Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
© 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
NOVEMBER 3-9
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU NYIMBO YA SOLOMO 1-2
Nkhani Yokhudza Cikondi Ceniceni
Kodi N’zotheka Kukhala m’Cikondi Ceniceni?
9 Okwatilana amene amatumikila Yehova, samaona cikwati kukhala mgwilizano wamba. Iwo amakondana kwambili ndipo amasonyezana cikondi. Koma ndi cikondi cotani cimene ayenela kusonyezana? Kodi ciyenela kukhala cikondi copanda dyela cimene Baibulo limatiphunzitsa kusonyeza anthu onse? (1 Yoh. 4:8) Kodi ndi cikondi cimene anthu a m’banja limodzi amasonyezana? Kodi ndi cikondi ca pakati pa mabwenzi apamtima? (Yoh. 11:3) Kapena kodi ndi cikondi ca pakati pa mwamuna ndi mkazi? (Miy. 5:15-20) Kunena zoona, okwatilana ayenela kusonyezana cikondi ca mitundu yonseyi. Iwo ayenela kupeza nthawi yotsimikizilana kuti amakondana mwa mau ndi zocita zao. Kucita zimenezi kudzathandiza kuti azisangalala mu cikwati cao. M’zikhalidwe zina, makolo ndi amene amasankhila mwana wao munthu wokwatilana naye, ndipo okwatilanawo samadziŵana mpaka pa tsiku la cikwati. Zikakhala conco, okwatilanawo ayenela kuzindikila kuti afunika kuuzana mau acikondi cifukwa zimenezi zidzathandiza kuti cikondi cao cilimbe, ndipo cikwati cao cidzakhala copambana.
10 Okwatilana amalimbitsanso cikwati cao mwa njila ina akamauzana mau acikondi. Mfumu Solomo analonjeza Msulami kuti adzam’pangila ‘zokongoletsa zoti azivala kumutu. Zokongoletsazo zokhala zozungulila, zagolide, zokhala ndi mikanda yasiliva.’ Solomo anatama mtsikanayo kuti ndi “wokongola ngati mwezi wathunthu, wosadetsedwa ngati dzuwa lowala.” (Nyimbo 1:9-11; 6:10) Koma mtsikanayo anakhalabe wokhulupilika kwa m’busa wake wokondedwa. N’ciani cinam’thandiza kukhalabe wokhulupilika kwa m’busayo panthawi imene anali kukhala motalikilana? (Ŵelengani Nyimbo ya Solomo 1:2, 3.) Cimene cinam’thandiza ndi kukumbukila cikondi cimene wokondedwa wake anali kumuonetsa kuti “cimaposa vinyo kukoma kwake,” ndipo dzina lake linali “ngati mafuta othila pamutu.” (Sal. 23:5; 104:15) Inde, n’zofunika kuti okwatilana azisonyezana cikondi kaŵilikaŵili cifukwa zimenezo zimathandiza cikondi cao kukula. Kukumbukila mmene amasonyezelana cikondi kumathandiza cikwati cao kukhala colimba!
Kufufuza Cuma Cauzimu
Kodi N’zotheka Kukhala m’Cikondi Ceniceni?
11 Ngati mukufuna wokwatilana naye, n’ciani cimene mungaphunzile kucokela kwa Msulami? Iye sanali kukonda Mfumu Solomo, ndipo anauza atsikana amene anali kukhala m’Nyumba Yacifumu ya Solomo kuti: “Musayese kudzutsa cikondi mwa ine mpaka pamene cikondico cifunile.” (Nyimbo 2:7; 3:5) N’cifukwa ciani anatelo? Cifukwa cakuti munthu sayenela kukhala m’cikondi ndi wina aliyense amene angamfikile. Mkristu amene afuna kuloŵa m’banja ayenela kuleza mtima kuti apeze munthu amene adzam’konda ndi mtima wonse.
NOVEMBER 10-16
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU NYIMBO YA SOLOMO 3-5
Kukongola kwa Umunthu Wamkati N’kofunika Kwambili
Kodi N’zotheka Kukhala m’Cikondi Ceniceni?
8 M’busayo ndi mtsikana wake, anayamikilanso zinthu zina kuonjezela pa maonekedwe ao. Mwacitsanzo, mbusayo anali kukonda mmene mtsikanayo anali kukambila ndi anthu ena. (Ŵelengani Nyimbo ya Solomo 4:7, 11.) Mbusayo anauza mtsikanayo kuti: “Milomo yako imangokhalila kukha uchi wapacisa.” N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti uci wapacisa umanzuna, ndipo umanunkhila kuposa uci umene wapitidwa mphepo. “Uci ndi mkaka zili kuseli kwa lilime [la mtsikanayo],” kutanthauza kuti mau ake ndi abwino ndiponso okoma ngati uci ndi mkaka. Mwacionekele, pamene mbusayo anauza mtsikanayo kuti “ndiwe wokongola paliponse, . . . ndipo mwa iwe mulibe cilema ciliconse,” sanali kutanthauza maonekedwe akunja cabe.
w00-CN 11/1 11 ¶17
Lingaliro Laumulungu la Khalidwe Loyera
17 Munthu wachitatu yemwe anasunga kukhulupirika ndiye namwali wa ku Sulami. Pokhala wachitsikana ndi wokongola, si mnyamata wobusa ziweto yekha amene anakopeka naye komanso mfumu ya Israyeli yolemerayo, Solomo. Nkhani yonse yosangalatsayo ya m’Nyimbo ya Solomo, ikusimba kuti Msulamiyo anakhalabe wodzisunga, zimene zinapangitsa kuti ena am’lemekeze. Ngakhale kuti Solomo anakanidwa ndi mtsikanayu, iye anauziridwa kulemba nkhani yake. Mbusa yemwe mtsikanayu anakonda anali kulemekezanso khalidwe la mtsikanayu lodzisunga. Panthaŵi ina mnyamatayo atasinkhasinkha anati Msulamiyo anali ngati “munda wotsekedwa.” (Nyimbo ya Solomo 4:12) M’Israyeli wakale, minda yokongola inkakhala ndi ndiwo zosiyanasiyana zamasamba, maluŵa onunkhira bwino, ndi mitengo yochititsa chidwi. Minda yoteroyo nthaŵi zambiri inkakhala yotchingidwa ndi mpanda wa mitengo yomera kapena ndi khoma ndipo panali khomo limodzi lokha lolowera lomwenso ankalikhoma. (Yesaya 5:5) Kwa mbusayo, kuyera kwa khalidwe la Msulami ndi kusangalatsa kwake zinali ngati munda wokongola kwambiri woterewu. Anali wodzisunga kotheratu. Chikondi chake anali kudzachisonyeza kwa mwamuna wake wam’tsogoloyo basi.
g04-CN 12/22 9 ¶2-5
Kukongola Kofunika Kwambiri
Kodi kukongola kwa mumtima kungakope ena? Georgina, amene wakhala pabanja kwa zaka pafupifupi khumi, anati: “Zaka zonsezi, ndakhala ndikukopeka ndi mwamuna wanga chifukwa cha kuona mtima kwake akamachita nane zinthu. Chinthu chofunika kwambiri pamoyo wake ndi kusangalatsa Mulungu. Zimenezi zamuchititsa kukhala munthu woganizira ena ndiponso wachikondi. Asanachite chinthu amayamba wandifunsa kaye maganizo anga ndipo amandichititsa kumva kuti amayamikira zimene ndimachita. Ndikudziwa kuti amandikondadi.”
Daniel, amene anakwatira mu 1987, anati: “Ndimaona kuti mkazi wanga ndi wokongola. Sikuti ndimangokopeka ndi maonekedwe ake okha, koma khalidwe lake limandichititsa kumukonda kwambiri. Nthawi zonse amaganizira anthu ena ndipo amayesetsa kuwachitira zinthu zabwino. Ali ndi makhalidwe abwino kwambiri achikristu. Zimenezi zachititsa kuti ndizisangalala kukhala naye.”
M’dziko lino limene anthu amangoona zakunja zokha, tiyenera kuona mtima wa munthu. Tiyenera kuzindikira kuti kukhala ndi thupi labwino kwambiri n’kovuta, mwinanso kosatheka kumene, ndipo kuli ndi phindu lochepa kwambiri. Komabe, n’zotheka kukhala ndi makhalidwe abwino amene amachititsa munthu kukhala wokongola mumtima. Baibulo limati: “Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.” Mosiyana ndi zimenezo, Malemba amachenjeza kuti: “Monga chipini chagolidi m’mphuno ya nkhumba, momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.”—Miyambo 11:22; 31:30.
Mawu a Mulungu amatithandiza kuyamikira “munthu wobisika wamtima, m’chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.” (1 Petro 3:4) Zoonadi, kukongola kwa mumtima kumeneko n’kofunika kwambiri kuposa kukongola kwa thupi. Ndipo aliyense akhoza kukhala nako.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06-CN 11/15 18 ¶4
Mfundo Zazikulu za Nyimbo ya Solomo
2:7; 3:5—N’chifukwa chiyani mtsikanayo akulumbirira akazi akumpanda wa mfumu pogwiritsa ntchito “mphoyo, ndi nswala ya kuthengo”? Mphoyo ndi nswala zili ndi maonekedwe ake ochititsa kaso ndiponso okongola kwambiri. Kwenikweni, Msulamiyu, akulumbirira akazi akumpanda wa mfumu kuti chilichonse chimene chili chochititsa kaso ndiponso chokongola chisautse chikondi mwa iye.
NOVEMBER 17-23
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU NYIMBO YA SOLOMO 6-8
Khalani Khoma, Osati Citseko
15 Ŵelengani Nyimbo ya Solomo 4:12. N’cifukwa ciani m’busa anakamba kuti wokondedwa wake anali “ngati munda wochingidwa ndi mpanda”? Munda wochingidwa sumakhala woonekela kwa anthu onse. Msulami anali ngati mundawo cifukwa anali kukonda cabe m’busa. Ngakhale kuti mfumu inali kumukopa, iye sanafune kusintha maganizo ake. Msulami anali kufuna kukwatiwa ndi m’busayo basi. Msulamiyo anali monga “khoma” osati monga “citseko” cimene cimatseguka mosavuta. (Nyimbo 8:8-10) Mofananamo, Akristu amene ali pa cisumbali ayenela kukhala okhulupilika kwa wina ndi mnzake. Iwo sayenela kukhala m’cikondi ndi munthu wina kusiyapo cisumbali cao.
16 Pamene m’busa anauza Msulami kuti apite limodzi kokayenda, azilongosi ake anamuletsa. M’malo mwake, io anam’patsa nchito yolondela minda yampesa yao. Kodi sanali kum’khulupilila? Kodi anali kuganiza kuti Msulami anali kufuna kucita ciwelewele ndi m’busayo? Iyai. Azilongosi ake anali kum’teteza kuti asagwe m’ciyeso ndi kucita chimo. (Nyimbo 1:6; 2:10-15) Ngati muli pa cisumbali, n’ciani cimene muyenela kupewa kuti musacite ciwelewele? Muyenela kudziŵa pasadakhale zinthu zimene muyenela kupewa kuti cisumbali canu cikhalebe coyela. Muyenelanso kupewa kukhala aŵiliŵili pa malo obisika. Mungasonyezane cikondi, koma mwa njila yoyenela
yp-E 188 ¶2
Nanga Bwanji pa Nkhani ya Kugonana Musanalowe M’banja?
Kukhala woyela kumathandiza kwambili wacinyamata kupewa mavuto amene amabwela cifukwa cocita ciwelewele. Baibo imanena za mtsikana wina amene anakhalabe woyela ngakhale kuti anali kukondana kwambili ndi cibwenzi cake. Cifukwa ca zimenezi, iye anakamba modzitamandila kuti: “Ine ndine khoma, ndipo mabele anga ali ngati nsanja.” Pankhani yopewa ciwelewele, iye sanali ngati citseko cimene cimangotseguka mosavuta. Khalidwe lake labwino analiyelekezela ndi nkhoma lolimba la nsanja yaitali imene palibe amene angaikwela! Conco anali woyenela kuchedwa “woyela,” ndipo ponena za mwamuna amene anali kufuna kum’kwatila, m’pomveka kuti iye anati: “Mʼmaso mwa wokondedwa wanga ndakhala ngati mkazi amene wapeza mtendele.” Iye anali ndi mtendele wa mumtima. Mtendelewo unathandiza kuti iye ndi wokondedwa wake akhale osangalala.—Nyimbo ya Solomo 6:9, 10; 8:9, 10.
yp2-CN 33
Chitsanzo Chabwino—Msulami
Mtsikana wachisulami ankadziwa kuti sayenera kungotengeka maganizo pankhani ya chikondi. Iye anauza anzake kuti: ‘Ndikulumbirirani, . . . musautse, musagalamutse chikondi, chisanafune mwini.’ Msulamiyu anadziwa kuti munthu angalephere kuganiza bwino chifukwa chongotengeka maganizo. Mwachitsanzo, anazindikira kuti anthu ena akanatha kumulimbikitsa kukhala pachibwenzi ndi munthu amene sakuyenerana naye. Anazindikiranso kuti mtima wake ungamuchititsenso kusaganiza mwanzeru. Choncho Msulamiyu anapitiriza kukhala ngati “khoma.”—Nyimbo ya Solomo 8:4, 10.
Kodi ndinu wokhwima maganizo moti mumaona nkhani ya chikondi ngati mmene Msulami anali kuionera? Kodi mumayamba mwaganiza kaye musanachite zinthu kapena mumangotsatira zimene mtima wanu wafuna? (Miyambo 2:10, 11) Nthawi zina ena angakulimbikitseni kukhala pachibwenzi inuyo musanafike poti n’kuchita zimenezo. Zochita zanunso zingakulowetseni m’vuto limeneli. Mwachitsanzo, mukaona mnyamata ndi mtsikana akuyenda atagwirana manja, kodi nanunso mumalakalaka mutachita zimenezo? Kodi mungafune munthu amene si wachipembedzo chanu? Pankhani zachikondi, mtsikana wachisulami anali wokhwima maganizo. Inunso mungakhale wotero!
Kufufuza Cuma Cauzimu
Kodi N’zotheka Kukhala m’Cikondi Ceniceni?
3 Ŵelengani Nyimbo ya Solomo 8:6. Pa lembali, cikondi cikufotokozedwa kuti ndi “lawi la Ya.” N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti cikondi ndi khalidwe lalikulu la Yehova, ndipo anatilenga m’njila yakuti tizitha kutengela cikondi cake. (Gen. 1:26, 27) Pambuyo poti Yehova walenga munthu woyamba, Adamu, Iye anam’patsa mkazi wokongola. Pamene Adamu anaona Hava kwa nthawi yoyamba, iye anasangalala kwambili cakuti sanabise mmene anali kumvelela pamene ananena ndakatulo yake. Hava nayenso anakonda kwambili mwamuna wake. Ndipo mpake kuti anatelo cifukwa Yehova analenga Hava kucoka kwa Adamu. (Gen. 2:21-23) Popeza kuti Yehova analenga anthu m’njila yakuti azisonyeza cikondi, n’zotheka kuti mwamuna ndi mkazi azisonyezana cikondi ceniceni
NOVEMBER 24-30
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 1-2
Ciyembekezo kwa Anthu “Olemedwa ndi Zolakwa”
ip-1-CN 14 ¶8
Atate ndi Ana Ake Opanduka
8 Yesaya akupitiriza uthenga wake mwa kuuza mtundu wa Yuda mawu amphamvu akuti: “Mtundu wochimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbewu yakuchita zoipa, ana amene achita mowononga, iwo amusiya Yehova, iwo amunyoza Woyera wa Israyeli, iwo adana naye nabwerera m’mbuyo.” (Yesaya 1:4) Zochita zoipa zingaunjikane kufika pokhala ngati chikatundu chopsinja. M’masiku a Abrahamu Yehova anafotokoza machimo a Sodomu ndi Gomora kuti anali “kulemera.” (Genesis 18:20) Chinthu chofanana ndi zimenezo tsopano chikuoneka mwa anthu a Yuda, pakuti Yesaya akuti iwo ali “olemedwa ndi mphulupulu.” Ndiponso, iye akuwatcha kuti “mbewu yakuchita zoipa, ana amene achita mowononga.” Inde, Ayuda ali ngati ana opulupudza. Iwo ‘abwerera m’mbuyo,’ kapena malinga n’kunena kwa Baibulo la New Revised Standard Version, iwo “alekeratu kuyanjana” ndi Atate awo.
ip-1-CN 28-29 ¶15-17
“Tiyeni Tikonze Zinthu”
15 Mawu a Yehova tsopano akumveka mwachikondi ndi mwachifundo kwambiri. “‘Bwerani, tsono, anthu inu, tiyeni tikonze zinthu pakati pathu,’ ati Yehova. ‘Ngakhale machimo a anthu inu akhale ofiira, adzakhala oyera ngati matalala; ngakhale akhale ofiira ngati kapezi, adzakhala ngati ubweya wa nkhosa.’” (Yesaya 1:18, NW) Kaŵirikaŵiri anthu amamva molakwa chiitano chimene chili koyambirira kwa vesili. Mwachitsanzo, Baibulo lachicheŵa lotchedwa Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu limati, “tiweruzane”—ngati kuti aliyense afunika kuvomereza zolakwa zake kuti agwirizane. Si choncho ayi! Yehova sali wolakwa m’pang’ono pomwe m’zochita zake ndi anthu ameneŵa opanduka ndi achinyengo. (Deuteronomo 32:4, 5) Vesili silikunena za kukambirana kwakuti wina anena mbali yake winanso mbali yake kwa anthu ofanana, koma kwa pabwalo la milandu pofuna kupeza chilungamo. Zili ngati kuti panopo Yehova akutengera Aisrayeli kukhoti.
16 Zimenezi zingakhale zovutitsa maganizo, koma Yehova ndi Woweruza wachifundo kwambiri zedi. Sitingayerekeze ndi wina aliyense mmene iye amakhululukira ena. (Salmo 86:5) Iye yekha ndi amene angatenge machimo a Israyeli amene ali “ofiira” n’kuwayeretsa, kuwapanga kukhala “oyera ngati matalala.” Kuthimbirira kwa uchimo sikungachotsedwe ndi zoyesayesa za anthu, kachitidwe kenakake ka zinthu, nsembe, kapena mapemphero. Machimo angatsukidwe kokha mwa kukhululukiridwa ndi Yehova. Mulungu amakhululukira moteromo pamlingo wa zimene amanena, zimene zimaphatikizapo kulapa koona kochokera pansi pa mtima.
17 Choonadi chimenechi chili chofunika kwambiri kwakuti Yehova akuchibwereza ngati kuti akunena ndakatulo—machimo a “ofiira” adzakhala ngati ubweya woyera watsopano wosasinthidwa mtundu. Yehova amafuna kuti ife tizidziŵa kuti iye alidi Wokhululukira machimo, ngakhale machimo akulu kwambiri, malinga ngati aona kuti ife tili olapadi zenizeni. Awo amene sakhulupirira kuti zimenezi zili choncho kwa iwowo angachite bwino kulingalira za zitsanzo za anthu ena monga Manase. Iye analakwa kwambiri—kwa zaka zochuluka. Komatu, iye analapa ndipo anamukhululukira. (2 Mbiri 33:9-16) Yehova akufuna tonsefe, kuphatikizapo awo amene achita machimo aakulu kwambiri, kuti tidziŵe kuti sitinachedwe ‘kukonza zinthu’ ndi iye.
Kufufuza Cuma Cauzimu
ip-1-CN 39 ¶9
Nyumba ya Yehova Ikwezedwa Pamwamba
9 Zoonadi, anthu a Mulungu lerolino sasonkhana pa phiri lenileni limene lili ndi kachisi wa miyala. Kachisi wa Yehova ku Yerusalemu anawonongedwa ndi asilikali achiroma mu 70 C.E. Komanso, mtumwi Paulo ananena momveka bwino kuti kachisi wa ku Yerusalemu ndiponso chihema chimene chinalipo kachisiyo asanamangidwe zinali zophiphiritsa. Zinaimira mkhalidwe wauzimu weniweni ndi wokulirapo, “chihema choona, chimene Ambuye anachimanga, si munthu ayi.” (Ahebri 8:2) Chihema chauzimu chimenecho chili makonzedwe ofikira Yehova polambira ozikidwa pa nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. (Ahebri 9:2-10, 23) Mogwirizana ndi zimenezi, “phiri la nyumba ya Yehova” lotchulidwa pa Yesaya 2:2 limaimira kulambira kokwezeka koyera kwa Yehova m’masiku athu. Awo amene amayamba kulambira koyera sasonkhana kumalo ena ake apadera; amasonkhana mu umodzi wa kulambira.
DECEMBER 1-7
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 3-5
Panali Poyenela Yehova Kuyembekezela kuti Anthu ake Azimumvela
ip-1-CN 73-74 ¶3-5
Tsoka Munda Wamphesa Wosakhulupirika!
3 Kaya Yesaya akuwaimbiradi fanizo limeneli omvetsera ake kapena ayi, koma ndithudi likuwakopa chidwi. Ambiri anazoloŵera kulima minda yamphesa, ndipo kulongosola kwa Yesaya n’komveka bwino komanso n’zimene zingachitikedi. Mofanana ndi anthu amene amalima mphesa masiku ano, mwini wake wa munda wamphesawo wabzala, osati njere za mphesa, koma “mpesa wosankhika,” kapena kuti wambambande—mtengo wampesa wodulidwa kapena nsonga ya mpesa wina. Moyenerera, walima munda wamphesa umenewu “m’chitunda cha zipatso zambiri,” malo amene mphesa zingabale bwino.
4 Pamakhala ntchito yaikulu kuti munda wamphesa ubale zipatso. Yesaya akulongosola kuti mwiniyo ‘anakumba mcherenje kuzungulira kwete natolatola miyala’—ntchito yoŵaŵa komanso yotopetsa! Ayenera kuti miyala ikuluikulu ‘anamangira nsanja.’ M’nthaŵi zakale pansanja zoterozo ndipo panali kukhala alonda amene anali kudikirira akuba ndi nyama. Ndiponso, wamanga linga la miyala m’malire mwa munda wamphesawo. (Yesaya 5:5) Kaŵirikaŵiri anali kuchita zimenezi pofuna kuti nthaka isakokoloke.
5 Pokhala kuti anagwira ntchito zolimba kuti ateteze munda wake wamphesawo, mwiniyo moyenerera akuyembekezera kuti udzabereka bwino. Poyembekezera zimenezi, akusema moponderamo mphesa. Koma kodi akolola zinthu zimene akuyembekezerazo? Ayi, munda wamphesawo ukubereka mphesa zosadya.
ip-1-CN 76 ¶8-9
Tsoka Munda Wamphesa Wosakhulupirika!
8 Yesaya akutchula Yehova, mwini wake wa munda wamphesawo, kuti “wokondedwa wanga.” (Yesaya 5:1) Yesaya atha kulankhula za Mulungu mwachikondi moteromo kokha chifukwa chakuti ali ndi unansi wolimba ndi Mulunguyo. Komabe, chikondi cha mneneriyu pa Mulungu ndi chochepa poyerekeza ndi chikondi chimene Mulungu wasonyeza pa “munda [wake] wamphesa”—mtundu umene ‘anauwoka.’—Yerekezani ndi Eksodo 15:17; Salmo 80:8, 9.
9 Yehova “anawoka” mtundu wake m’dziko la Kanani naupatsa malamulo ndi malangizo ake, amene anali ngati khoma lowateteza kuti asaipitsidwe ndi mitundu ina. (Eksodo 19:5, 6; Salmo 147:19, 20; Aefeso 2:14) Ndiponso, Yehova anawapatsa oweruza, ansembe, ndi aneneri kuti aziwalangiza. (2 Mafumu 17:13; Malaki 2:7; Machitidwe 13:20) Pamene Israyeli anali kuopsezedwa ndi magulu ankhondo, Yehova anali kupereka anthu oti awapulumutse. (Ahebri 11:32, 33) Pachifukwa chomveka, Yehova akufunsa kuti: “Ndikanachitanso chiyani ndi munda wanga wamphesa, chimene sindinachite mmenemo?”
w06-CN 6/15 18 ¶1
Samalirani “Mpesa Uwu”!
Yesaya anayerekezera “banja la Israyeli” ndi munda wa mphesa umene pang’ono ndi pang’ono unabereka “mphesa zosadya,” kapena kuti, mphesa zowola. (Yesaya 5:2, 7) Mphesa zosadya zimakhala zazing’ono poyerekezera ndi mphesa zakudya ndipo zimakhala ndi mnofu wochepa kwambiri, popeza nthanga zake zimadzaza pafupifupi mphesa yonseyo. Mphesa zosadya sangapangire vinyo kapena kuzidya. Ichi n’chizindikiro chabwino cha mtundu wopandukawo, umene chipatso chake chinali kuphwanya malamulo m’malo mwa kuchita chilungamo. Kubereka chipatso chopanda ntchitoku silinali vuto la Mlimi wa mpesawo. Yehova anachita zonse zomwe akanatha kuti apangitse mtunduwo kukhala wobala zipatso. Iye anafunsa kuti: “Ndikanachitanso chiyani ndi munda wanga wamphesa, chimene sindinachite mmenemo”?—Yesaya 5:4.
w06-CN 6/15 18 ¶2
Samalirani “Mpesa Uwu”!
Popeza mpesa wa Israyeli unakhala wosabereka, Yehova anawachenjeza kuti adzagwetsa mpanda umene anamanga mozungulira anthu ake kuti uwateteze. Sadzaduliranso mpesa wake wophiphiritsira kapena kulimira dothi lake. Mvula ya m’nyengo ya masika yomwe zipatsozo zinkadalira sidzabwera, ndipo minga ndi udzu zidzamera m’munda wa mphesawo.—Yesaya 5:5, 6.
Kufufuza Cuma Cauzimu
ip-1-CN 80 ¶18-19
Tsoka Munda Wamphesa Wosakhulupirika!
18 Mu Israyeli wakale dziko lonse kwenikweni linali la Yehova. Banja lililonse linali ndi choloŵa chopatsidwa ndi Mulungu, chimene anali kutha kubwereka wina kapena kumupatsa pa ngongole koma osati kugulitsa “chigulitsire.” (Levitiko 25:23) Lamulo limeneli linali kuteteza kugwiritsa ntchito molakwa zinthu, monga ngati kuphangira malo. Linalinso kuteteza mabanja kuti asasauke kwambiri. Komabe, anthu ena mu Yuda anali kuswa mwadyera malamulo a Mulungu onena za malo. Mika analemba kuti: “Akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi choloŵa chake.” (Mika 2:2) Koma Miyambo 20:21 imachenjeza kuti: “Choloŵa chingalandiridwe msangamsanga poyamba pake; koma chitsiriziro chake sichidzadala.”
19 Yehova akulonjeza kuti anthu adyera ameneŵa adzawalanda zinthu zimene anapeza m’njira zolakwika. Nyumba zimene akulanda ena zidzakhala “zopanda wokhalamo.” Minda imene akuisirira idzabereka pang’ono kwambiri kusiyana ndi mmene ikuberekera. Sizikutchulidwa kuti temberero limeneli lidzachitika motani kwenikweni ngakhalenso nthaŵi yake yeniyeni imene lidzakwaniritsidwa. Pang’ono chabe, mwina likunena za mikhalidwe imene idzakhalapo pamene adzakhala akapolo ku Babulo.—Yesaya 27:10.
DECEMBER 8-14
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 6-8
“Ine Ndilipo! Nditumizeni”
ip-1-CN 93-94 ¶13-14
Yehova Mulungu Ali M’kachisi Wake Wopatulika
13 Tiyeni timvetsere zimene Yesaya akumva. “Ndinamva mawu a Ambuye akuti, Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife? Ndipo ine ndinati, Ndine pano; munditumize ine.” (Yesaya 6:8) Funso limene Yehova akufunsa mwachionekere lalinganizidwa kuti Yesaya ayankhe, popeza kuti palibe mneneri winanso waumunthu m’masomphenyawo. Popanda kukayika Yesaya akuitanidwa kuti akhale mthenga wa Yehova. Koma kodi ndi chifukwa chiyani Yehova akufunsa kuti, “Ndani adzatimukira ife?” Mwa kusintha kanenedweko kuchoka pa kunena za munthu m’modzi kuti “ndidzatumiza” n’kunena za anthu ambiri kuti “adzatimukira,” tsopano Yehova akuphatikizapo munthu winanso m’modzi pa iye mwini. Ndaniyo? Kodi ameneyu sanali Mwana wake wobadwa yekha, amene kenako anadzakhala munthu wotchedwa Yesu Kristu? Indedi, anali Mwana mmodzimodziyu amene Mulungu anamuuza kuti, “tipange munthu m’chifanizo chathu.” (Genesis 1:26; Miyambo 8:30, 31) Inde, Mwana wake wobadwa yekha ali pambali pake Yehova m’mabwalo akumwamba.—Yohane 1:14.
14 Yesaya sakuchedwa kuyankha! Mosasamala kanthu kuti uthengawo ndi wotani, iye mofulumira akuyankha kuti: “Ndine pano; munditumize ine.” Iye sakufunsa chimene adzapindulapo ngati atavomera ntchitoyo. Mzimu wake wofunitsitsa uli chitsanzo chabwino kwambiri kwa atumiki onse a Mulungu lerolino, amene apatsidwa ntchito yolalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi.’ (Mateyu 24:14) Mofanana ndi Yesaya, mokhulupirika amagwirabe ntchito yawoyo ndipo amakwanitsa kuchita ‘umboni kwa anthu a mitundu yonse,’ mosasamala kanthu kuti anthu ambiri salabadira. Ndipo mwachidaliro amapitirizabe kugwira ntchitoyi, monga mmene Yesaya anachitira, podziŵa kuti ntchito yawoyo inalamulidwa ndi munthu wamkulu kwambiri.
ip-1-CN 95 ¶15-16
Yehova Mulungu Ali M’kachisi Wake Wopatulika
15 Tsopano Yehova akulongosola zimene Yesaya adzanene ndiponso mmene anthu adzalabadirire: “Kauze anthu aŵa, Imvani inu ndithu [“mobwerezabwereza,” NW], koma osazindikira; yang’anani inu ndithu [“mobwerezabwereza,” NW], koma osadziŵitsa. Nenepetsa mtima wa anthu aŵa, lemeretsa makutu awo, nutseke maso awo; angaone ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angazindikire ndi mtima wawo, nakabwerenso, nachiritsidwe.” (Yesaya 6:9, 10) Kodi izi zikutanthauza kuti Yesaya azilankhula mosazindikira bwino ndi mopanda luso akumatsutsa Ayuda, kuwapangitsa kuti asamvane ndi Yehova? Ayi ndithu! Aŵa ndi anthu a mtundu wake Yesaya amene akuwaona kuti ndi abale ake. Koma mawu a Yehova akusonyeza mmene anthu adzachitira ndi uthenga wake, mosasamala kanthu za mmene Yesaya akagwirira ntchito yake mokhulupirika.
16 Anthu ndiwo ali ndi vuto. Yesaya adzalankhula “mobwerezabwereza,” koma uthengawo sadzaulandira ngakhalenso kuumvetsa. Ochuluka adzakhala ouma khosi ndi osalabadira, ngati kuti ndi akhungu ndi ogontha kotheratu. Mwa kuwayendera mobwerezabwereza, Yesaya adzalola “anthu aŵa” kuti asonyeze kuti safuna kumvetsetsa. Adzaonetsa kuti safuna kuti uthenga wa Yesaya—uthenga wa Mulungu—umene adzauzidwa uloŵe m’maganizo mwawo ndi m’mitima yawo. Anthu a m’masiku ano akuchitanso mofananamo! Ambiri amakana kumvetsera Mboni za Yehova pamene zikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umene ukubwerawo.
ip-1-CN 99 ¶23
Yehova Mulungu Ali M’kachisi Wake Wopatulika
23 Pogwira mawu a Yesaya, Yesu anasonyeza kuti ulosiwo unalinso ndi kukwaniritsidwa m’masiku ake. Anthuwo monga gulu anali ndi mtima wonga wa Ayuda a m’masiku a Yesaya. Iwo anadzipangitsa kukhala akhungu ndi ogontha ku uthenga wake ndipo moteronso anawonongedwa. (Mateyu 23:35-38; 24:1,2) Zimenezi zinachitika pamene ankhondo a Aroma motsogoleredwa ndi Kazembe Tito anaukira Yerusalemu mu 70 C.E. ndi kuphwasula mzindawo ndi kachisi wake. Komabe, ena anamvetsera Yesu ndipo anakhala ophunzira ake. Yesu anawatcha kuti “odala.” (Mateyu 13:16-23, 51) Anawauza kuti pamene adzaona “Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo,” iwo ‘akathaŵire kumapiri.’ (Luka 21:20-22) Motero “mbewu yopatulika” imene inasonyeza chikhulupiriro ndi imene inapangidwa kukhala mtundu wauzimu, “Israyeli wa Mulungu,” inapulumuka.—Agalatiya 6:16.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06-CN 12/1 9 ¶4
Mfundo Zazikulu za M’buku la Yesaya—Gawo 1
7:3, 4—N’chifukwa chiyani Yehova anapulumutsa Ahazi mfumu yoipa? Mafumu a Aramu ndi Isiraeli anakonza zochotsa Mfumu Ahazi ya Yuda pampando wachifumu n’kuikapo wolamulira woti azingowamvera iwowo. Wolamulira wake anali mwana wamwamuna wa Tabeeli, yemwe sanali mbadwa ya Davide. Nzeru zochokera kwa Satana zimenezi zikanasokoneza pangano la Ufumu la pakati pa Yehova ndi Davide. Yehova anapulumutsa Ahazi n’cholinga choteteza mzere umene “Kalonga wa mtendere” adzabadwiremo.—Yesaya 9:6.
DECEMBER 15-21
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 9-10
Ulosi Wonena za “Kuwala Kwakukulu”
ip-1-CN 125-126 ¶16-17
Lonjezo la Kalonga wa Mtendere
16 Inde, “nthaŵi ina m’tsogolo” imene Yesaya analosera ndi nthaŵi ya utumiki wapadziko lapansi wa Kristu. Yesu ali padziko lapansi anakhalitsa kwambiri ku Galileya. Munali m’dera la Galileya mmene anayambira utumiki wake ndi kuyamba kulengeza kuti: “Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” (Mateyu 4:17) Ku Galileya, anapereka Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri, anasankha atumwi ake, anachita chozizwitsa chake choyamba, ndipo ataukitsidwa anaonekera kwa otsatira ake pafupifupi 500. (Mateyu 5:1–7:27; 28:16-20; Marko 3:13, 14; Yohane 2:8-11; 1 Akorinto 15:6) Mwa njirayi Yesu anakwaniritsa ulosi wa Yesaya mwa kuchitira ulemu “dziko la Zebuloni, ndi dziko la Naftali.” Zoona, Yesu sanangochita utumiki wake kwa anthu a ku Galileya okha. Mwa kulalikira uthenga wabwino m’dziko lonselo, Yesu ‘anachitira ulemu’ mtundu wonse wa Israyeli, kuphatikizapo Yuda.
17 Nanga bwanji za “kuwala kwakukulu” mu Galileya kumene Mateyu akutchula? Mawu ameneŵanso anawatenga mu ulosi wa Yesaya. Yesaya analemba kuti: “Anthu amene anayenda mumdima, aona kuŵala kwakukulu; iwo amene anakhala m’dziko la mthunzi wa imfa, kuŵala kwatulukira kwa iwo.” (Yesaya 9:2) Pofika zaka za zana loyamba C.E., kuŵala kwa choonadi kunali kutabisika ndi mabodza achikunja. Atsogoleri achipembedzo achiyuda anawonjezera vutolo mwa kumamatira ku miyambo yawo yachipembedzo imene ‘anapeputsa [nayo] mawu a Mulungu.’ (Mateyu 15:6) Anthu odzichepetsa anali kuponderezedwa ndi kusokonezedwa maganizo, anali kutsatira “atsogoleri akhungu.” (Mateyu 23:2-4,16) Pamene Yesu Mesiyayo anaoneka, maso a anthu ambiri odzichepetsa anatsegulidwa modabwitsa zedi. (Yohane 1:9,12) Ntchito ya Yesu pamene anali padziko lapansi ndiponso madalitso obwera chifukwa cha nsembe yake analongosoledwa bwino mu ulosi wa Yesaya kuti ndi “kuŵala kwakukulu.”—Yohane 8:12.
ip-1-CN 126-128 ¶18-19
Lonjezo la Kalonga wa Mtendere
18 Amene analabadira kuwalako anali ndi chifukwa chokwanira chokhalira okondwa. Yesaya anapitiriza kuti: “Inu mwachulukitsa mtundu, inu mwaonjezera kukondwa kwawo; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m’masika, monga anthu akondwa pogaŵana zofunkha.” (Yesaya 9:3) Chifukwa cha kulalikira kwa Yesu ndi otsatira ake, anthu oona mtima anaoneka, anadzionetsa kuti anali kukhumba kulambira Yehova mu mzimu ndi m’choonadi. (Yohane 4:24) Pa zaka zosakwana zinayi, anthu ambiri zedi anakhala Akristu. Anthu 3,000 anabatizidwa pa tsiku la Pentekoste mu 33 C.E. Patapita nthaŵi yochepa, “chiŵerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu.” (Machitidwe 2:41; 4:4) Pamene ophunzirawo anali kusonyeza kuwalako mwachangu, “chiŵerengero cha akuphunzira chidachulukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.”—Machitidwe 6:7.
19 Mofanana ndi amene amakondwera ndi zotuta zochuluka kapena amene amasangalala pogaŵana zofunkha zamtengo wapatali atapambana nkhondo, otsatira a Yesu anakondwera kuti anali kuwonjezeka. (Machitidwe 2:46,47) M’kupita kwa nthaŵi, Yehova anapangitsa kuŵalako kuŵalira amitundu. (Machitidwe 14:27) Motero anthu a mafuko onse anakondwera kuti njira yofikira kwa Yehova inatsegulidwa kwa iwo.—Machitidwe 13:48.
ip-1-CN 128-129 ¶20-21
Lonjezo la Kalonga wa Mtendere
20 Zotsatira za ntchito ya Mesiya sizidzatha, monga momwe tikuonera m’mawu otsatira a Yesaya akuti: “Goli la katundu wake, mkunkhu wa paphewa pake, ndodo ya womusautsa, inu mwazithyola monga tsiku la Midyani.” (Yesaya 9:4) Zaka mazana angapo Yesaya asanabadwe, Amidyani limodzi ndi Amoabu anakonza chiwembu kuti achimwitse Israyeli. (Numeri 25:1-9, 14-18; 31:15, 16) Kenako, Amidyani anakhaulitsa Aisrayeli mwa kukantha ndi kufunkha midzi yawo ndi minda yawo kwa zaka zisanu ndi ziŵiri. (Oweruza 6:1-6) Komano Yehova, kupyolera mwa mtumiki wake Gideoni, anakantha gulu lankhondo la Midyani. Kuchokera pa “tsiku la Midyani” limenelo, palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti anthu a Yehova anavutitsidwanso ndi Amidyani. (Oweruza 6:7-16; 8:28) Posachedwa m’tsogolo, Yesu Kristu, Gideoni wamkulu, adzakantha adani amakono a anthu a Yehova. (Chivumbulutso 17:14; 19:11-21) Ndiyeno, “monga tsiku la Midyani,” padzakhala chipambano chotheratu ndi chokhalitsa, osati mwa maluso aumunthu, koma mwa mphamvu ya Yehova. (Oweruza 7:2-22) Anthu a Mulungu sadzavutikanso m’goli lopondereza!
21 Kusonyeza mphamvu yaumulungu si kutamanda nkhondo. Yesu woukitsidwayo ali Kalonga wa Mtendere, ndipo mwa kufafaniziratu adani ake, adzabweretsa mtendere wosatha. Tsopano Yesaya akunena za zida zankhondo kuti zikuwonongedwa kotheratu ndi moto: “Zida zonse za mwamuna wovala zida za nkhondo m’phokosomo, ndi zovala zovimvinika m’mwazi, zidakhala zonyeka ngati nkhuni.” (Yesaya 9:5) Phokoso la mgugu wa nsapato za asilikali oguba silidzamvekanso. Mayunifolomu amagazi a asilikali okonda nkhondo sadzaonekanso. Sikudzakhalanso nkhondo!—Salmo 46:9.
Kufufuza Cuma Cauzimu
ip-1-CN 130 ¶23-24
Lonjezo la Kalonga wa Mtendere
23 Phungu ndi munthu amene amapereka uphungu, kapena malangizo. Pamene anali padziko lapansi Yesu Kristu anapereka uphungu wodabwitsa. M’Baibulo timaŵerenga kuti “makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake.” (Mateyu 7:28) Iye ndi Phungu wanzeru ndi wachifundo, amene amamvetsetsa chibadwa cha anthu mwapadera kwambiri. Uphungu wake sukhala kudzudzula kapena kupereka chilango kokhakokha. Kaŵirikaŵiri, umakhala kuphunzitsa ndi kulangiza mwachikondi. Uphungu wa Yesu ndi wodabwitsa chifukwa nthaŵi zonse uli wanzeru, wangwiro, ndi wosalakwika. Pamene watsatiridwa, umapezetsa moyo wosatha.—Yohane 6:68.
24 Uphungu wa Yesu suli wotero chabe chifukwa chakuti amaganiza kwambiri. M’malo mwake, iye akuti: “Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine.” (Yohane 7:16) Monga mmene zinalili ndi Solomo, Yehova Mulungu ndiye Gwero la nzeru za Yesu. (1 Mafumu 3:7-14; Mateyu 12:42) Chitsanzo cha Yesu chiyenera kusonkhezera aphunzitsi ndi aphungu mu mpingo wachikristu kuti nthaŵi zonse zophunzitsa zawo zizichokera m’Mawu a Mulungu.—Miyambo 21:30.
DECEMBER 22-28
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 11-13
Kodi Maulosi Ananenelatu Zotani Zokhudza Mesiya?
ip-1-CN 159 ¶4-5
Chipulumutso ndi Kusangalala mu Ulamuliro wa Mesiya
4 Zaka mazana ambiri Yesaya asanabadwe, olemba Baibulo achihebri ena anatchula za kubwera kwa Mesiya, Mtsogoleri woona, amene Yehova adzatumiza ku Israyeli. (Genesis 49:10; Deuteronomo 18:18; Salmo 118:22, 26) Tsopano kupyolera mwa Yesaya, Yehova akuwonjeza mbali zina. Yesaya akulemba kuti: “Padzatuluka mphukira pa tsinde la Jese, ndi nthambi yotuluka m’mizu yake idzabala zipatso.” (Yesaya 11:1; yerekezani ndi Salmo 132:11.) Mawu akuti “mphukira” komanso akuti “nthambi” akusonyeza kuti Mesiya adzakhala mbadwa ya Jese kupyolera mwa mwana wake Davide, amene anadzozedwa ndi mafuta kukhala mfumu ya Israyeli. (1 Samueli 16:13; Yeremiya 23:5; Chivumbulutso 22:16) Pamene Mesiya woona wafika, “nthambi” imeneyi, ya m’nyumba ya Davide, idzabala chipatso chabwino.
5 Mesiya wolonjezedwayo ndi Yesu. Wolemba uthenga wabwino Mateyu ananena za mawu a pa Yesaya 11:1 pamene anati kunali kukwaniritsa mawu a aneneri kutchula Yesu kuti ‘Mnazara.’ Chifukwa chakuti anakulira m’tauni ya Nazarete, Yesu anatchedwa kuti Mnazara, dzina limene likuoneka kuti n’lofanana ndi liwu lachihebri logwiritsidwa ntchito pa Yesaya 11:1 kuti “nthambi.”—Mateyu 2:23, NW, mawu am’munsi; Luka 2:39,40.
ip-1-CN 159 ¶6
Chipulumutso ndi Kusangalala mu Ulamuliro wa Mesiya
6 Kodi Mesiya adzakhala wolamulira wotani? Kodi adzakhala ngati Asuri wankhanza, amene akuwononga ufumu wakumpoto wa mafuko khumi wa Israyeli? Ndithudi ayi. Ponena za Mesiya, Yesaya akuti: “Mzimu wa Yehova udzamubalira [“uyenera kukhala pa,” NW] iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziŵa ndi wakuopa Yehova; ndipo adzakondwera nako kumuopa Yehova.” (Yesaya 11:2, 3a) Mesiyayo akudzozedwa, osati ndi mafuta, koma ndi mzimu woyera wa Mulungu. Izi zikuchitika pa ubatizo wa Yesu, pamene Yohane Mbatizi akuona mzimu woyera wa Mulungu ukutsikira pa Yesu mooneka ngati nkhunda. (Luka 3:22) Mzimu wa Yehova ‘ukukhala pa’ Yesu, ndipo akupereka umboni wa zimenezi pamene akuchita zinthu mwanzeru, mozindikira, mwauphungu, mwamphamvu, ndi mwachidziŵitso. Mikhalidwe yabwinotu kwambiri ya mtsogoleri!
ip-1-CN 160 ¶8
Chipulumutso ndi Kusangalala mu Ulamuliro wa Mesiya
8 Kodi kuopa Yehova kumene Mesiya akusonyeza n’chiyani? Ndithudi Yesu sakuchita mantha oopa mkwiyo wa Mulungu, kuopa chiweruzo chake ayi. M’malo mwake, Mesiya amaopa Mulungu mwa kum’patsa ulemu, ali ndi mantha achikondi pa iye. Munthu amene amaopa Mulungu amalakalaka kuti nthaŵi zonse ‘azichita zimene zimamukondweretsa Iye,’ monga amachitira Yesu. (Yohane 8:29) Mwa mawu komanso chitsanzo chake, Yesu amaphunzitsa kuti palibe amene angakhale n’chimwemwe chachikulu kuposa amene tsiku lililonse akuyenda mu kuopa koyenerera kwa Yehova.
ip-1-CN 160 ¶9
Chipulumutso ndi Kusangalala mu Ulamuliro wa Mesiya
9 Yesaya akulosera mikhalidwe inanso ya Mesiya kuti: “Sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera.” (Yesaya 11:3b) Ngati munali kuweruzidwa m’khothi, kodi simungayamikire kukhala ndi woweruza wonga ameneyu? Pa udindo wake monga Woweruza wa anthu onse, Mesiya satengeka ndi mfundo zabodza, luso la kalankhulidwe kamachenjera pamilandu, mphekesera, kapena zinthu zimene munthu ali nazo, monga chuma. Amazindikira chinyengo ndipo amayang’ana kupyola pa maonekedwe akunja oshashalika, nazindikira “munthu wobisika wamtima,” “munthu wosaoneka.” (1 Petro 3:4, NW, mawu am’munsi) Chitsanzo chapamwamba cha Yesu chimenechi n’choyenera kuti onse amene afunika kuweruza milandu mumpingo wachikristu azichitsatira.—1 Akorinto 6:1-4.
ip-1-CN 161 ¶11
Chipulumutso ndi Kusangalala mu Ulamuliro wa Mesiya
11 Pamene otsatira ake akufunika kuwawongolera, Yesu amatero m’njira imene imawapindulitsa kwambiri—chitsanzo chabwino kwambiri kwa akulu achikristu. Komabe, amene amachita zoipa angayembekezere chiweruzo choŵaŵa kwambiri. Pamene Mulungu adzafuna kuti dongosolo la zinthu lino liyankhe pa zochita zake, Mesiya “adzamenya dziko” ndi mawu ake aulamuliro, kupereka chiweruzo cha chiwonongeko kwa onse oipa. (Salmo 2:9; yerekezani ndi Chivumbulutso 19:15.) Pomaliza pake, sipadzakhala anthu oipa osokoneza mtendere wa anthu. (Salmo 37:10, 11) Yesu, m’chiuno ndi m’impso zake atamangamo chilungamo ndi kukhulupirika, ali ndi mphamvu yochita zimenezi.—Salmo 45:3-7.
Kufufuza Cuma Cauzimu
ip-1-CN 165-166 ¶16-18
Chipulumutso ndi Kusangalala mu Ulamuliro wa Mesiya
16 Kulambira koyera kunayamba kuukiridwa mu Edene pamene Satana anapambana posonkhezera Adamu ndi Hava kuti asamvere Yehova. Kufikira lerolino, Satana sanasiye cholinga chake cha kupatutsa kwa Mulungu anthu ochuluka monga mmene angathere. Koma Yehova sadzalola kuti kulambira koyera kuthe padziko lapansi. Dzina lake likuphatikizidwapo, ndipo amasamalira amene amamutumikira. Motero kupyolera mwa Yesaya akupereka lonjezo lochititsa chidwi ili: “Padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Jese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.” (Yesaya 11:10) M’mbuyomo mu 537 B.C.E., Yerusalemu, mzinda umene Davide anaupanga kukhala likulu la dzikolo, unali ngati mbendera, unaitana Ayuda otsalira okhulupirika amene anali atamwazikana kuti abwere ndi kudzamanga kachisi.
17 Komabe, ulosiwu ukusonya zoposa pamenepo. Monga taonera kale, ukunena za ulamuliro wa Mesiya, Mtsogoleri yekha woona wa anthu a mitundu yonse. Mtumwi Paulo anagwira mawu Yesaya 11:10 posonyeza kuti m’masiku ake anthu a mitundu anali ndi malo mu mpingo wachikristu. Pogwira mawu matembenuzidwe a mu Septuagint a vesili, iye analemba kuti: “Yesaya ati, Padzali muzu wa Jese, ndi iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.” (Aroma 15:12) Ndiponso, ulosiwu ukufika patali—ukufika m’masiku athu ano pamene anthu amitundu akusonyeza chikondi kwa Yehova mwa kuchirikiza abale ake odzozedwa a Mesiya.—Yesaya 61:5-9; Mateyu 25:31-40.
18 M’kukwaniritsidwa kwamakono, “tsiku lomwelo” lotchulidwa ndi Yesaya linayamba pamene Mesiya anaikidwa pa mpando wachifumu monga Mfumu ya Ufumu wa kumwamba wa Mulungu mu 1914. (Luka 21:10; 2 Timoteo 3:1-5; Chivumbulutso 12:10) Kuchokera nthaŵiyo, Yesu Kristu wakhala mbendera yooneka bwino, malo osonkhanako anthu, kwa Israyeli wauzimu ndi kwa anthu amitundu amene amakhumba kukhala ndi boma lachilungamo. Motsogoleredwa ndi Mesiya, uthenga wabwino wa Ufumu waperekedwa ku mitundu yonse, monga momwe Yesu analoserera. (Mateyu 24:14; Marko 13:10) Uthenga wabwino umenewu umakhudza anthu mwamphamvu. “Khamu lalikulu, loti palibe munthu [akhoza] kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse” likugonjera kwa Mesiya mwa kugwirizana ndi otsalira odzozedwa m’kulambira koyera. (Chivumbulutso 7:9) Pamene atsopano ambiri akupitiriza kuyanjana ndi otsalira mu “nyumba yopemphereramo” yauzimu ya Yehova, amawonjezera ulemerero wa “popuma” pa Mesiya, kachisi wauzimu waukulu wa Mulungu.—Yesaya 56:7; Hagai 2:7.
DECEMBER 29–JANUARY 4
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 14-16
Adani a Anthu a Mulungu Adzalangidwa
ip-1-CN 180 ¶16
Yehova Anyazitsa Mzinda Wodzikuza
16 Izi sizinachitike panthaŵi yomweyo mu 539 B.C.E. Komabe, lerolino n’zodziŵika kwambiri kuti chilichonse chimene Yesaya analosera ponena za Babulo chakwaniritsidwa. Babulo “tsopano ndi malo ophwasulidwa aakulu, komanso ali mabwinja okhaokha, ndipo wakhala choncho kwa zaka mazana ambiri,” anatero munthu wina wothirira ndemanga pa Baibulo. Ndiyeno anatinso: “N’kosatheka kuona malo ameneŵa n’kusakumbukira mmene maulosi a Yesaya ndi Yeremiya akwaniritsidwira ndendende.” Mwachionekere, m’masiku a Yesaya palibe munthu amene akanalosera kugwa kwa Babulo ndi kudzafafanizidwa kwake. Ndiponsotu, Babulo anagwa kwa Amedi ndi Aperisi pafupifupi zaka 200 Yesaya atalemba buku lake! Ndipo kufafanizidwa kwake kunachitika zaka mazana angapo pambuyo pa zimenezi. Kodi zimenezi sizikulimbitsa chikhulupiriro chathu mu Baibulo monga Mawu ouziridwa a Mulungu? (2 Timoteo 3:16) Ndiponso, popeza kuti Yehova anakwaniritsa maulosi m’nthaŵi za m’mbuyomu, tingakhale ndi chidaliro chonse kuti maulosi a Baibulo amene sanakwaniritsidwebe adzakwaniritsidwa m’nthaŵi yoikika ya Mulungu.
ip-1-CN 184 ¶24
Yehova Anyazitsa Mzinda Wodzikuza
24 M’Baibulo mafumu a banja lachifumu la Davide amafanizidwa ndi nyenyezi. (Numeri 24:17) Kuyambira ndi Davide, “nyenyezi” zimenezo zinali kulamulira zili pa Phiri la Ziyoni. Solomo atamanga kachisi mu Yerusalemu, dzina lakuti Ziyoni linali kugwiritsidwa ntchito pa mzinda wonsewo. Mu pangano la Chilamulo, amuna onse achiisrayeli anali kulamulidwa kupita ku Ziyoni katatu pachaka. Motero linakhala “phiri losonkhanako.” Mwa kutsimikiza mtima kukagonjetsa mafumu achiyuda ndiyeno n’kuwachotsa pa phiri limenelo, Nebukadinezara akulengeza cholinga chake cha kukhala pamwamba pa “nyenyezi” zimenezo. Sakuthokoza Yehova kuti ndiye wamutheketsa kuwagonjetsa. M’malo mwake, iye kwenikweni modzikuza akudziika pamalo a Yehova.
ip-1-CN 189 ¶1
Uphungu wa Yehova Wotsutsa Amitundu
YEHOVA angagwiritse ntchito amitundu kulanga anthu ake chifukwa cha kuipa kwawo. Ngakhale n’choncho, mitunduyo saikhululukira chifukwa cha nkhanza zawo, kunyada kwawo, ndi kudana kwawo ndi kulambira koona. Motero kudakali nthaŵi yaitali kuti zichitike, akuuzira Yesaya kulemba za “katundu wa Babulo.” (Yesaya 13:1) Komabe, Babulo adzaopsa m’tsogolo. M’masiku a Yesaya, Asuri ndiye akupondereza anthu apangano a Mulungu. Asuri wawononga ufumu wakumpoto wa Israyeli ndi kusakaza Yuda kwambiri. Koma chipambano cha Asuri n’chochepa. Yesaya akulemba kuti: “Yehova wa makamu walumbira, nati, Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa . . . kuti Ine ndidzathyola Asuri m’dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo goli lidzachoka pa iwo, ndi katundu wake adzachoka paphuzi pawo.” (Yesaya 14:24, 25) Mosakhalitsa Yesaya atanena ulosi umenewu, kuopsa kwa Asuri mu Yuda kukuthetsedwa.
ip-1-CN 194 ¶12
Uphungu wa Yehova Wotsutsa Amitundu
12 12 Kodi ulosiwu udzakwaniritsidwa liti? Posachedwapa. “Aŵa ndi mawu amene Yehova adanena za Moabu nthaŵi zapitazo. Koma tsopano Yehova wanena, nati, Zisanapite zaka zitatu monga zaka za wolembedwa ntchito, ulemerero wa Moabu udzakhala wonyozeka, ndi khamu lalikulu lake, ndi otsala adzakhala ang’onong’ono ndi achabe.” (Yesaya 16:13,14) Mogwirizana ndi zimenezi, pali umboni wa ofukula za m’mabwinja kuti mu zaka za zana la chisanu ndi chitatu B.C.E., Moabu anavutika kwambiri ndipo m’midzi yake yambiri munatsala anthu ochepa. Tigilati Pilesere 3 anatchula Salamanu wa ku Moabu kuti anali m’modzi wa olamulira amene anali kumupatsa msonkho. Sanakeribu analandira msonkho kuchokera kwa Kamusunabi, mfumu ya Moabu. Mafumu a Asuri Esarihadoni ndi Ashabanipalu anati anali kulamulira Mfumu Musuri ndi Mfumu Kamashalitu, mafumu a Moabu. Zaka mazana angapo zapitazo, Amoabu sanakhalekonso monga mtundu wa anthu. Mabwinja a midzi yomwe ikulingaliridwa kuti inali ya Amoabu apezeka, koma kufikira lerolino pafukulidwa chabe umboni wochepa wa mdani wa Israyeli ameneyu amene panthaŵi ina anali wamphamvu.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w06-CN 12/1 10 ¶11
Mfundo Zazikulu za M’buku la Yesaya—Gawo 1
14:1, 2—Kodi zinachitika motani kuti anthu a Yehova atengere m’ndende amitundu omwe poyamba anawatengera m’ndende iwowo ndiponso kuti ‘alamulire owavuta’? Zimenezi zinachitika kwa anthu ngati Danieli, amene anali ndi udindo waukulu ku Babulo pansi pa ulamuliro wa Amedi ndi Aperisi; Estere, amene anakhala mfumukazi ya Aperisi; Moredekai amene anakhala nduna yaikulu mu ufumu wa Aperisi.