ZAKUMAPETO
Zimene Ulosi wa Danieli Unakambilatu za Kufika kwa Mesiya
MNENELI Danieli anakhalako zaka zoposa 500 Yesu akalibe kubadwa. Ngakhale ni conco, Yehova anauza Danieli zinthu zimene zinali kudzathandiza kudziŵa nthawi yeni-yeni pamene Yesu anali kudzadzozedwa, kapena kuti kusankhidwa kukhala Mesiya, kapena kuti Kristu. Danieli anauzidwa kuti: “Uyenela kudziŵa ndi kuzindikila kuti kucokela pamene mau adzamveka onena kuti Yerusalemu akonzedwe ndi kumangidwanso, kufika pamene Mesiya Mtsogoleli adzaonekele, padzadutsa milungu 7, komanso milungu 62.”—Danieli 9:25.
Kuti tipeze nthawi ya kufika kwa Mesiya, coyamba tiyenela kudziŵa pamene ulosi wa Danieli wokamba za kubwela kwa Mesiya unayamba kukwanilitsika. Malinga ndi ulosi umenewu, nthawi yake inali ‘kucokela pamene mau anamveka onena kuti Yerusalemu akonzedwe ndi kumangidwanso.’ Kodi ‘mau anamveka’ liti? Mogwilizana ndi zimene Nehemiya, wolemba Baibo, anakamba, mau omanganso mpanda wozungulila Yerusalemu anapelekedwa “m’caka ca 20 ca mfumu Aritasasita.” (Nehemiya 2:1, 5-8) Kodi lamulo limeneli linapelekedwa liti? Akatswili a mbili yakale amakamba motsimikiza kuti linapelekedwa mu 455 B.C.E. Apa ndiye panayambila ulosi wa Danieli wokamba za Mesiya.
Danieli amationetsa utali wa nthawi imene inayenela kupitapo kuti “Mesiya Mtsogoleli” afike. Ulosiwo umachula “milungu 7, komanso milungu 62”—yonse pamodzi ikwana milungu 69. Kodi nthawi imeneyi ndi yaitali bwanji? Mabaibo osiyana-siyana amaonetsa kuti, milungu imeneyi si milungu ya masiku 7, koma milungu ya zaka. Kutanthauza kuti mlungu uliwonse umaimila zaka 7. Kaŵelengedwe kameneka ka milungu ya zaka kanali kofala kwa Ayuda a m’nthawi yakale. Mwacitsanzo, caka cacisanu ndi ciŵili ciliconse anali kukumbukila caka ca sabata. (Ekisodo 23:10, 11) Conco, milungu 69 yaulosi imapanga zigao 69, cigao ciliconse ca zaka 7, kapena kuti zaka 483 zonse pamodzi.
Tsopano cofunikila ndi kuŵelengela. Tikaŵelenga zaka 483 kucokela m’caka ca 455 B.C.E., zimatifikitsa m’caka ca 29 C.E. Ndico caka cimene Yesu anabatizika ndi kukhala Mesiya.a (Luka 3:1, 2, 21, 22) Kodi kukwanilitsika kwa ulosi wa m’Baibo kumeneku si kolimbikitsa cikhulupililo?
a Kucokela m’caka ca 455 B.C.E. kudzafika m’caka ca 1 B.C.E. panapita zaka 454. Kucokela m’caka ca 1 B.C.E. kudzafika m’caka ca 1 C.E. pali caka cimodzi. Ndipo kucokela m’caka ca 1 C.E. kudzafika m’caka ca 29 C.E. pali zaka 28. Kuonkhetsa manambala atatu awa (454+1+28) timapeza zaka zokwana 483. Yesu “anaphedwa” m’caka ca 33 C.E., mkati mwa milungu 70 ya zaka. (Danieli 9:24, 26) Onani buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli! mutu 11, ndi buku lakuti Insight on the Scriptures, Voliyamu 2, pamapeji 899 mpaka 901. Mabuku onse aŵili awa analembedwa ndi Mboni za Yehova.