Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Umoyo ndi Utumiki
SEPTEMBER 1-7
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU Miyambo 29
Pewani Miyambo ndi Zikhulupililo Zosagwilizana ndi Malemba
wp16.06 6, bokosi
Masomphenya Oonetsa Amene Ali Kumwamba
Mofanana ndi akaidi, anthu mamiliyoni ambili amakhala mwamantha cifukwa cokhulupilila zamatsenga na kuopa mizimu yoipa. Kuti iwo adziteteze, amadalila mankhwala ocita kuvala, zithumwa, na zinthu zina zamatsenga. Koma inu simufunika kucita zimenezo cifukwa Baibo imati: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Conco, Mulungu woona Yehova, amene ni wamphamvu kuposa Satana, adzakutetezani ngati mum’khulupilila.
Kuti Yehova akutetezeni, muyenela kudziŵa zimene zimam’kondweletsa ndi kuzicita. Mwacitsanzo, ca m’ma 100 C.E., Akhiristu a mu mzinda wa Efeso anashoka mabuku awo onse a zamatsenga. (Machitidwe 19:19, 20) Mofananamo, kuti Mulungu akutetezeni, muyenela kuwononga zonse zokhudzana na ziŵanda monga zithumwa, mabuku a zamatsenga, na mankhwala otsilikila.
Cilikizani Coonadi pa Nkhani ya Akufa
13 Ngati simuli wotsimikiza ngati mwambo winawake ni wogwilizana na Malemba kapena ayi, pemphelani kwa Yehova. M’pempheni kuti akupatseni nzelu. (Ŵelengani Yakobo 1:5.) Kenako, citani zinthu mogwilizana na pemphelo lanu mwa kufufuza malangizo m’zofalitsa zathu. Mwinanso mungafunsile kwa akulu mumpingo. Iwo sadzakuuzani zocita, koma adzakufotokozelani mfundo za m’Baibo zogwilizana na nkhaniyo, monga zimene zafotokozedwa m’nkhani ino. Ngati mucita zimenezi, mudzaphunzitsa “mphamvu [zanu] za kuzindikila,” zimene zidzakuthandizani “kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.”—Aheb. 5:14.
“Ndidzayenda M’coonadi Canu”
12 Miyambo na zikondwelelo zosagwilizana na Malemba. Acibululu, anzathu a ku nchito, ndiponso anzathu a ku sukulu, angayese kutikopa kuti ticiteko zikondwelelo zosemphana na Malemba. Tingacite ciani kuti tisagonje ngati anthu akutituntha kuti ticite nawo miyambo na zikondwelelo zosalemekeza Yehova? Tizikumbukila nthawi zonse mmene Yehova amaonela miyambo na zikondwelelo zimenezo. Kuŵelenganso nkhani za m’mabuku athu, zofotokoza mmene zikondwelelo zofala zinayambila n’kothandiza. Ngati tikumbukila zifukwa za m’Malemba zimene siticitila nawo zikondwelelo zimenezo, timakhala okhutila kuti tikuyenda m’njila ‘yovomelezeka kwa Ambuye.” (Aef. 5:10) Kukhulupilila Yehova na Mawu ake a coonadi kudzatiteteza ku msampha ‘woopa anthu.’—Miy. 29:25.
Kufufuza Cuma Cauzimu
“Tizisonyezana Cikondi Ceni-ceni m’Zocita Zathu”
Muziyamikila abale mocokela pansi pa mtima. Tiyenela kufuna-funa mipata yoyamikila ena cifukwa kucita zimenezi ‘kumalimbikitsa.’ (Aef. 4:29) Komabe, ciyamikilo cathu ciyenela kukhala cocokela pansi pa mtima. Apo ayi, ndiye kuti tikumugwila m’maso munthu kapena tikuopa kumupatsa uphungu. (Miy. 29:5) Kuyamikila munthu koma tikakhala kuseli n’kumamunena, ni cinyengo. Mtumwi Paulo anapewa khalidwe limeneli, ndipo anapeleka citsanzo cabwino pankhani yoonetsa cikondi ceni-ceni poyamikila ena. Mwacitsanzo, anayamikila Akhristu a ku Korinto moona mtima pa zimene anali kucita bwino. (1 Akor. 11:2) Koma akaona kuti pena pake sanacite bwino, anali kuwauza mokoma mtima ndi momveka bwino cifukwa cake anafunika kuwongolela.—1 Akor. 11:20-22.
SEPTEMBER 8-14
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU Miyambo 30
“Musandipatse Umphawi Kapena Cuma”
N’cikondi Cotani Cimene Cimabweletsa Cimwemwe Ceni-ceni?
10 Tonse timafunikila ndalama. Zimatitetezela pa zinthu zina. (Mlal. 7:12) Koma kodi munthu angakhaledi wacimwemwe ngati ali cabe na ndalama zocepa zomuthandiza kugula zinthu zofunikila mu umoyo? Inde! (Ŵelengani Mlaliki 5:12.) Aguri mwana wa Yake analemba kuti: “Musandipatse umphawi kapena cuma. Ndidye cakudya cimene ndikufunika kudya.” N’zosavuta kudziŵa cifukwa cake sanafune kukhala wosauka kwambili. Iye anafotokoza kuti sanafune kuti akabe, cifukwa kuba kukananyozetsa Mulungu. Nanga n’cifukwa ciani anapempha Mulungu kuti asam’patse cuma? Iye anafotokoza kuti: “Kuti ndisakhute kwambili n’kukukanani kuti: ‘Kodi Yehova ndani?’” (Miy. 30:8, 9) Mwacionekele, mudziŵako anthu ena amene amadalila cuma cawo m’malo mokhulupilila Mulungu.
11 Anthu okonda ndalama sangakondweletse Mulungu. Yesu anati: “Kapolo sangatumikile ambuye awili, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupilika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikila Mulungu ndi Cuma nthawi imodzi.” Asanakambe izi, iye anati: “Lekani kudziunjikila cuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbili zimawononga, ndiponso pamene mbala zimathyola ndi kuba. Koma unjikani cuma canu kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbili sizingawononge, ndiponso kumene mbala sizingathyole n’kuba.”—Mat. 6:19, 20, 24.
12 Ambili aona kuti kukhala na umoyo wosalila zambili kumawathandiza kukhala acimwemwe, komanso kumawapatsa nthawi yokwanila yotumikila Yehova. Mwacitsanzo, Jack, amene amakhala ku United States, anagulitsa nyumba yake yaikulu na bizinesi n’colinga cakuti akhale na nthawi yocita upainiya pamodzi na mkazi wake. Iye anati: “Cinali covuta kusiya nyumba yathu yokongola na malo athu m’dela labwino. Koma, kwa zaka zambili, n’nali kubwela ku nyumba nili osasangalala cifukwa ca mavuto a ku nchito. Mkazi wanga, amene ni mpainiya, nthawi zonse anali kukhala wosangalala. Anali kukonda kukamba kuti: ‘Ine nimaseŵenzela bwana wabwino ngako!’ Koma popeza tonse lomba ndise apainiya, timaseŵenzela Bwana mmodzi, Yehova.”
w87-CN 5/15 30 ¶8
Opani Yehova ndipo Mudzakhala Achimwemwe
◆ 30:15, 16—Kodi ndi iti yomwe iri nsonga ya zitsanzo zimenezi?
Zimachitira chitsanzo kusakwaniritsidwa kwa umbombo. Misundu imazikwaniritsa yokha ndi mwazi, monga mmenedi munthu wa umbombo nthawi zonse amafuna ndalama kapena mphamvu. Mofananamo, Manda sakwaniritsidwa, koma amakhala otseguka kulandira mikhole yambiri ya imfa. Mimba yosabala ‘imalirira’ ana (Genesis 30:1) Dziko louma limamwa madzi a mvula ndipo mwamsanga limawonekanso louma. Ndipo moto womwe watha zinthu zimene zaponyedwa pa iwo, umadzutsa malawi amene amayatsanso zina zomwe zingagwire moto mwamsanga zimene ziri pafupi. Ndi mmene ziriri ndi munthu waumbombo. Koma awo otsogozedwa ndi nzeru ya umulungu sakalipitsidwa kosathandi umbombo wotero.
w11-CN 6/1 10 ¶4
Kodi Mungatani Kuti Muzigula Zinthu Mogwirizana Ndi Ndalama Zimene Mumapeza?
Muzisunga ndalama pang’onopang’ono musanagule kanthu. Ngakhale kuti zimaoneka ngati zachikale, ndi bwino kumasunga kaye ndalama musanagule chinthu. Imeneyi ndi njira ina yabwino kwambiri imene ingakuthandizeni kupewa kugwera m’mavuto azachuma. Kuchita zimenezi kumathandiza anthu ambiri kupewa kukhala ndi ngongole. Kumathandizanso kuti musamagule zinthu pa mtengo wokwera chifukwa nthawi zambiri mukagula chinthu pangongole, mumachigula modula. Baibulo limanena kuti nyerere “n’zanzeru” chifukwa “zimasonkhanitsa chakudya chawo m’chilimwe” kuti zidzachigwiritse ntchito m’tsogolo.—Miyambo 6:6-8; 30:24, 25.
Khalani Mlendo m’Tenti ya Yehova Kwamuyaya!
18 Tingacite bwino kudzisanthula kuti tidziŵe mmene timaonela ndalama. Dzifunseni kuti: ‘Kodi nthawi zambili nimaganizila za ndalama komanso zimene ningagule na ndalamazo? Nikakongola ndalama, kodi nimacedwa kuibweza poganiza kuti mwiniwake sakuifuna? Kodi kukhala na ndalama kumanipangitsa kudziona wofunika ngako kuposa ena? Kodi ndine wowolowa manja na ndalama zanga? Kodi nimaweluza abale na alongo anga kuti amakonda zakuthupi cabe cifukwa cakuti ali na ndalama? Kodi nimapanga ubwenzi na anthu olemela na kupewa anthu osauka?’ Tili na mwayi wapadela wokhala alendo a Yehova. Kuti tikhalebe mabwenzi a Mulungu, tiyenela kupewa mzimu wokonda ndalama. Ndipo tikatelo, Yehova sadzatisiya!—Ŵelengani Aheberi 13:5.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w09-CN 4/15 17 ¶11-13
Chilengedwe Chimasonyeza Nzeru Za Yehova
11 Mbira ndi mtundu wina wa zolengedwa zazing’ono zimene zingatiphunzitse mfundo zofunika kwambiri. (Werengani Miyambo 30:26.) Nyamayi imaoneka ngati kalulu ndipo ili ndi makutu aafupi koma ozungulira, komanso miyendo yake ndi yaifupi. Nyama yaing’ono imeneyi imakhala m’matanthwe. Iyo ili ndi maso akuthwa kwambiri ndipo amaithandiza kuona msanga adani. Komanso m’matanthwe amene imakhala muli maenje ndi mphako zimene zimaiteteza kwa adani. Mwachibadwa, mbira zimakula bwino chifukwa chokhala pagulu, ndipo zimenezi zimapereka chitetezo komanso zimathandiza nyamazi kukhala zofunda m’nyengo yozizira.
12 Kodi tikuphunzira chiyani kwa mbira? Choyamba, onani kuti nyamayi imasamala kuti isagwidwe. Imagwiritsa ntchito maso ake akuthwa kuonera msanga adani ngakhale ali kutali, ndipo imakhala pafupi ndi dzenje kapena mphako, zimene zingathandize kupulumutsa moyo wake. Ifenso tiyenera kukhala ndi maso auzimu akuthwa kuti tizitha kuona zinthu zobisika zangozi zimene zili m’dziko la Satanali. Mtumwi Petulo analangiza Akhristu kuti: “Sungani maganizo anu, khalani maso. Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti wina umudye.” (1 Pet. 5:8) Yesu ali padziko lapansi, anakhalabe maso, inde watcheru, pamene Satana ankayesetsa kufuna kuswa umphumphu Wake. (Mat. 4:1-11) Yesu anasonyeza chitsanzo chabwino kwa otsatira ake.
13 Njira imodzi imene tingakhalire maso ndiyo kuyesetsa kugwiritsa ntchito chitetezo chauzimu chimene Yehova wapereka kwa ife. Sitiyenera kunyalanyaza kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kupezeka pamisonkhano yachikhristu. (Luka 4:4; Aheb. 10:24, 25) Ndiponso mofanana ndi mbira zimene zimakula bwino chifukwa chokhala pagulu, tifunikira kukhala pafupi kwambiri ndi Akhristu anzathu kuti ‘tizilimbikitsana.’ (Aroma 1:12) Tikamagwiritsa ntchito chitetezo chimene Yehova wapereka, timasonyeza kuti tikugwirizana ndi zimene wamasalmo Davide analemba kuti: “Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye.”—Sal. 18:2.
SEPTEMBER 15-21
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU Miyambo 31
Zimene Tingaphunzilepo pa Malangizo Acikondi a Mayi
w11-CN 2/1 19 ¶7-8
Muziphunzitsa Ana Anu Makhalidwe Abwino
Aphunzitseni zinthu zonse zokhudza kugonana. Ndi bwinodi kuti makolo azichenjeza ana awo nkhani zokhudza kugonana. (1 Akorinto 6:18; Yakobo 1:14, 15) Komabe Baibulo limanena kuti kugonana ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, osati msampha wa Satana. (Miyambo 5:18, 19; Nyimbo ya Solomo 1:2) Choncho kuuza ana anu achinyamata zoipa zokhazokha zokhudza kugonana kungachititse kuti aziganiza molakwa za nkhaniyi komanso mosagwirizana ndi Malemba. Mtsikana wina wa ku France dzina lake Corrina ananena kuti: “Makolo anga akafuna kunena nkhani zokhudza kugonana, ankangonena za kuipa kwa chiwerewere ndipo zimenezi zinandichititsa kuganiza kuti kugonana ndi koipa nthawi zonse.”
Onetsetsani kuti mwauza ana anu mbali zonse zokhudza kugonana. Mayi wina wa ku Mexico, dzina lake Nadia, ananena kuti: “Pokambirana ndi ana anga nkhani zokhudza kugonana, nthawi zonse ndimawauza kuti kugonana ndi kwabwino chifukwa ndi mmene tinalengedwera. Yehova Mulungu anakonza zoti anthu azigonana ndiponso azisangalala. Koma ndimawauzanso kuti anthu okwatirana okha ndi amene ayenera kugonana. Ndimawauza kuti munthu angasangalale ngati akutsatira dongosolo la Yehova pa nkhaniyi kapena akhoza kupeza mavuto ngati sanatsatire dongosolo limeneli.”
ijwhf-CN nkhani 4 ¶11-13
Mmene Mungathandizire Ana Anu pa Nkhani ya Mowa
Muziyamba ndi inuyo kukambirana ndi mwana wanu zokhudza mowa. Bambo wina wa ku Britain dzina lake Mark ananena kuti: “Mowa umasokoneza kwambiri ana. Tsiku lina ndinafunsa mwana wanga wamwamuna wa zaka 8 kuti afotokozepo maganizo ake ngati kumwa mowa n’kwabwino kapena ayi. Ndinkalankhula naye momasuka ngati kuti tikungocheza ndipo zimenezi zinathandiza kuti nayenso amasuke kunena maganizo ake pa nkhani ya mowa.”
Ngati nthawi zambiri mumakonda kunena za mavuto amene amakhalapo chifukwa cha mowa, zingathandize ana anu kudziwa kuopsa kwa mowa. Choncho potengera msinkhu wa mwana wanu, mukamakambirana nkhani zofunika pa moyo monga kupewa ngozi pamsewu komanso nkhani zokhudza kugonana, mungakambirane nayenso zokhudza kuopsa kwa mowa.
Muzikhala chitsanzo chabwino. Ana ali ngati thonje. Thonje likaviikidwa m’madzi, kaya akuda kapena oyera, limayamwa komanso kutengera mtundu wa madziwo. Ochita kafukufuku anapeza kuti nawonso ana amatengera kwambiri zimene makolo awo amakonda kuchita. Izi zikutanthauza kuti ngati inuyo mumaona kuti kumwa mowa ndi njira yokhayo yabwino yochepetsera nkhawa kapena mavuto anu, mwana wanunso amatengera zomwezo. Choncho muzikhala chitsanzo chabwino. Ndipo ngati mumamwa, muziyesetsa kumwa moyenera.
g17.6-CN 9 ¶5
Mungaphunzitse Bwanji Ana Anu Kukhala Odzichepetsa?
Muziwalimbikitsa kukhala opatsa. Muzithandiza mwana wanu kudziwa kuti “kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Mungachite zimenezi polemba mayina a anthu amene mungawathandize komanso mmene mungawathandizire monga kuwagulira zinthu, kuwapatsa ndalama ya thiransipoti kapena kuwakonzera zinthu zomwe zawonongeka. Kenako muzipita ndi mwana wanuyo pokathandiza anthuwo. Mwana wanu adzachita chidwi akamaona kuti mukusangalala chifukwa chothandiza ena. Adzaphunziranso kukhala wodzichepetsa poona zimene mumachita.—Lemba lothandiza: Luka 6:38.
Kufufuza Cuma Cauzimu
w92-CN 11/1 11 ¶7-8
Maphunziro m’Nthaŵi za m’Baibulo
7 Mu Israyeli, ana anaphunzitsidwa kuyambira pamsinkhu waung’ono kwambiri ndi onse aŵiri atate ndi amayi. (Deuteronomo 11:18, 19; Miyambo 1:8; 31:26) Mu Dictionnaire de la Bible la Chifalansa, katswiri wa Baibulo E. Mangenot analemba kuti: “Atangoyamba kumene kulankhula, mwana anaphunzira ndime zochepa za Chilamulo. Amayi wake anabwereza vesi; pamene analidziŵa, anamupatsa vesi lina. Pambuyo pake, lemba lolembedwa la mavesi amene anakhoza kuwatchula pamtima anapatsidwa kwa anawo. Motero, anaphunzitsidwa kuŵerenga, ndipo pamene anakula, anapitiriza malangizo awo achipembedzo mwa kuŵerenga ndi kusinkhasinkha pa lamulo la Ambuye.”
8 Zimenezi zikusonyeza kuti njira yakuphunzitsa yaikulu yogwiritsidwa ntchito inali yakuloŵeza zinthu pamtima. Zinthu zophunziridwa ponena za malamulo a Yehova ndi zochita zake ndi anthu ake zinafunikira kuloŵa mu mtima. (Deuteronomo 6:6, 7) Zinafunikira kulingaliridwa. (Salmo 77:11, 12) Kuthandiza achichepere ndi akulu kuloŵeza, njira zosiyanasiyana zolowezera zinagwiritsidwa ntchito. Zimenezi zinaphatikizapo malembo a alifabeti, mavesi otsatizana m’salmo oyamba ndi chilembo chosiyana, mu ndandanda ya alifabeti (monga ngati Miyambo 31:10-31, NW); mawu oyamba ndi chilembo chofanana kapena akamvekedwe kofanana; ndi kagwiritsiridwe ka ziŵerengelo, monga zotchulidwa m’theka lomalizira la Miyambo chaputala 30. Mokondweretsa, Kalenda ya Gezer, imodzi ya zitsanzo zakale kwambiri za zolembedwa Zachihebri, imalingaliridwa ndi akatswiri ena kukhala zolembedwa zoloŵeza za mwana wa sukulu.
SEPTEMBER 22-28
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU Mlaliki 1-2
Pitilizani Kuphunzitsa M’badwo Wotsatila
“Zimenezo Uziphunzitse kwa Amuna Okhulupilika”
3 Ambili timakonda nchito zathu, ndipo tingakonde kupitiliza nazo kwamuyaya. Koma cosapeweka n’cakuti, kuyambila kwa Adamu, m’badwo uliwonse umakalamba ndi kuloŵedwa m’malo ndi wina. (Mlal. 1:4) M’zaka zaposacedwapa, kusintha kumeneku kwakhala cinthu covuta kucilandila kwa Akhiristu ena. Nchito ya anthu a Yehova ikukulila-kulila, ndipo ikuloŵetsamo zambili. Nchito zambili tsopano zimafuna kutsatila njila za sayansi yamakono zimene zimasintha mofulumila. Njila zimenezi zingakhale zovutilapo kwa acikulile ena. (Luka 5:39) Mwina cifukwa sicingakhale cimeneco. Komabe, acinyamata ndiwo ali na mphamvu ndi nyonga kuposa acikulile. (Miy. 20:29) Conco, ni njila yacikondi komanso yothandiza kuti acikulile azikonzekeletsa acinyamata kutenga maudindo aakulu.—Ŵelengani Salimo 71:18.
4 Ena ali pa maudindo, zingawavute kugaŵilako acinyamata maudindo. Ena amaopa kuti pothela pake adzaluza udindo umene amaukonda kwambili. Ena amaopa kutaikidwa ulamulilo, poganiza kuti acinyamata sangayendetse bwino zinthu. Enanso angaganize kuti alibe nthawi yophunzitsa munthu wina. Komanso nawonso acinyamata, afunika kukhala oleza mtima ngati sapatsidwa maudindo owonjezeleka.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-E “Mlaliki”
“Mlaliki”
Mawu Aciheberi akuti Qo·heʹleth (kutanthauza “Wosonkhanitsa; Woitanitsa”) amafotokoza bwino nchito imene wolamulila anali nayo mu ulamulilo umene Mulungu anakhazikitsa mu Isiraeli. (Mla. 1:1, 12) Unali udindo wa wolamulila kuthandiza anthu a Mulungu kukhalabe okhulupilika kwa Mfumu yawo yaikulu komanso Mulungu wawo. (1 Maf. 8:1-5, 41-43, 66) Conco mfumu inali kuonedwa yabwino kapena yoipa potengela zimene inacita pothandiza anthu pa nkhani ya kulambila Yehova. (2 Maf. 16:1-4; 18:1-6) Wosonkhanitsa, yemwe anali Solomo, anali atacita kale zambili posonkhanitsa Aisiraeli ndi anthu ena ku kacisi. M’bukuli, iye anali kufuna kusonkhanitsa anthu a Mulungu kuti awathandize kupewa nchito zacabecabe ndiponso zopanda pake za m’dzikoli ndi kuwathandiza kugwila nchito zimene Mulungu wawo anali kufuna.
SEPTEMBER 29–OCTOBER 5
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU Mlaliki 3-4
Limbitsani Ukwati Wanu
ijwhf-CN nkhani 10 ¶2-8
Kodi Mungatani Kuti Zipangizo Zamakono Zisamakusokonezeni?
● Kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono mwanzeru kukhoza kulimbitsa banja lanu. Mwachitsanzo, amuna ena ndi akazi awo, amagwiritsira ntchito zipangizozi polumikizana pa nthawi imene sali limodzi.
“Meseji yachidule yongonena kuti ‘ndimakukonda’ kapena ‘ndakusowa’ ingatanthauze zambiri ndipo imakupangitsa kumva bwino.”—Jonathan.
● Kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono mopanda nzeru kukhoza kusokoneza banja lanu. Mwachitsanzo, anthu ena amangokhalira kucheza pa foni ndipo zimenezi zimachititsa kuti asamakhale ndi nthawi yokwanira yocheza ndi mwamuna kapena mkazi wawo.
“Sindikukayikira kuti pali nthawi zina pamene mwamuna wanga ankafuna atacheza nane, koma ankalephera chifukwa choti ndinkatanganidwa ndi foni.”—Julissa.
● Anthu ena amaona kuti akhoza kumakambirana zinthu zofunika ndi mwamuna kapena mkazi wawo kwinakunso akugwiritsa ntchito chipangizo chawo chamakono. Koma Sherry Turkle, yemwe ndi katswiri wa zachikhalidwe anatsutsa mfundo imeneyi. Iye ananena kuti “n’zosatheka kumachita zinthu ziwiri pa nthawi imodzi, ndipo tikamachita zinthu zingapo pa nthawi imodzi m’pamene zambiri zimawonongeka.” “Ndimasangalala kwambiri kucheza ndi mwamuna wanga akakhala kuti sakuchita zinthu zina. Koma ndikamacheza naye, iyeyo n’kumatanganidwa ndi foni, zimakhala ngati foniyo ndi yofunika kwambiri kuposa ineyo.”—Sarah.
Mfundo yofunika kwambiri: Mmene mumagwiritsira ntchito zipangizo zamakono zingachititse kuti banja lanu likhale lolimba kapena lisokonezeke.
Musazimitse “Lawi la Ya”
12 Kodi anthu okwatirana angatsanzire bwanji Akula ndi Purisika? Taganizirani zinthu zambiri zimene inuyo monga mwamuna kapena mkazi, mumafunika kuchita. Kodi n’zotheka kuti muzichitira limodzi zina mwa zinthu zimenezi monga banja, osati aliyense payekha? Mwachitsanzo, Akula ndi Purisika ankalalikira limodzi. Kodi inunso nthawi zambiri mumakonza zoti muzilalikira limodzi? Akula ndi Purisika ankagwiranso ntchito limodzi. Mwina inuyo ndi mwamuna kapena mkazi wanu simugwira ntchito yofanana, koma kodi mungamagwire limodzi ntchito zapakhomo? (Mlal. 4:9) Mukamathandizana ntchito inayake, mumagwirizana kwambiri ndiponso mumapeza mpata wocheza. A Robert ndi a Linda akhala m’banja kwa zaka zoposa 50. A Robert anati: “Kunena zoona, sitipeza nthawi yambiri yochitira limodzi zinthu zosangalatsa. Koma ndikamatsuka mbale, mkazi wanga n’kumapukuta kapena ndikamalima panja, iye n’kubwera kudzandithandiza, ndimasangalala kwambiri. Kuchitira zinthu limodzi kumatithandiza kuti tizikhala ogwirizana ndipo chikondi chathu chimapitiriza kukula.”
13 Komabe, muzikumbukira kuti kungokhala limodzi, sikutanthauza kuti nthawi zonse muzichita zinthu mogwirizana. Mayi wina wa pabanja ku Brazil ananena kuti: “Masiku ano, pali zinthu zambiri zosokoneza, moti ndaona kuti tikhoza kugwera mumsampha womaganiza kuti timachitira zinthu limodzi chabe chifukwa choti timakhala nyumba imodzi. Ndaphunzira kuti kuwonjezera pa kukhala limodzi, timafunikiranso kumachita chidwi ndi mnzathuyo.” Taonani zimene Bruno ndi mkazi wake Tays amachita kuti aliyense azichita chidwi ndi mnzake. Iye anati: “Pa nthawi yathu yocheza, timaika patali mafoni athu n’kumangocheza basi.”
14 Koma bwanji ngati inuyo ndi mwamuna kapena mkazi wanu simusangalala kuchitira zinthu limodzi? Mwina mumakonda zinthu zosiyana kapenanso mumangokhalira kuyambana, ndiye kodi mungatani? Taganizirani za moto, womwe tinautchula kumayambiriro kuja. Motowu sumangofikira kuyaka mwamphamvu. Umafunika kusonkhezera pang’onopang’ono, kenako n’kumaika nkhuni zazikulu. Mofanana ndi zimenezi, bwanji osayamba ndi kumapeza nthawi yochepa tsiku lililonse yochitira zinthu limodzi? Muzionetsetsa kuti muzichita zinthu zomwe nonse mumasangalala nazo, osati zimene zingachititse kuti muyambe kukangana. (Yak. 3:18) Kuyamba mwapang’onopang’ono kungathandize kuti mukulitse chikondi chanu.
Musazimitse “Lawi la Ya”
3 Kuti asazimitse “lawi la Ya,” onse, mwamuna ndi mkazi ayenera kuyesetsa kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova. Kodi zimenezi zimathandiza bwanji banja lawo? Anthu okwatirana akamaona kuti ubwenzi wawo ndi Atate wawo wakumwamba ndi wofunika kwambiri, amakhala okonzeka kutsatira malangizo ake, zimene zimawathandiza kupewa komanso kulimbana ndi mavuto omwe angachititse kuti chikondi chawo chichepe. (Werengani Mlaliki 4:12.) Anthu omwe ali pa ubwenzi ndi Yehova amayesetsa kumutsanzira ndipo amakhala ndi makhalidwe monga kukoma mtima, kuleza mtima komanso kukhululuka. (Aef. 4:32–5:1) Anthu okwatirana omwe amasonyeza makhalidwewa siziwavuta kuti azikondana kwambiri. Mlongo wina dzina lake Lena, yemwe wakhala pabanja kwa zaka zoposa 25, anati: “Zimakhala zosavuta kukonda komanso kulemekeza munthu yemwe amakonda Yehova.”
Kufufuza Cuma Cauzimu
Musaleke Kulambila Yehova pa Nthawi ya Ciletso
Tisamale na zimene timauza anthu ena. Pa nthawi ya ciletso, tifunika kuzindikila “nthawi yokhala cete.” (Mlal. 3:7) Sitiyenela kuulula zinthu zimene zingatiikitse m’mavuto, monga maina a abale na alongo athu, malo amene timacitilako misonkhano, mmene timalalikilila, kapena mmene timalandilila cakudya cauzimu. Sitiyenela kuulula zimenezi kwa anthu oimila boma, kapena kwa anzathu kapena acibululu, kaya amene akhala m’dziko lathu kapena ku dziko lina. Ngati tingacite zimenezi, tingaike miyoyo ya abale athu pa ciwopsezo.—Ŵelengani Salimo 39:1.
OCTOBER 6-12
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU Mlaliki 5-6
Mmene Timaonetsela Ulemu Waukulu kwa Mulungu Wathu Wamkulu
w08-CN 8/15 15-16 ¶17-18
Lemekezani Yehova mwa Kusonyeza Ulemu
17 Tifunikira kusonyeza ulemu wapadera polambira Yehova. Lemba la Mlaliki 5:1 limati: “Samalira phazi lako popita ku nyumba ya Mulungu.” Mose ndi Yoswa analamulidwa kuvula nsapato zawo pamalo opatulika. (Eks. 3:5; Yos. 5:15) Iwo amafunika kuchita zimenezi posonyeza ulemu. Ansembe achiisiraeli analamulidwa kuvala zovala za miyendo kuti ‘abise maliseche.’ (Eks. 28:42, 43) Zimenezi zinathandiza kuti azivala modzilemekeza akamatumikira pa guwa la nsembe. Aliyense m’banja la wansembe amafunikira kutsatira malamulo a Mulungu okhudza kudzilemekeza.
18 Motero, monga olambira a Yehova tifunikira kusonyeza ulemu m’mbali zonse za moyo wathu. Kuti ena azitipatsa ulemu ifenso tiyenera kuwapatsa ulemu. Tisasonyeze ulemu mwachiphamaso kapena mongodzionetsera chabe. Koma uzikhala ulemu wochokera mu mtima chifukwa Mulungu amaona mumtima. (1 Sam. 16:7; Miy. 21:2) Tiyenera kukhala aulemu nthawi zonse, m’zochita zathu ndi pochita zinthu ndi ena. Ndipo tiyeneranso kumadzilemekeza. Ndithudi, tizisonyeza ulemu polankhula ndi pochita zinthu zina. Pankhani ya khalidwe lathu, kavalidwe ndi kudzikongoletsa, tifunikira kutsatira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe; koma m’zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu.” (2 Akor. 6:3, 4) Mwa njira imeneyi ‘timakometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu, Mulungu, m’zinthu zonse.’—Tito 2:10.
w09-CN 11/15 11 ¶21
Kuphunzira Baibulo Kungathandize Kuti Mapemphero Anu Azikhala Atanthauzo
21 Yesu anapemphera mwaulemu ndiponso ndi chikhulupiriro chonse. Mwachitsanzo asanaukitse Lazaro, “Yesu anakweza maso ake kumwamba ndi kunena kuti: ‘Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva. Inde, ndikudziwa kuti mumandimva nthawi zonse.’” (Yoh. 11:41, 42) Kodi mapemphero anu amasonyeza ulemu ndi chikhulupiriro chotero? Mukawerenga bwinobwino pemphero la Yesu lachitsanzo, mudzaona kuti mbali zazikulu zimene anatchula ndi kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova, kubwera kwa Ufumu wake ndi kuchitika kwa chifuniro chake. (Mat. 6:9, 10) Ndiyeno ganizirani za mapemphero anu. Kodi amasonyeza kuti inuyo mumafunadi Ufumu wa Yehova, kuchita chifuniro chake ndiponso mumafuna kuona dzina lake loyera litayeretsedwa? Mapemphero anu ayenera kusonyeza zimenezi.
“Uzikwaniritsa Zinthu Zimene Walonjeza”
12 Koma kubatizidwa ndi chiyambi chabe. Munthu akabatizidwa ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene analonjeza kwa Mulungu. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zinthu zakhala zikuyenda bwanji kuyambira pamene ndinabatizidwa? Kodi ndikutumikirabe Yehova ndi mtima wonse? (Akol. 3:23) Kodi ndimapemphera, kuwerenga Mawu a Mulungu, kusonkhana komanso kulalikira nthawi zonse? Kapena kodi ndafooka pang’ono pa zinthu zimenezi? Paja mtumwi Petulo anati tiyenera “kuwonjezera pa chikhulupiriro chathu kudziwa zinthu, kudziletsa, kupirira ndiponso kudzipereka kwa Mulungu.” (Werengani 2 Petulo 1:5-8.) Makhalidwe amenewa angatithandize kuti tizitumikirabe Mulungu mwakhama.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
Lemba la Mlaliki 5:8 limakamba za wolamulila amene amapondeleza anthu osauka na kuwacitila zinthu zopanda cilungamo. Wolamulilayo afunika kukumbukila kuti winawake amene ali na malo apamwamba kapena kuti ulamulilo waukulu kuposa iye, akuona zimene akucita. Ndipo pangakhale anthu ena amene ali na ulamulilo waukulu kuposa onsewo. Koma n’zacisoni kuti m’maboma a anthu, olamulila onse nthawi zina amakhala opanda cilungamo, ndipo anthu wamba amavutika cifukwa ca kupanda cilungamo kwawo.
Koma olo zinthu zivute bwanji, tingapeze citonthozo podziŵa kuti Yehova akuyang’ana ngakhale olamulila akulu-akulu m’maboma a anthu. Tingapemphe thandizo kwa Mulungu na kumutulila nkhawa zathu. (Sal. 55:22; Afil. 4:6, 7) Tidziŵa kuti “maso a Yehova akuyenda-yenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.”—2 Mbiri 16:9.
Conco, lemba la Mlaliki 5:8 limatikumbutsa mmene zinthu zilili m’maboma a anthu kuti nthawi zonse pamakhala winawake wa ulamulilo waukulu kuposa ena. Koma cofunika kwambili n’cakuti lembali limatithandiza kukumbukila mfundo yakuti Yehova ndiye Wolamulila Wamkulu kuposa onse. Palipano, iye akulamulila kupitila mwa Mwana wake Yesu Khristu, amene ni Mfumu ya Ufumu wake. Yehova Wamphamvuzonse ameneyo, akuona zonse zimene zikucitika, ndipo ni wacilungamo nthawi zonse. Umu ni mmenenso Mwana wake alili.
OCTOBER 13-19
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU Mlaliki 7-8
‘Muzipita Kunyumba ya Malilo’
“Lilani Ndi Anthu Amene Akulila”
Njila ina imene anthu ofedwa angapezele citonthozo ni kupitila mumpingo wacikhristu. (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:11.) Kodi anthu amene ali na “mtima wosweka” mungawatonthoze bwanji ndi kuwalimbikitsa? (Miy. 17:22) Kumbukilani kuti pali “nthawi yokhala cete ndi nthawi yolankhula.” (Mlal. 3:7) Mlongo wina wamasiye, dzina lake Dalene anati: “Anthu amene afedwa amafuna kufotokoza maganizo awo ndi mmene amvelela. Conco, cinthu cofunika kwambili cimene mungacite kwa wofedwa ndi kumumvetsela popanda kum’dula mau.” Junia, amene m’bale wake anadzipha, anakamba kuti: “Ngakhale kuti simungamvetsetse zonse zokhudza cisoni cimene munthu wofedwa ali naco, cofunika ngako ni nkhawa imene mwamuonetsa mwa kuyesetsa kumumvetsela.”
Thandizani Ena Kulimbana na Nkhawa
15 M’bale William, amene anafedwa mkazi wake zaka zingapo zapitazo, anati: “Zimanilimbikitsa kwambili anthu akamakamba zabwino zimene mkazi wanga anali kucita. Zimanithandiza kuona kuti anali kum’konda na kum’lemekeza. Zimanitonthoza kwambili, cifukwa n’nali kum’konda ngako mkazi wanga, ndipo anali kunithandiza m’zambili.” Mlongo wina wofedwa, dzina lake Bianca, anati: “Nimalimbikitsidwa kwambili ngati ena apemphela nane na kuŵelenga nane lemba limodzi kapena aŵili. Nimatonthozedwa akamakamba za mwamuna wanga, kapena kunimvetsela pamene nifotokoza za iye.”
“Lilani Ndi Anthu Amene Akulila”
16 Kupemphela pamodzi na Mkhristu wofedwa ndiponso kumupemphelela n’zofunika kwambili. N’zoona kuti, cifukwa ca cisoni, zingakhale zovuta kufotokoza bwino-bwino maganizo anu popemphela. Komabe, kupemphela naye mocokela pansi pamtima kungamutonthoze kwambili, ngakhale m’takhala kuti mukulila ndipo mau anu sakumveka bwino. Dalene anati: “Nthawi zina alongo akabwela kudzaniona, nimawapempha kuti anipemphelele. Poyamba kupemphela, nthawi zambili amakamba movutikila, koma posakhalitsa mau awo amayamba kumveka amphamvu ndi acidalilo, ndipo pemphelo limene amapeleka limakhala locokela pansi pamtima. Cikhulupililo canga cimalimba kwambili nikaganizila cikondi cawo, nkhawa imene amanionetsa, ndi cikhulupililo cawo.”
“Lilani Ndi Anthu Amene Akulila”
17 Kutalika kwa nthawi imene anthu ofedwa amakhala na cisoni kumasiyana-siyana. Conco, muzilimbikitsa wofedwa osati cabe panthawi ya malilo pamene mabwenzi ndi acibululu ambili alipo, koma ngakhale kwa miyezi ingapo pambuyo pakuti ena abwelela ku zocita zawo za tsiku na tsiku. Baibo imati: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.” (Miy. 17:17) Akhristu afunika kupitiliza kutonthoza mnzawo wofedwa mpaka pamene iye adzakwanitsa kupilila payekha.—Ŵelengani 1 Atesalonika 3:7.
18 Kumbukilani kuti pali zinthu zina zimene zingadzutse cisoni ca munthu. Zinthu zimenezi ni monga zocitika zapadela, nyimbo zinazake, masinapu, ngakhale fungo la zinazake, mau, kapena nyengo inayake m’caka. Ngati munthu anafedwa mnzake wam’cikwati, amavutika kwambili na cisoni nthawi yoyamba pamene acita yekha zinthu zimene anazoloŵela kucita ndi mnzakeyo. Zinthu zimenezi ndi monga kupezeka pa misonkhano ikulu-ikulu kapena pa Cikumbutso. M’bale wina anati: “Mkazi wanga atamwalila, n’nadziŵa kuti tsiku lokumbukila cikwati cathu likadzafika nidzavutika kwambili ndi cisoni, ndipo zinalidi zovuta. Koma abale na alongo ena, amene nanzanga anakonza zakuti tidzakhale na maceza n’colinga cakuti patsikulo nisadzakhale nekha.”
19 Komabe, musaiŵale kuti ofedwa amafunika citonthozo nthawi zonse, osati cabe pa nthawi ya zocitika zapadela. Junia anati: “Nthawi zambili, kukhala na maceza ndi kupeleka thandizo kwa munthu pamene kulibe zocitika zapadela kumakhala kothandiza kwambili. Kucita zinthu mwanjila imeneyi n’kopindulitsa ndiponso kumatonthoza kwambili.” N’zoona kuti sitingathetse cisoni conse cimene munthu amakhala naco ngati wokondedwa wake wamwalila. Koma tingathe kum’tonthoza mwa kuyesetsa kumuthandiza m’njila zosiyana-siyana. (1 Yoh. 3:18) Gaby anati: “Niyamikila ngako Yehova cifukwa ca akulu acikondi amene anali nane pa nthawi yonse imene n’nali kuvutika. Ananicititsa kuona kuti Yehova amanikonda.”
Kufufuza Cuma Cauzimu
“Mwakutelo, Onse Adzadziŵa Kuti Ndinu Ophunzila Anga”
18 Nthawi zina, tingaone kuti tiyenela kukambilana naye Mkhristu mnzathu amene anatilakwila. Koma coyamba, tingacite bwino kudzifunsa mafunso monga akuti: ‘Kodi nikudziŵa bwino zonse zimene zinacitika?’ (Miy. 18:13) ‘Kodi n’kutheka kuti sicinali colinga cake kuti anikhumudwitse?’ (Mlal. 7:20) ‘Kodi inenso n’nalakwilapo wina mwanjila imeneyi?’ (Mlal. 7:21, 22) ‘Ngati ningakambilane naye nkhaniyo, kodi zidzangowonjezela mavuto?’ (Ŵelengani Miyambo 26:20.) Tikamaganizila mafunso ngati amenewa, cikondi cathu pa m’bale wathuyo cidzatilimbikitsa kungonyalanyaza colakwaco.
OCTOBER 20-26
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU Mlaliki 9-10
Muziwaona Moyenela Mavuto Anu
w13 8/15 14 ¶20-21
‘Musakwiile Yehova’
20 Dziŵani cimene cimacititsa mavuto. N’cifukwa ciani tiyenela kutelo? Cifukwa cakuti mwina tikukumana ndi mavuto kaamba ka zolakwa zathu. Ngati zili conco, tiyenela kuvomeleza mfundo imeneyi. (Agal. 6:7) Musayese kuimba mlandu Yehova cifukwa ca mavutowo. N’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kupanda nzelu? Ganizilani citsanzo ici: Galimoto ingathe kuthamanga kwambili. Ndiyeno yelekezelani kuti galimotoyo yacita ngozi cifukwa cakuti dalaivala anali kuithamangitsa kwambili. Kodi kungakhale kwanzelu kuimba mlandu amene anapanga galimoto imeneyo cifukwa ca ngoziyo? Iyai. Mofanana ndi zimenezi, Yehova anatilenga ndi ufulu wodzisankhila zocita. Koma watipatsanso malangizo amene angatithandize kupanga zosankha zanzelu. Conco, sitiyenela kuimba mlandu Mlengi wathu cifukwa ca zolakwa zathu.
21 Koma sikuti mavuto onse amene timakumana nao ali kaamba ka zolakwa zathu. Zinthu zina zimacitika cifukwa ca “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka” zimene tingakumane nazo. (Mlal. 9:11) Koma koposa zonse, tisaiwale kuti Satana Mdyelekezi ndiye amacititsa mavuto ambili. (1 Yoh. 5:19; Chiv. 12:9) Iye ndiye mdani wathu osati Yehova.—1 Pet. 5:8.
Yehova Amaona Atumiki Ake Odzicepetsa Kukhala Amtengo Wapatali
10 Kudzicepetsa kumatithandiza kuti tiziona zinthu moyenela mu umoyo wathu. Nthawi zina, tingaone kapena kukumana na zinthu zimene tiona kuti n’zopanda cilungamo. Mfumu yanzelu Solomo anati: “Ndaonapo anchito atakwela pamahachi, koma akalonga akuyenda pansi ngati anchito.” (Mlal. 10:7) Anthu aluso kwambili, nthawi zina sapatsidwa ulemu. Ndipo nthawi zina anthu amene alibe luso kweni-kweni, ni amene amalandila ulemu woculuka. Ngakhale n’conco, Solomo anaonetsa kuti n’cinthu canzelu kungovomeleza mmene zinthu zilili, m’malo mongokhalila kuda nkhawa cifukwa ca zinthu zimene sizinayende bwino. (Mlal. 6:9) Ngati ndife odzicepetsa, cidzakhala cosavuta kungovomeleza mmene zinthu zilili mu umoyo wathu.
w11 10/15 8 ¶1-2
Kodi Zimene Mumachita pa Nthawi Yosangalala Zimakhala Zopindulitsa?
M’BAIBULO muli mawu ambiri osonyeza kuti Yehova samangofuna kuti tikhale ndi moyo, koma kuti tizisangalala nawo. Mwachitsanzo, lemba la Masalimo 104:14, 15 limanena kuti Yehova amachititsa “kuti chakudya chituluke m’nthaka, komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu. Amachita zonsezi kuti nkhope ya munthu isalale ndi mafuta, komanso kuti apereke chakudya chimene chimakhutiritsa mtima wa munthu.” Yehova ndi amene amatipatsa chakudya chimene chimatithandiza kuti tizikhala ndi moyo. Amameretsa mbewu kuti tipeze chakudya, mafuta ndi vinyo. Ngakhale kuti vinyo sali m’gulu la zinthu zofunika kwambiri pa moyo, ‘amachititsa mtima kusangalala.’ (Mlal. 9:7; 10:19) Apa n’zoonekeratu kuti Yehova amafuna kuti tizisangalala ndiponso kuti mitima yathu izikhala yodzaza ndi “chimwemwe.”—Mac. 14:16, 17.
2 Choncho tisamaone ngati talakwitsa ngati nthawi zina timakonza nthawi yosangalala. Mwina timakonza zokaona “mbalame zam’mlengalenga” ndi “maluwa akutchire,” komanso kuchita zinthu zina zimene zimatitsitsimula. (Mat. 6:26, 28; Sal. 8:3, 4) Kukhala ndi moyo wosangalala “ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.” (Mlal. 3:12, 13) Kudziwa kuti nthawi yosangalala ndi mphatso, kungatithandize kuti tiziigwiritsa ntchito m’njira yosangalatsa amene anaipereka.
Kufufuza Cuma Cauzimu
Lankhulani Mau “Olimbikitsa”
11 Mijedo yovulaza, misece. Kujeda kumatanthauza kulankhula za anthu ena ndi umoyo wao. Koma kodi kulankhula za anthu ena ndi kulakwa? Iyai, makamaka ngati zimene tikamba ndi zinthu zabwino, ndi zothandiza, monga za amene anabatizidwa posacedwapa kapena amene afunikila cilimbikitso. Akristu a m’nthawi ya atumwi anali ndi cidwi cofuna kudziŵa za umoyo wa ena ndi kuuzana nkhani zokhudza okhulupilila anzao. (Aefeso 6:21, 22; Akolose 4:8, 9) Komabe, mijedo ingakhale yoipa ngati munthu akamba zabodza ndi kuulula zisinsi za ena. Ndipo coipa kwambili n’cakuti mijedo imayambitsa misece, imene nthawi zonse imakhala yovulaza. Misece ndi “kunenela munthu zonama . . . zimene zimaononga mbili yake.” Mwacitsanzo, Afalisi anali kudyela Yesu misece yovulaza kuti amuwonongele mbili. (Mateyu 9:32-34; 12:22-24) Misece nthawi zambili imayambitsa mikangano.—Miyambo 26:20.
12 Yehova amakhumudwa ndi anthu amene amagwilitsila nchito mphatso yao ya kulankhula kuononga mbili ya anzao kapena kuyambitsa magaŵano. Amadana ndi anthu amene ‘amayambitsa mikangano pakati pa abale.’ (Miyambo 6:16-19) Liu la Cigiliki lakuti di·aʹbo·los, limatembenuzidwa kuti “woneneza” ndipo limeneli ndi dzina linanso la Satana. Iye ndi “Mdyelekezi” woneneza Mulungu. (Chivumbulutso 12:9, 10) Ndithudi, tiyenela kupewa kalankhulidwe kamene kangaticititse kukhala ngati Mdyelekezi. Mumpingo simuyenela kukhala anthu olankhula misece imene imasonkhezela nchito za thupi monga “mikangano” ndi “magawano.” (Agalatiya 5:19-21) Conco, musanauze munthu wina nkhani, dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhaniyi ndi yoona? Nanga ndi cikondi kuuzako ena? Kodi n’kofunikadi kuti ndiuzeko ena nkhaniyi?—Ŵelengani 1 Atesalonika 4:11.
OCTOBER 27–NOVEMBER 2
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU Mlaliki 11-12
Mmene Mungakhalile Athanzi Komanso Acimwemwe
g-CN 3/15 13 ¶6-7
Kamphepo Kayaziyazi Komanso Dzuwa Ndi Mankhwala
Dzuwa nalonso limapha tizilombo toyambitsa matenda. Magazini ina inanena kuti “tizilombo tambiri toyambitsa matenda monga chimfine, timafa tikawombedwa ndi dzuwa.”—Journal of Hospital Infection.”
Popeza taona kuti kamphepo kayaziyazi komanso dzuwa ndi mankhwala, si bwino kumangobindikira m’nyumba. Muzikonda kukhala panja nthawi zina n’kumaothera dzuwa komanso kupitidwa kamphepo kayaziyazi. Zimenezi zingakuthandizeni kuti musamadwaledwale.
Yamikilani Mphatso ya Mulungu ya Moyo
6 Ngakhale kuti Baibo si buku la zacipatala kapena lophunzitsa za thanzi, imafotokoza maganizo a Yehova pa nkhani zimenezi. Mwacitsanzo, iye amatilangiza kuti ticotse zinthu zimene zingawononge thupi lathu. (Mlal. 11:10) Baibo imati tizipewa kudya kwambili na kumwa kwambili, cifukwa zimaika moyo wathu pa ciwopsezo. (Miy. 23:20) Yehova amafuna kuti tizisankha zimene timadya na kumwa, komanso kuculuka kwake.—1 Akor. 6:12; 9:25.
7 Mwa kugwilitsa nchito luntha la kuzindikila, tikhoza kupanga zisankho zoonetsa kuti mphatso ya Mulungu ya moyo timailemekeza kwambili. (Sal. 119:99, 100; ŵelengani Miyambo 2:11.) Mwacitsanzo, timakhala osamala kwambili na zakudya zimene timadya. Ngati timakonda cakudya cina cake koma tapeza kuti cimatidwalitsa, nzelu zimatithandiza kucipewa. Cina, timaonetsa kuti ndife oganiza bwino tikamagona mokwanila, tikamacita maseŵela olimbitsa thupi nthawi zonse, komanso tikamasunga mathupi athu na nyumba zathu zili zaukhondo.
“Muzicita Zimene Mawu Amanena”
2 Alambili a Yehova ni anthu acimwemwe. Cifukwa ciyani? Tili na zifukwa zambili, koma cifukwa cacikulu n’cakuti timaŵelenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse, ndipo timayesetsa kucita zimene taŵelenga.—Ŵelengani Yakobo 1:22-25.
3 Timapeza mapindu ambili ngati timacita “zimene mawu amanena.” Mwa citsanzo, tikacita zimene taŵelenga m’Mawu a Mulungu, timakondweletsa Yehova. Kucita zimenezi kumatibweletsela cimwemwe. (Mlal. 12:13) Tikamacita zimene timaŵelenga m’Mawu ouzilidwa a Mulungu, timakhala paubale wolimba na a m’banja lathu komanso okhulupilila anzathu. Mwina mwaona kuti mfundoyi ni yoona pa umoyo wanu. Kuwonjezela apo, timapewa mavuto ambili amene anthu omwe satsatila mfundo za Yehova amakumana nawo. Zili monga anakambila Mfumu Davide. Davide m’nyimbo yake atachula za cilamulo ca Yehova na zigamulo zake, ananena kuti: “Munthu wosunga zigamulozo amapeza mphoto yaikulu.”—Sal. 19:7-11.
Kufufuza Cuma Cauzimu
it-E Kuuzilidwa ¶10
“Kuuzilidwa”
Pali umboni woonetsa kuti amuna amene Mulungu anawagwilitsa nchito kulemba Baibo sanali kungocita zinthu ngati maloboti, kumalemba zilizonse zimene auzidwa. Ponena za mtumwi Yohane, timawelenga m’Baibo kuti Mulungu anamupatsa Chivumbulutso kudzela mwa mngelo wake “pogwilitsa nchito zizindikilo” ndi kuti “Yohaneyo anacitila umboni mawu amene Mulungu anapeleka ndiponso umboni umene Khristu anapeleka, kutanthauza zonse zimene anaona.” (Chiv. 1:1, 2) Yohane ‘atadzazidwa ndi mzimu woyela anapezeka kuti ali m’tsiku la Ambuye’ ndipo anauzidwa kuti: “Zimene ukuona, uzilembe mumpukutu.” (Chiv. 1:10, 11) Conco, Yehova anaona kuti zinali bwino kulola olemba Baibo kugwilitsa nchito nzelu zawo kusankha mawu amene akanafotokoza bwino masomphenya amene anali kuona. (Hab 2:2) Koma anali kuwayang’anila kuti aonetsetse kuti zonse zimene anali kulemba zinali zoona komanso zolondola, ndiponso kuti zinali zogwilizana ndi cifunilo ca Yehova. (Miy. 30:5, 6) Mawu a pa Mlaliki 12:9, 10, amaonetsa kuti olemba Baibo “anaganizila mozama komanso anafufuza zinthu mosamala,” ndiponso kuti analemba zinthu mwatsatanetsatane n’colinga coti alembe ‘mawu osangalatsa komanso olondola a coonadi.’—Yelekezelani ndi Luka 1:1-4.