LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 205-nkhani 206 pala. 5
  • Cifukwa Cake Akristu Oona Sagwilitsila Nchito Mtanda Polambila

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Cifukwa Cake Akristu Oona Sagwilitsila Nchito Mtanda Polambila
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 205-nkhani 206 pala. 5

ZAKUMAPETO

Cifukwa Cake Akristu Oona Sagwilitsila Nchito Mtanda Polambila

Anthu ambili amakonda mtanda ndipo amaulemekeza kwambili. Buku lina limachula mtanda kukhala “cizindikilo cacikulu ca cipembedzo Cacikristu.” (The Encyclopædia Britannica) Komabe, Akristu oona sagwilitsila nchito mtanda polambila. N’cifukwa ciani?

Cifukwa cacikulu n’cakuti Yesu Kristu sanafele pamtanda. Liu la Cigiriki lotembenuzidwa kuti “mtanda” ni stau·rosʹ. Kweni-kweni limatanthauza “mtengo woongoka.” Baibo yochedwa kuti The Companion Bible imakamba kuti: [Stau·rosʹ] silimatanthauza mitengo iŵili yopingasa mwanjila iliyonse . . . M’malemba a Cigiriki a mu [Cipangano Catsopano] mulibe mau alionse amene amaonetsa kuti panali mitengo iŵili.”

M’malemba ena, olemba Baibo anagwilitsila nchito liu lina pochula cinthu cimene Yesu anafelapo. Liu la Cigiriki limenelo n’lakuti xyʹlon. (Machitidwe 5:30; 10:39; 13:29; Agalatiya 3:13; 1 Petulo 2:24) Liu limeneli limatanthauza “thabwa” kapena “mtengo.”

Pofotokoza cifukwa cimene nthawi zambili anali kugwilitsila nchito mtengo umodzi ponyonga anthu, buku lina la Cijelemani, lolembedwa ndi Hermann Fulda limati: “Mitengo sinali kupezeka pena paliponse pamalo osankhidwa kunyongelapo anthu. Conco anali kukumbila mtengo umodzi cabe m’nthaka. Pamtengo umodzi umenewo m’pamene anali kumanga kapena kukhokhomela anthu ophwanya malamulo. Anali kucita kuwakwezeka ndi kuwamanga manja m’mwamba, ndi kumanganso mapazi ao.”—The Cross and the Crucifixion.

Koma umboni wotsimikizika kwambili pa maumboni onse, umapezeka m’Mau a Mulungu. Mtumwi Paulo anati: “Kristu anatiombola ku tembelelo la Cilamulo, atakhala tembelelo m’malo mwathu; pakuti kwalembedwa: ‘Wotembeleledwa ali yense wopacikidwa pamtengo.’” [Buku Lopatulika] (Agalatiya 3:13) Pamenepa Paulo anagwila mau a pa Deuteronomo 21:22, 23, amene amachula momveka bwino kwambili kuti mtengo, osati mtanda. Popeza kuti kunyongedwa kumeneko kunali kupangitsa munthu kukhala “wotembeleledwa,” sicingakhale coyenela kuti Akristu azikongoletsa manyumba ao ndi zifanizilo zoonetsa Kristu atapacikidwa.

Palibe umboni uliwonse woonetsa kuti pazaka 300 zoyambilila pambuyo pa imfa ya Kristu, anthu amene anali kudzicha kuti Akristu anali kugwilitsila nchito mtanda polambila. Komabe, m’zaka za m’ma 300, Mfumu Konstantine amene anali wacikunja, anatembenuka ndi kukhala Mkristu wampatuko, ndipo analimbikitsa Akristu kugwilitsila nchito mtanda monga cizindikilo cao. Kaya zolinga za Konstantine zinali zotani, panalibe mgwilizano uliwonse pakati pa mtanda ndi Yesu Kristu. Mfundo yeni-yeni ndi yakuti, mtanda unacokela ku zipembedzo zacikunja. Buku lina la Akatolika limavomeleza zimenezi kuti: “Mtanda umapezeka m’zipembedzo zimene zinaliko Cikristu cisanabwele, ndi m’zipembedzo zimene si zacikristu.” (New Catholic Encyclopedia) Mabuku enanso amanena kuti mtanda unali kugwilitsilidwa nchito ndi anthu olambila zacilengedwe, ndiponso anthu acikunja ocita miyambo ya zakugonana.

Nanga n’cifukwa ciani anthu anali kulimbikitsidwa kugwilitsila nchito cizindikilo cacikunja cimeneci ca mtanda? Anacita zimenezi pofuna kuti anthu akunja alandile “Cikristu” mosavuta. Komabe, Baibo siivomeleza kugwilitsila nchito cizindikilo ciliconse cacikunja polambila. (2 Akorinto 6:14-18) Malemba naonso samavomeleza mtundu uliwonse wa kupembedza mafano. (Ekisodo 20:4, 5; 1 Akorinto 10:14) Conco, pacifukwa comveka, Akristu oona samagwilitsila nchito mtanda polambila.a

a Kuti mudziŵe zambili za mtanda, onani buku lakuti Kukambitsirana za M’malemba, pamapeji 89 mpaka 93, lolembedwa ndi Mboni za Yehova.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani