Dalilani Yehova. Kumbukilani kuti Yehova amasamala kwambili za moyo wanu komanso wa abale amene mufuna kuthandiza. Iye angakuthandizeni kuti mupeleke thandizo kwa abale anu muli otetezeka.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w05-CN 7/15 19 5-6
“Wochenjera Asamalira Mayendedwe Ake”
M’chinenero choyambirira, mawu amene anawamasulira kuti “ziwembu” ali ndi matanthauzo awiri. Mawuwa angatanthauze kuzindikira kapena kuchenjera. (Miyambo 1:4; 2:11; 3:21) Mawuwa angatanthauzenso maganizo oipa kapena kuganizira za chiwembu.—Salmo 37:7; Miyambo 12:2; 24:8.
Ngati m’chinenero choyambiriracho mawuwa akutanthauza “ziwembu,” n’kosavuta kuona chifukwa chake munthu wotero amadedwa. Koma ngati tanthauzo lake lili la wozindikira kapena wochenjera, kodi munthu wotero angamadedwe chifukwa chiyani? Kodi sizoona kuti munthu wozindikira angamadedwe ndi anthu osazindikira? Mwachitsanzo, amene mwanzeru amasankha ‘kusakhala a dziko lapansi,’ amadedwa ndi dziko. (Yohane 15:19) Achinyamata achikristu amene mwanzeru satengera zochita zosayenera za anzawo kuti apewe makhalidwe oipa amanyozedwa. Mfundo ndi yakuti opembedza oona amadedwa ndi dzikoli lomwe lili m’manja mwa Satana Mdyerekezi.—1 Yohane 5:19.
MAY 26–JUNE 1
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 15
Thandizani Ena Kukhala Acimwemwe
w10-CN 11/15 31 ¶16
Tidzayenda Mogwirizana Ndi Mtima Wathu Wosagawanika!
Yobu anali ndi mtima wochereza. (Yobu 31:31, 32) Ngakhale kuti sindife olemera, tikhoza ‘kukhala ochereza.’ (Aroma 12:13) Tikhoza kugawana ndi ena zinthu zochepa zimene tili nazo podziwa kuti, “ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi, kusiyana ndi kudya nyama ya ng’ombe yamphongo yodyetsedwa bwino pali chidani.” (Miy. 15:17) Kudya chakudya chosalira zambiri koma pali mtendere ndi mtumiki mnzathu wokhulupirika kumakhala kosangalatsa ndiponso kopindulitsa mwauzimu.
Tiyeni Tilimbikitsane, Ndipo Tiwonjezele Kucita Zimenezi”
N’kulakwa kuganiza kuti sitingakwanitse kulimbikitsa ena cifukwa cakuti ndise osamasuka kweni-kweni na ŵanthu. Kulimbikitsa ena sikulila zambili. Mwina mungangomwetulila popatsa moni munthu. Ngati iye sakumwetulila, ndiye kuti mwina pali cinacake cimene cikumuvutitsa maganizo, ndipo kungomumvetsela pamene akamba nkhawa zake kungamulimbikitse.—Yak. 1:19.
M’bale wina wacicepele, dzina lake Henri, cinamuŵaŵa kwambili mu mtima pamene abululu ake anasiya coonadi, kuphatikizapo atate ŵake, amene anali mkulu wodziŵika. Henri analimbikitsiwa na woyang’anila dela amene anapita naye ku lesitilanti kukamwa naye tiyi. Kumeneko, anamulola kufotokoza momasuka mmene anali kumvelela. Pambuyo pa makambilanowo, Henri anazindikila kuti njila yokha imene akanathandizila a m’banja lake kubwelela m’coonadi ni kupilila ciyeso cimeneco mokhulupilika. Iye analimbikitsiwa ngako mwa kuŵelenga Salimo 46; Zefaniya 3:17; na Maliko 10:29, 30.
Zitsanzo zimene takambilana, ca Marthe ndi ca Henri, zionetsa kuti tingakwanitse kulimbikitsa m’bale kapena mlongo wathu amene afunikila citonthozo. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenela ndi abwino kwambili. Maso owala amapangitsa mtima kusangalala. Uthenga wabwino umanenepetsa mafupa.” (Miy. 15:23, 30) Kuwonjezela apo, kuŵelenga Nsanja ya Mlonda kapena zofalitsa za pa webusaiti yathu kungalimbikitse munthu wopanikizika m’maganizo. Komanso, Paulo anaonetsa kuti kuimba nyimbo za Ufumu capamodzi kungakhale kolimbikitsa. Iye analemba kuti: “Pitilizani kuphunzitsana ndi kulangizana mwa masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu, ndi nyimbo zauzimu zogwila mtima. Pitilizani kuimbila Yehova m’mitima yanu.”—Akol. 3:16; Mac. 16:25.
Kufufuza Cuma Cauzimu
ijwbq-CN nkhani 39 ¶3
Kodi Mkhristu Angalandire Chithandizo cha Mankhwala Akadwala?
2. Kodi ndifunse maganizo madokotala ena ndisanalandire chithandizochi? Kumva maganizo a anthu ambiri kukhoza kukuthandizani kusankha bwino, makamaka ngati matenda anuwo ndi aakulu.—Miyambo 15:22.
JUNE 2-8
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
MIYAMBO 16
Mafunso Atatu Amene Angatithandize Kupanga Zisankho Zabwino
Pangani Zosankha Mwanzelu Mukali Acinyamata
Timakhala ndi cimwemwe coculuka cifukwa cotumikila Yehova. (Miy. 16:20) Baruki, mlembi wa Yeremiya, anaiŵala mfundo imeneyi. Panthawi ina, kutumikila Yehova sikunali kum’sangalatsa. Conco Yehova anamuuza kuti: “Iwe ukufuna-funabe zinthu zazikulu. Leka kuzifuna-funa. Anthu onse ndikuwagwetsela tsoka ndipo iwe ndidzakupatsa moyo wako monga cofunkha cako kulikonse kumene ungapite.” (Yer. 45:3, 5) Kodi muganiza n’ciani cikanacititsa Baruki kukhala wacimwemwe? Kodi ndi kufuna-funa zinthu zazikulu kapena kupulumuka cionongeko ca Yerusalemu monga mtumiki wokhulupilika wa Mulungu?—Yak. 1:12.
M’bale wina amene anapeza cimwemwe potumikila ena ndi Ramiro. Iye anati: “Ndinakulila m’banja losauka m’mudzi wa ku maphili a Andes. Conco, pamene mkulu wanga ananena kuti adzandilipilila maphunzilo a ku yunivesite, ndinaona kuti unali mwai waukulu. Panthawi imeneyo, ndinali nditangobatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Panthawi imodzi-modziyo, mpainiya wina anandipempha kuti ndipite kukalalikila naye ku tauni ina yaing’ono. Ndinapita kumeneko ndipo ndinaphunzila kumeta tsitsi, ndiyeno ndinatsegula malo anga ometela tsitsi kuti ndizipezako zofunika. Pamene tinali kuphunzitsa anthu Malemba, ambili analabadila. Pambuyo pake ndinagwilizana ndi mpingo umene unangokhazikitsidwa kumene ndipo unali kugwilitsila nchito cinenelo camakolo anga. Tsopano ndakhala muutumiki wa nthawi zonse kwa zaka 10. Palibe nchito iliyonse imene ingandipatse cimwemwe cofanana ndi cimene ndimakhala naco pothandiza anthu kuphunzila za uthenga wabwino m’cinenelo cao”
w13 9/15 17 ¶1-3
Kodi Mwasandulika?
TONSEFE timacita zinthu mogwilizana ndi mmene tinaleledwela ndiponso anthu amene timakhala nao. Cifukwa ca zimenezi, timakonda zovala zina zake, zakudya zina zake ndi kucita zinthu m’njila ina yake.
Koma pali zinthu zina zofunika kwambili kupambana zakudya ndi zovala zimene timasankha. Mwacitsanzo, tinaphunzila kuona zinthu zina kukhala zabwino ndi zoyenela komanso kuona zinthu zina kukhala zoipa ndi zosayenela. Timaona zinthu zimenezi mosiyana ndi mmene ena amazionela. Zosankha zathu zimaonetsa mmene cikumbumtima cathu cilili. Potsimikizila mfundo imeneyi, Baibo imanena kuti nthawi zambili ‘anthu a mitundu amene alibe cilamulo amacita mwacibadwa zinthu za m’cilamulo.’ (Aroma 2:14) Kodi izi zitanthauza kuti ngati palibe lamulo lacindunji la Mulungu ndiye kuti tingacite zinthu mongotsatila zocita ndi miyezo ya anthu amene timakhala nao?
Akristu samacita zinthu mongotsatila zocita ndi miyezo ya anthu amene amakhala nao. Pali zifukwa ziŵili zimene io sacitila zimenezi. Coyamba, Baibo imati: “Pali njila yooneka ngati yoongoka kwa munthu, koma mapeto ake ndi imfa.” (Miy. 16:25) Cifukwa copanda ungwilo, anthufe tilibe nzelu zokwanila ndipo sitingakwanitse kuongolela mapazi athu. (Miy. 28: 26; Yer. 10:23) Caciŵili, Baibo imanena kuti Satana “mulungu wa nthawi ino” ndi amene amacilikiza mfundo zimene anthu amayendela. (2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19) Conco, ngati tifuna kuti Yehova atidalitse ndi kutiyanja, tiyenela kutsatila malangizo a pa Aroma 12:2.—Welengani.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1-E 629
Cilango
Zotsatilapo za Kumvela Komanso Kusamvela. Anthu oipa, zitsilu, kapena anthu amakhalidwe otayilila amaonetsa kuti amadana ndi cilango ca Yehova mwa kucikanilatu cilango cimeneco. (Sal. 50:16, 17; Miy. 1:7) Ucitsilu wawo umakhala ndi zotsatilapo zoipa zimene zimacititsa kuti alangidwe, ndipo nthawi zambili cilango cimeneci cimakhala cacikulu. Monga mmene mwambi wina umanenela: “Zitsilu zimalangidwa ndi kupusa kwawo komwe.” (Miy. 16:22) Amadzibweletsela mavuto monga umphawi, kucititsidwa manyazi, matenda, ngakhalenso imfa ya mwamsanga. Mbili ya Aisiraeli ionetsa kukula kwa mavuto amene angakhalepo. Iwo sanalabadile cilango cimene anapatsidwa kudzela mwa aneneli pamene anapatsidwa uphungu komanso kuwongoleledwa. Sanamvelenso cilango cimene Yehova anawapatsa pamene analeka kuwateteza komanso kuwadalitsa. Pothela pake, analandila cilango cacikulu cimene cinali citanenedwelatu, iwo anagonjetsedwa ndi kutengedwa ku ukapolo.—Yer. 2:30; 5:3; 7:28; 17:23; 32:33; Hos. 7:12-16; 10:10; Zef. 3:2.
JUNE 9-15
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 17
Khalani Mwamtendele mu Ukwati Wanu
g-CN 9/14 11 ¶2
Mungatani Kuti Musamasunge Chakukhosi
Dzifufuzeni moona mtima. Baibulo limasonyeza kuti anthu ena ‘amakonda kukwiya’ komanso ‘amakonda kupsa mtima.’ (Miyambo 29:22) Kodi ndi mmene inuyo mulili? Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndine munthu wosachedwa kupsa mtima? Kodi sindichedwa kukhumudwa? Nanga kodi ndimakhumudwa ngakhale pa nkhani yaing’ono?’ Baibulo limati, “amene amangokhalira kulankhula za nkhani inayake amalekanitsa mabwenzi apamtima.” (Miyambo 17:9; Mlaliki 7:9) Zimenezi zingachitikenso m’banja. Choncho ngati mumakonda kusunga chakukhosi, mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndingatani kuti ndizileza mtima mwamuna kapena mkazi wanga akandikhumudwitsa?’—Lemba lothandiza: 1 Petulo 4:8.
w08-CN 5/1 10 ¶6–11 ¶1
Kuthetsa Mavuto
1. Sankhani nthawi yoti mukambirane vutolo. Kanthu kali konse kali ndi nthawi yake, . . . mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula.” (Mlaliki 3:1, 7) Monga mmene taonera mu mkangano umene uli koyambirira kwa nkhani ino, mavuto ena angachititse kuti mupsetsane mitima. Pokambirana vuto linalake, mukaona kuti mwayamba kupsetsana mitima, siyani kaye kukambirana nkhaniyo. Kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo otsatirawa kungateteze ukwati wanu. “Chiyambi cha ndewu chifanana ndi kutsegulira madzi; tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.”—Miyambo 17:14.
Komabe, palinso “mphindi yakulankhula.” Mofanana ndi udzu m’munda, mavuto amakula kwambiri mukawalekerera. Choncho musanyalanyaze vutolo poganiza kuti litha lokha. Ngati mwagwirizana kuti musiye kaye nkhaniyo, lemekezani mnzanuyo mwa kusankha nthawi ina yoyenera yoti mukambirane. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni nonse kuti mutsatire malangizo a m’Baibulo akuti: “Dzuwa lisalowe muli chikwiyire.” (Aefeso 4:26) Motero, yesetsani kukwaniritsa zimene mwagwirizanazo.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-1-E 790 ¶2
Diso
Zimene munthu amacita ndi maso ake zimaonetsa bwino mmene akumvela mumtima. Maso a munthu angaonetse cifundo kapena ayi (Deut. 19:13); ‘angatsinzinile’ kapena ‘kupsinyila’ mosakondwa, kapena pokonza ciwembu. (Sal. 35:19; Miy. 6:13; 16:30) Munthu amene safuna kumvela kapena amaene safuna kucitila wina zina zake anganenedwe kuti watseka kapena kuphimba maso ake. (Mat. 13:15; Miy. 28:27) Baibulo limanena kuti maso a munthu wopusa sakhala pamalo amodzi, koma amangoyendayenda uku ndi uku “mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” Maganizo ake amangoyendayenda ndipo saganizila zinthu zofunika. (Miy. 17:24) Ngakhale thanzi la munthu, mphamvu, kapena cimwemwe cake zimaoneka m’maso mwake. (1 Sam. 14:27-29; Deut. 34:7; Yobu 17:7; Sal. 6:7; 88:9) Mfumu Yehosafati anauza Yehova kuti: “Maso athu ali pa inu.”—2 Mbiri 20:12.
JUNE 16-22
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 18
Muzilankhula Mawu Olimbikitsa Kwa Amene Akudwala
Nzelu Yeniyeni Imafuula
Muziyamba mwaganiza musanalankhule. Ngati sitisamala, mawu athu akhoza kupweteka ena. Baibo imati: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizila ndi mawu olasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzelu limacilitsa.” (Miy. 12:18) Timateteza ubale wathu na anthu ena ngati timapewa kuwajeda pa zolakwa zawo. (Miy. 20:19) Kuti mawu athu akhale ocilitsa osati opweteka ena, tiyenela kudzaza mitima yathu na cidziŵitso copezeka m’Mawu a Mulungu. (Luka 6:45) Ndipo tikamasinkhasinkha zimene Baibo imakamba, mawu athu adzakhala monga “citsime ca nzelu” cimene cimatsitsimutsa ena.—Miy. 18:4.
mrt-CN nkhani 19 bokosi
Zimene Zingakuthandizeni Ngati Mwayamba Kudwala Mwadzidzidzi
Muzimvetsera akamalankhula. Njira yabwino kwambiri yothandizira mnzanu ndi kumvetsera akafuna kulankhula nanu. Musaganize kuti muyenera kuyankha pa chilichonse chimene wanena. Nthawi zambiri kungomvetsera n’kokwanira. Muzipewa kumuweruza koma muziyesetsa kumumvetsa. Musamangoganiza kuti mukudziwa mmene akumvera m’thupi, makamaka ngati sakuoneka kuti akudwala.—Miyambo 11:2.
Muzinena zinthu zolimbikitsa. Mwina mungasowe choti munene. Koma m’malo mongokhala chete, munganene zinthu zochepa zosonyeza kuti mwamumvetsa. Zimenezi zingamulimbikitse. Mwachitsanzo, ngati mulibe zonena, yesetsani kungonena mawu osavuta koma ochokera mumtima ngati kuti “Sindidziwa zimene ndinganene, koma dziwani kuti ndimakukondani.” Koma musamanene mawu ngati akuti “Pali anthu ena omwe akuvutika kwambiri kuposa inuyo” kapena akuti “Bola inuyo chifukwa simukudwala matenda a . . . ”
Mungasonyeze kuti mumamufunira zabwino mukamayesetsa kudziwa zambiri zokhudza matenda ake. N’zosakayikitsa kuti adzayamikira zimenezi ndipo mudzatha kumuuza zinthu zothandiza. (Miyambo 18:13) Koma musamangopereka malangizo okhudza matenda ake ngati sanakupempheni.
Muzimuthandiza. M’malo mongoganiza zimene mungachite pomuthandiza, muzimufunsa zimene mungachite. Koma muzikumbukira kuti mwina mnzanuyo sangavomere kuti akufunikira kuthandizidwa chifukwa sakufuna kukuvutitsani. Ngati zili choncho, muzimuuza zinthu zimene mungachite monga kukamugulira zinthu zofunika, kumugwirira ntchito zapakhomo kapena zinthu zina.—Agalatiya 6:2.
Musataye mtima. Mnzanu akamadwala, nthawi zina mwina sangakwanitse kuchita zimene munagwirizana kapenanso sangafune kucheza nanu. Muzimulezera mtima n’kumumvetsa. Pitirizani kumayesetsa kumuthandiza.—Miyambo 18:24.
Mmene Tingathandizile Odwala Matenda a Maganizo
“Lankhulani molimbikitsa.”—1 ATESALONIKA 5:14.
Mnzanu wodwala matenda a maganizo angakhale na nkhawa, kapena angamavutike na maganizo odziona ngati wosafunika. Conco, muyenela kum’tsimikizila kuti mumam’konda. Mukatelo, mungamutonthoze na kum’limbikitsa, ngakhale kuti simudziŵa mawu eni-eni amene mungakambe.
“Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse.”—MIYAMBO 17:17.
M’thandizeni mnzanuyo pa zimene akufunikila. M’malo moganiza kuti mudziŵa mmene mungamuthandizile, mufunseni zimene mungacite pomuthandiza. Ngati mnzanuyo zikumuvuta kufotokoza zimene akufunika, yesani kupeleka malingalilo a zinthu zimene mungacitile pamodzi, monga kupita kokayenda. Kapena mungamuthandizeko kukagula zinthu, kuyeletsa, kapena nchito zina.—Agalatiya 6:2.
“Khalani oleza mtima.”—1 ATESALONIKA 5:14.
Si nthawi zonse pamene mnzanu angakhale wokonzeka kulankhula. Conco, muuzeni kuti ndinu wokonzeka kumumvetsela nthawi iliyonse imene angafune kukamba nanu. Cifukwa ca matenda ake, mnzanu angakambe kapena kucita zinthu zina zimene zingakukhumudwitseni. Iye angasinthe maganizo pa zinthu zimene munagwilizana kucitila limodzi komanso angakhumudwe. Koma khalani oleza mtima, ndiponso muzimumvetsa pamene mukumuthandiza.—Miyambo 18:24.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-2-E 271-272
Maere, I
Kale kucita maere inali njila yovomelezeka kutsatila pogamula nkhani zikuluzikulu. Pocita maere, anali kutenga tinthu ting’onoting’ono monga timiyala kapena timitengo n’kutikulunga m’covala, kutiponya “pamwendo” kapena kutiika m’cikho. Kenaka anali kutipukusa zolimba. Ndiyeno anali kutolapo kanthu kamodzi ndipo mwini wa kanthuko ndiye amene anali kusankhidwa. Pocita maere anthu anali kupemphela monga mmene anali kucitila popanga lumbilo. Pemphelo linali kukhala lacidule kapena anali kuchulilatu zonse zimene afuna, ndipo anali kupempha komanso kuyembekezela kuti Yehova acitepo kanthu. Mawu akuti maere (m’Ciheberi, goh·ralʹ) amagwilitsidwa nchito potanthauza “gawo” kapena “colowa.”—Yos. 15:1; Sal. 16:5; 125:3; Yes. 57:6; Yer. 13:25.
Mmene Anali Kuwagwilitsila Nchito. Miyambo 16:33 imati: “Maere amaponyedwa pacovala, koma zonse zimene maerewo asonyeza zimacokela kwa Yehova.” Mu Isiraeli njila yovomelezeka yogwilitsila nchito maere inali pogamula nkhani zikuluzikulu: “Kucita maere kumathetsa mikangano ndipo kumathetsa nkhani pakati pa anthu amphamvu.” (Miy. 18:18) Sanali kuwagwilitsa nchito pa masewela kapena pochova njuga. Sanali kubechelana ndipo panalibe wopambana kapena woluza. Sanali kucita maere kuti akongoletse kacisi kapena kulemeletsa ansembe, ndipo sanali kuwacita kuti athandize ovutika. Mosiyana ndi zimenezi, asilikali Aciroma anacita izi ndi zolinga zadyela pamene anacita maere pa zovala za Yesu, monga mmene Salimo 22:18 inakambila.—Mat. 27:35.
JUNE 23-29
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 19
Khalani Bwenzi Lenileni kwa Abale Anu
Mmene Tingalimbikitsile Cikondi Cathu pa Ena
Muziika maganizo anu pa zabwino zimene abale na alongo anu amacita, osati pa zolakwa zawo. Ganizilani cocitika ici. Yelekezani kuti muli pa maceza na kagulu ka abale na alongo. Mukusangalala na maceza, ndiyeno kumapeto kwa macezawo, mukujambula cithunzi ca gulu lonse. Mukujambulanso zithunzi zina ziŵili kucitila kuti mwina coyambaco sicinaoneke bwino. Tsopano muli na zithunzi zitatu. Koma mwazindikila kuti pa cimodzi mwa zithunzizo, m’bale wina sanamwetulile. Kodi mungatani na cithunzico? Mungacifafanize cifukwa muli na zithunzi zina ziŵili pamene aliyense pa gulupo akumwetulila kuphatikizapo m’baleyo.
Tingayelekeze zithunzi zimene timasunga na zinthu zimene timakumbukila zokhudza ena. Nthawi zambili timakumbukila zinthu zabwino zimene tinacita pamodzi na abale na alongo. Koma bwanji ngati pa cocika cina m’bale kapena mlongo anakamba kapena kucita cinthu cimene cinakukhumudwitsani? Kodi mungatani na cocitika cimeneco? Kodi simungacifafanize m’maganizo mwanu monga mmene mungafafanizile cithunzi cija? (Miy. 19:11; Aef. 4:32) Tingakwanitse kufafaniza cocitikaco m’maganizo mwathu cifukwa tili na zocitika zambili zabwino zokhudza m’baleyo. Izi ndiye zocitika zimene tiyenela kusunga m’maganizo mwathu na kuzinyadila.
Muzikulabe m’Cikondi Canu
Nafenso timafuna-funa mipata kuti tithandize abale na alongo. (Aheb. 13:16) Ganizilani citsanzo ca mlongo Anna, amene tinam’chula m’nkhani yapita. Pambuyo pa cimphepo camkuntho, iye na mwamuna wake anapita kukaona banja lina la Mboni. Atafika, anapeza kuti mtenje wa nyumba unawonongeka na cimphepoco, ndipo zovala zonse za banjalo zinali zitada. Mlongo Anna anati: “Tinatenga zovalazo kuti tikazicape, ndipo tinazibweza zili zochisa komanso zopeteka bwino. Zimene tinacitazo zinali zocepa, koma zinalimbitsa ubwenzi wathu mpaka pano.” Cifukwa cokonda abale na alongo awo, mlongo Anna na mwamuna wake anapeleka thandizo lofunikila kwa iwo.—1 Yoh. 3:17, 18.
Tikamacita nawo mwacikondi komanso mokoma mtima anthu ena, iwo amaona kuti tikuyesetsa kutengela Yehova. Ndipo angatiyamikile koposa cifukwa cowakomela mtima. Mlongo Khanh amene tam’chula uja, saiŵala anthu amene anam’thandiza. Iye anakamba kuti: “Niwayamikila ngako alongo onse amene anali kupita nane mu ulaliki. Anali kubwela kudzanitenga, kuniitanila ku cakudya, komanso kunibweletsa pa nyumba. Tsopano nazindikila kuti imeneyo inali nchito yaikulu. Anali kucita zimenezo cifukwa conikonda.” N’zoona kuti si onse angatiyamikile pa zimene timawacitila. Ponena za amene anam’thandiza, mlongo Khanh anati: “Nimafuna kuwabwezela pa kukoma mtima kumene ananionetsa, kungoti sinidziŵa kumene amakhala. Koma Yehova adziŵako, ndipo nimam’pempha kuti awabwezele m’malo mwa ine.” Zimenezi n’zoona. Yehova amaona ngakhale zocepa zimene timacitila anthu ena. Iye amaziona kuti ni nsembe zamtengo wapatali, komanso nkhongole imene adzatibwezela.—Ŵelengani Miyambo 19:17.
Pitilizani Kuonetsana Cikondi Cosasintha
Munthu amene waseŵenza pa kampani kwa zaka zambili, timanena kuti ni wanchito wokhulupilika. Zingatheke kuti pa zaka zonse zimene wagwila nchito pa kampaniyo, eni ake a kampani sanaonanepo nawo. Ndipo nthawi zina, iye sangagwilizane na malamulo a kampaniyo, ngakhale kusaikonda kumene. Koma amafunabe kugwila nchitoyo cifukwa amalandila ndalama. Iye angapitilize kugwilabe nchito pa kampaniyo mpaka pokacita lithaya, kupatula ngati angapeze nchito ina yabwino kuposa imene akugwilayo.
Malinga na ndime 6, kusiyana kumene kulipo pakati pa kukhulupilika cabe na cikondi cosasintha, ni colinga cimene munthu angakhale naco pa kukhulupilika kwake. M’nthawi za m’Baibo, n’ciani cinasonkhezela anthu a Mulungu kuonetsa cikondi cosasintha? Anthu amene anaonetsa khalidwe limeneli, anacita zimenezo osati mokakamizika na mkhalidwe uliwonse, koma cifukwa cofunitsitsa kucokela pansi pa mtima. Ganizilani citsanzo ca Davide. Mtima wake unali wofunitsitsa kuonetsa cikondi cosasintha kwa bwenzi lake la pa mtima Yonatani, ngakhale kuti tate wake Yonatani anali kufuna kumupha Davide. Patapita zaka Yonatani atafa, Davide anapitilizabe kuonetsa cikondi cosasintha kwa Mefiboseti mwana wa Yonatani.—1 Sam. 20:9, 14, 15; 2 Sam. 4:4; 8:15; 9:1, 6, 7.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w87-CN 5/15 29
Mfundo Zazikulu Zabaibulo Miyambo 1:1–31:31
Aumphawi ali a Mulungu, ndipo chimene timachita kwa iwo chimawonedwa monga chachitidwa kwa iye. (Miyambo 14:31) Ngati chikondi ndi kuolowa manja kutifulumiza ife kuwonetsa chiyanjo kwa aumphawi kapena kupatsa mphatso kwa osauka, osayembekezera chobwezera chirichonse kuchokera kwa iwo, Yehova amawona kupatsa koteroko monga zomubwereka iye zimene amabwezera ndi chiyanjo ndi madalitso.—Luka 14:12-14.
JUNE 30–JULY 6
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 20
Mmene Mungakhalile pa Cibwenzi Copambana
Mmene Mungakhalile pa Cibwenzi Copambana
Ngakhale kuti kukhala pa cibwenzi n’kosangalatsa, ni sitepe yosafunika kuitenga mopepuka imene ingatsogolele ku ukwati. Pa tsiku la cikwati cawo, okwatilana amalumbila pamaso pa Yehova kuti adzakondana na kulemekezana kwa moyo wawo wonse. Musanacite lumbilo lililonse pa umoyo wanu, ni bwino kuiganizila mofatsa nkhaniyo. (Ŵelengani Miyambo 20:25.) N’cimodzimodzi na malumbilo a ukwati. Cibwenzi cimathandiza anthu aŵiliwo kuti adziŵane bwino na kuwathandiza kupanga cisankho canzelu. Nthawi zina cisankhoco cingakhale kukwatilana kapena kuthetsa cibwenzi. Cibwenzi cikatha, sizitanthauza kuti analakwitsa kucithetsa. M’malo mwake, cibwenzico cinakwanilitsa colinga cake, cimene ni kuwathandiza kupanga cisankho canzelu.
N’cifukwa ciyani m’pofunika kukumbukila colinga cokhalila pa cibwenzi? Ngati anthu amene ni mbeta amakumbukila colinga cokhalila pa cibwenzi, adzapewa kuyamba cibwenzi na munthu amene alibe naye colinga comanga banja. Koma si mbeta zokha zimene zifunikila kukhala na maganizo oyenela pa nkhaniyi. Tonsefe tiyenela kutelo. Mwa citsanzo, ena amaganiza kuti ngati anthu ali pa cibwenzi, ndiye kuti basi ayenela kukakwatilana. Kodi maganizo amenewa amawakhudza bwanji Akhristu amene ni mbeta? Mlongo Melissa wa ku America amene ni mbeta anati, “Mboni zambili zimene zili pa cibwenzi zimakakamizika kungoloŵa m’banja basi. Cifukwa ca maganizo olakwika amenewo, ena amene ali pa cibwenzi amaopa kuthetsa cibwenzico ngakhale pamene zinthu sizikuyenda bwino. Ndipo ena amakhala na nkhawa kwambili, moti amangopewelatu zokhala pa cibwenzi.”
Mmene Mungapezele Womanga Naye Banja
Kodi kuyang’anila munthu capatali kuyenela kucitika motani? Pa misonkhano ya mpingo kapena pa maceza a gulu, mungadziŵeko zinthu zina zokhudza munthuyo monga uzimu wake, umunthu wake, komanso makhalidwe ake. Kodi ali na mabwenzi otani, ndipo amakonda kukamba zinthu zotani? (Luka 6:45) Kodi zolinga zake n’zofanana ni zanu? Mungafunseko akulu a mu mpingo mwawo, kapena Akhristu okhwima amene amam’dziŵa bwino. (Miy. 20:18) Mungawafunse za mbili yake, komanso makhalidwe ake. (Rute 2:11) Pamene mukuyang’anila munthuyo capatali, samalani kuti musamukhumudwitse na kacitidwe kanu. Musungileni ulemu wake, pewani kumulondalonda, kapena kuloŵelela m’nkhani za munthu mwini.
Mmene Mungakhalile pa Cibwenzi Copambana
Kodi mungam’dziŵe bwanji munthu wamkati wa mnzanuyo? Njila yabwino koposa ni kukambilana momasuka komanso moona mtima, kufunsana mafunso na kumvetsela mwachelu. (Miy. 20:5; Yak. 1:19) Kuti mucite zimenezi, sankhani kucita zinthu zimene zingakupatseni mwayi wocezako. Mungacite zinthu monga kudyela pamodzi, kupita kokayenda, komanso kukalalikila. Mungadziŵanenso bwino mwa kuceza pamodzi na mabwenzi anu, komanso acibale. Kuwonjezela apo, muzicitanso zimene zingakuthandizeni kuona mmene mnzanuyo amacitila zinthu na anthu ena, komanso m’mikhalidwe yosiyana-siyana. Onani zimene m’bale Aschwin wa ku Netherlands anali kucita. Ponena za nthawi imene anali pa cibwenzi na Alicia, iye anati: “Tinali kusankha zinthu zimene zinatithandiza kudziŵana bwino. Nthawi zambili zinthuzo zinali kukhala zosavuta monga kuphikila pamodzi, kapena kugwila nchito zina za pakhomo. Pa zocitika zimenezi m’pamene tinali kuona zimene aliyense wa ife amacita bwino, komanso zofooka zathu.”
Mungadziŵanenso bwino mukamacitila pamodzi zinthu zauzimu. Mukaloŵa m’banja, muzipatula nthawi yocita kulambila kwa pabanja kuti Mulungu akhale mbali yofunika kwambili m’banja lanu. (Mlal. 4:12) Conco, bwanji osapanga makonzedwe oyamba kucitila pamodzi zinthu zauzimu pamene muli pa cibwenzi? N’zoona kuti anthu amene ali pa cibwenzi sali pabanja, ndipo m’bale sanakhalebe mutu wa mlongoyo. Ngakhale n’telo, kucitila zinthu zauzimu pamodzi, kudzakuthandizani kudziŵa uzimu wa aliyense wa inu. Max na Laysa, okwatilana a ku America anapeza phindu locita zimenezi. Max anati: “Kuciyambi kwa cibwenzi cathu, tinayamba kuŵelengela pamodzi zofalitsa zimene zikamba pa cibwenzi, ukwati, komanso umoyo wa m’banja. Zofalitsa zimenezi zinatsegula mipata yokambilana nkhani zambili zofunika zimene zingakhale zovuta kuyamba kuzikambilana.”
Kufufuza Cuma Cauzimu
g-CN 5/11 19 ¶1-2
Kodi Milomo Yanu Ndi “Ziwiya Zamtengo Wapatali”?
Mfumu Solomo inalemba kuti: “Pali golide komanso miyala yamtengo wapatali ya korali yambirimbiri, koma milomo yodziwa zinthu ndiyo ziwiya zamtengo wapatali.” (Miyambo 20:15) Golide wakhala akuonedwa kuti ndi chinthu cha mtengo wapatali kuyambira kalekale, ndipo m’nthawi ya Solomo miyala ya korali inkaonedwanso kuti ndi yamtengo wapatali. Koma milomo yathu ikhoza kukhala yamtengo wapatali kuposa zinthu zimenezi. Motani? Osati chifukwa chakuti ndi yooneka bwino, koma chifukwa cha zimene timalankhula.
Milomo yamtengo wapatali imanena zinthu zabwino mwachikondi ndiponso mwachifundo. “Milomo yodziwa zinthu” imanena za choonadi chokhudza Mulungu chopezeka m’Baibulo. Buku lakale limeneli ndi nkhokwe ya nzeru ndi choonadi chokhudza Mlengi wathu komanso lili ndi malangizo abwino kwambiri omwe angatithandize pa moyo wathu.—Yohane 17:17.