NYIMBO 33
Tulila Yehova Nkhawa Zako
Yopulinta
(Salimo 55)
1. Conde nipempha Yehova
Muniyankhe pemphelo.
Mvelani kulila kwanga,
Ndipo nithandizeni.
(KOLASI)
Uzani Yehova nkhawa,
Iye adzakuthandizani.
Adzakutsogolelani
Kuti mutetezeke.
2. Sembe nenze monga nkhunda,
Sembe nambululuka,
Kuthaŵa adani anga
Kuti asanipeze.
(KOLASI)
Uzani Yehova nkhawa,
Iye adzakuthandizani.
Adzakutsogolelani
Kuti mutetezeke.
3. Yehova ‘katitonthoza
Timapeza mtendele.
Iye adzatithandiza
Tisakhale na nkhawa.
(KOLASI)
Uzani Yehova nkhawa,
Iye adzakuthandizani.
Adzakutsogolelani
Kuti mutetezeke.
(Onaninso Sal. 22:5; 31:1-24.)