NYIMBO 107
Cikondi ca Umulungu
Yopulinta
(1 Yohane 4:19)
1. Timaphunzila cikondi kwa M’lungu,
Poona citsanzo
Wationetsa mu zocita zake,
Kuti ise tim’tengele.
Polola kuti Yesu atifele,
Kuti ’se anthu tikhululukidwe.
Cikondi cake ni copambanadi!
Njila zake ni zacikondi.
2. Cikondi cathu poyenda na M’lungu,
Cikula kwambili.
Citithandiza kukonda abale,
Nthawi zonse, inde onse.
Okonda M’lungu na kuzonda m’bale
Anama ndithu, izo n’zosatheka.
Tisasungile abale zifukwa,
Cikondici ni ca zoona.
3. Cikondi cathu cimatipangitsa
Kukhala pamodzi.
Ndipo Yehova amasangalala
Tikakhala capamodzi.
Cikondi cathu na cisangalalo
Tizionetse pomutumikila.
Mwa Mau ake na abale athu
Timaona cikondi cake.
(Onaninso Aroma 12:10; Aef. 4:3; 2 Pet. 1:7.)