NKHANI 3
Kodi Mulungu Ali Nalo Colinga Canji Dziko Lapansi?
Kodi colinga ca Mulungu kwa anthu n’ciani?
Kodi Mulungu anatsutsidwa bwanji?
Kodi umoyo padziko lapansi udzakhala bwanji mtsogolo?
1. Kodi Mulungu ali nalo colinga canji dziko lapansi?
COLINGA cimene Mulungu ali naco ndi dziko lapansi n’cokondweletsa kwambili. Yehova amafuna kuti anthu onse padziko lapansi akakhale acimwemwe ndi athanzi labwino. Baibo imakamba kuti Mulungu “anakonza munda ku Edeni,” ndipo “anameletsa . . . mtengo wamtundu uliwonse wooneka bwino ndi wa zipatso zabwino kudya.” Pamene Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi woyamba, Adamu ndi Hava, anawaika m’malo ao okongola ndi kuwauza kuti: “Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anile.” (Genesis 1:28; 2:8, 9, 15) Conco, cinali colinga ca Mulungu kuti anthu abeleke ana, akulitse munda wokongola umenewo mpaka kukafika kumalekezelo a dziko lapansi, ndi kuti azisamalila nyama.
2. (a) Kodi timadziŵa bwanji kuti colinga ca Mulungu ca dziko lapansi cidzakwanilitsidwa? (b) Monga mmene Baibo imakambila, kodi padziko lapansi padzakhala anthu otani?
2 Kodi inu muona kuti colinga ca Yehova Mulungu cakuti anthu akakhale m’paladaiso padziko lapansi cidzacitika zoona? Mulungu anakamba kuti, “ineyo ndalankhula ndipo ndidzazicita.” (Yesaya 46:9-11; 55:11) Zoona, Mulungu akakamba colinga cake, salephela kucikwanilitsa! Iye amakamba kuti “sanalilenge [dziko lapansi] popanda colinga,” koma “analiumba kuti anthu akhalemo.” (Yesaya 45:18) Kodi Mulungu anali kufuna kuti padziko lapansi pakhale anthu a mtundu wanji? Ndipo anafuna kuti akhalepo kwanthawi yaitali bwanji? Baibo imayankha kuti: “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29; Chivumbulutso 21:3, 4.
3. Kodi padziko lapansi masiku ano pali mavuto anji? Ndipo zimenezi zimabweletsa mafunso ati?
3 Zimenezi zikalibe kucitika. Pali pano anthu amadwala ndi kufa; amamenyana ndi kuphana. Mwacionekele, pali cimene cinasokonezeka. Kukamba zoona, Mulungu sanali kufuna kuti dziko lapansi likhale mmene timalionela! Nanga n’ciani cinasokonezeka maka-maka? N’cifukwa ciani colinga ca Mulungu sicinakwanilitsidwe? Palibe buku lililonse lolembedwa ndi munthu limene lingayankhe mafunso amenewa, cifukwa mavuto anayambila kumwamba.
MMENE MDANI ANAKHALILAKO
4, 5. (a) Kodi ndani maka-maka anakamba ndi Hava kupitila mwa njoka? (b) Kodi zingacitike bwanji kuti munthu amene kale anali wabwino ndi woona mtima akhale wakuba?
4 Buku loyamba m’Baibo limatiuza za wotsutsa Mulungu amene anaonekela m’munda wa Edeni. Limamuchula “njoka,” koma sanali njoka yeni-yeni. Buku lotsiliza la m’Baibo limamukamba kuti, “iye wochedwa Mdyelekezi ndi Satana, amene akusoceletsa dziko lonse lapansi.” Amachedwanso “njoka yakale ija.” (Genesis 3:1; Chivumbulutso 12:9) Mngelo wamphamvu ameneyu, kapena kuti colengedwa cauzimu cosaoneka, anagwilitsila nchito njoka kukamba ndi Hava. Anapangitsa mau ake kumveka monga anali kucokela kwa njoka. Munthu wauzimu ameneyu analiko pamene Mulungu anali kulenga dziko lapansi kuti anthu akhalepo.—Yobu 38:4, 7.
5 Popeza kuti zinthu zonse zimene Yehova analenga n’zangwilo, nanga ndani anapanga “Mdyelekezi,” kapena kuti “Satana”? Mwacidule, mmodzi wa ana amphamvu ndi auzimu a Mulungu, anadzisandutsa yekha kukhala Mdyelekezi. Kodi zinacitika bwanji zimenezi? Cabwino, tiyeni tikambe zimene zimacitika ngakhale masiku ano. Munthu amene poyamba anali wa makhalidwe abwino ndi woona mtima akhoza kusintha ndi kukhala wakuba. Kodi zimenezi zingacitike bwanji? Ngati munthu alola cikhumbo coipa kukula mumtima mwake, ndipo apitiliza kuciganizila nthawi zonse, cikhumbo coipa cimeneco cingakule ndi kukhala camphamvu kwambili. Ndiyeno ngati mpata ungapezeke, munthuyo angafike pa kucita cinthu coipa cimene wakhala akuganizila.—Yakobo 1:13-15.
6. Kodi zinacitika bwanji kuti mwana wauzimu ndi wamphamvu wa Mulungu akhale Satana Mdyelekezi?
6 Izi n’zimene zinacitika kwa Satana Mdyelekezi. Iye anamvela pamene Mulungu anauza Adamu ndi Hava kuti abale ana ndi kudzaza dziko lapansi. (Genesis 1:27, 28) Mwacionekele, Satana ayenela kuti anaganiza kuti, ‘anthu onse awa akhoza kumalambila ine m’malo molambila Mulungu!’ Conco, cikhumbo coipa cinakula mumtima mwake. Ndipo potsilizila pake, anacitapo kanthu mwa kuuza Hava zabodza ponena za Mulungu. (Genesis 3:1-5) Motelo, iye anakhala “Mdyelekezi,” kutanthauza “Woneneza.” Panthawi imodzi-modzi, anakhalanso “Satana,” kutanthauza “Wotsutsa.”
7. (a) N’cifukwa ciani Adamu ndi Hava anafa? (b) Nanga n’cifukwa ciani ana onse a Adamu amakalamba ndi kufa?
7 Mwa kugwilitsila nchito mabodza ndi macenjela, Satana Mdyelekezi anacititsa Adamu ndi Hava kusamvela Mulungu. (Genesis 2:17; 3:6) M’kupita kwa nthawi, io anafa, monga mmene Mulungu anakambila kuti adzafa ngati sadzamumvela. (Genesis 3:17-19) Cifukwa cakuti Adamu anakhala wopanda ungwilo pamene anacimwa, ana ake onse analandila ucimo kucokela kwa iye. (Aroma 5:12) Tingafanizile ndi mmene zimakhalila poumba nchelwa. Ngati cikombole ndi copindika, kodi nchelwa zotulukamo zimakhala bwanji? Nchelwa iliyonse imatuluka yopindika, kapena kuti yacilema. N’cimodzi-modzi ndi ife anthu. Aliyense anatengela “cilema” ca kupanda ungwilo kwa Adamu. Ndiye cifukwa cake anthu onse amakalamba ndi kufa.—Aroma 3:23.
8, 9. (a) Kodi Satana anatsutsa bwanji ulamulilo wa Mulungu? (b) N’cifukwa ciani Mulungu sanawaphe cabe opandukawo panthawi imeneyo?
8 Pamene Satana anacititsa Adamu ndi Hava kupandukila Mulungu, kweni-kweni iye anakhala mtsogoleli wacipanduko. Anatsutsa ulamulilo wa Yehova. M’njila ina tingati iye anakamba kuti: ‘Mulungu ndi wolamulila woipa. Amakamba zabodza ndipo amamana anthu ake zinthu zabwino. Anthu safunikila kulamulilidwa ndi Mulungu. Angadzisankhile okha cabwino ndi coipa. Ndipo angakhale ndi umoyo wabwino ine ndikayamba kuwalamulila.’ Koma kodi Mulungu akanacita bwanji ndi kutsutsa konyoza kumeneku? Anthu ena amaganiza kuti Mulungu anayenela kungowapha opandukawo panthawi imeneyo. Koma kodi zimenezo zikanapeleka yankho pa zimene Satana anatsutsa? Kodi zikanapeleka umboni wakuti Mulungu ndiye woyenela kulamulila?
9 Cilungamo ca Yehova sicikanamulola kupha apanduwo panthawi imeneyo. Iye anaona kuti panafunikila nthawi yokwanila yakuti ayankhe bwino zimene Satana anatsutsa, ndi kuti umboni uonekele wakuti Mdyelekezi ndi wabodza. Conco, Mulungu analola anthu kudzilamulila okha kwa kanthawi pansi pa uyang’anilo wa Satana. Mu Nkhani 11 ya buku lino tidzaphunzila za cifukwa cimene Yehova anacitila zimenezo, ndi cimene walolela nthawi yaitali conco akalibe kuthetsa nkhani imeneyi. Koma pali pano, ndi bwino kuganizila pa mafunso awa: Kodi Adamu ndi Hava anacita bwino kukhulupilila Satana, amene sanawacitilepo cinthu cabwino ciliconse? Kodi cinali cinthu cabwino kukhulupilila kuti Yehova, amene anawapatsa zonse zimene anali nazo, anali wabodza? Kodi inu mukanacita bwanji?
10. Kodi mungaonetse bwanji kuti muli kumbali ya Yehova pa zimene Satana anamutsutsa?
10 N’cinthu canzelu kuganizila mafunso amenewa cifukwa aliyense wa ife amakhudzidwa ndi nkhaniyo ngakhale masiku ano. Inde, inunso muli ndi mwai woonetsa kuti muli kumbali ya Yehova pa zimene Satana anatsutsa Yehova. Mungavomeleze kuti Yehova ndi Wolamulila wanu ndi kuthandizila kuonetsa kuti Satana ndi wabodza. (Salimo 73:28; Miyambo 27:11) Comvetsa cisoni n’cakuti, ndi anthu ocepa cabe padziko lapansi amene amacita zimenezi. Ndipo zimenezi zimabweletsa funso lina lofunika kwambili lakuti, Kodi Baibo imaphunzitsadi kuti Satana ndi amene alamulila dziko?
KODI NDANI AMENE ALAMULILA DZIKO?
Kodi Satana akanalonjeza kupatsa Yesu maufumu onse a padziko akanakhala kuti sanali ake?
11, 12. (a) Kodi kuyesedwa kwa Yesu kunaonetsa bwanji kuti Satana ndiye wolamulila wa dziko lino? (b) N’cianinso cimaonetsa kuti Satana ndi wolamulila wa dziko?
11 Yesu sanakaikile kuti Satana ndi amene alamulila dziko lino. Mwanjila inayake yozizwitsa, Satana anaonetsa Yesu “maufumu onse a padziko ndi ulemelelo wao.” Ndiyeno Satana analonjeza Yesu kuti: “Ndikupatsani zinthu zonsezi ngati mutangogwada pansi n’kundiŵelamila kamodzi kokha.” (Mateyu 4:8, 9; Luka 4:5, 6) Ganizilani zimenezi. Kodi cikanakhala ciyeso kwa Yesu kukanakhala kuti Satana sanali wolamulila maufumu amenewo? Yesu sanatsutse mfundo yakuti maboma onse a padziko lapansi anali a Satana. Kukamba zoona, kukanakhala kuti maboma amenewo sanali a Satana, Yesu akanam’tsutsa.
12 N’zoona kuti, Yehova ndi Mulungu Wamphamvuyonse, Mlengi wa cilengedwe conse. (Chivumbulutso 4:11) Komabe, Yesu ananena mwacindunji kuti Satana ndi “wolamulila wa dzikoli.” (Yohane 12:31; 14:30; 16:11) Ndiponso Baibo imachulanso Satana Mdyelekezi kuti ndi “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akorinto 4:3, 4) Ponena za wotsutsa ameneyu, kapena kuti Satana, Mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.
DZIKO LA SATANA LIDZACOTSEDWA
13. N’cifukwa ciani dziko latsopano likufunika?
13 Caka ciliconse cimene capita, dziko limangoipila-ipila. Ladzala ndi nkhondo, andale za dziko osaona mtima, abusa acipembedzo acinyengo, ndi zigawenga. Tsopano dziko lafika posakonzeka. Baibo imaonetsa kuti nthawi ili pafupi pamene Mulungu adzacotsapo dziko loipa limeneli pankhondo yake ya Aramagedo. Zimenezi zidzatsegulila njila dziko latsopano lolungama.—Chivumbulutso 16:14-16.
14. Kodi Mulungu anasankha ndani kukhala Mfumu ya Ufumu wake? Ndipo ulosi unanenelatu ciani pa zimenezi?
14 Yehova Mulungu adzagwilitsila nchito boma lake la kumwamba kucotsapo maboma a padziko lapansi. Baibo imacha boma limeneli kuti Ufumu wa Mulungu. Bomali n’limene Yesu anaphunzitsa otsatila ake kupemphelela kuti: “Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzi-modzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Mulungu anasankha Yesu Kristu kukhala Mfumu ya Ufumu wake wakumwamba. Kale kwambili, Baibo inalosela kuti: “Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamulilo udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamucha dzina lake . . . Kalonga wa mtendele. Za kuenjezela ulamulilo wake, ndi za mtendele sizidzatha.” (Yesaya 9:6, 7, Buku Lopatulika) Monga mmene tidzaonela m’nkhani za kutsogolo m’buku lino, posacedwa Ufumu wa Mulungu udzacotsapo maboma onse a padziko lapansi, ndipo Ufumu wa Mulungu udzaloŵa m’malo maboma onse amenewa. (Danieli 2:44) Pamenepo Ufumu wa Mulungu udzabweletsa paladaiso padziko lapansi.
DZIKO LATSOPANO LILI PAFUPI!
15. Kodi “dziko lapansi latsopano” n’ciani?
15 Baibo imatitsimikizila kuti: “Pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezela mogwilizana ndi lonjezo lake [Mulungu], ndipo mmenemo mudzakhala cilungamo.” (2 Petulo 3:13; Yesaya 65:17) Nthawi zina Baibo ikamakamba za “dziko lapansi,” imatanthauza anthu amene amakhala padziko lapansi. (Genesis 11:1, Buku Lopatulika) Conco, “dziko lapansi latsopano” lolungama limatanthauza anthu olandilidwa ndi Mulungu.
16. Kodi anthu oyanjidwa ndi Mulungu adzalandila mphatso yanji ya mtengo wapatali? Nanga tiyenela kucita ciani kuti tikalandile mphatso imeneyo?
16 Yesu analonjeza kuti, anthu oyanjidwa ndi Mulungu adzalandila mphatso ya “moyo wosatha” m’dziko latsopano limene lidzabwela. (Maliko 10:30) Tsegulani Baibo yanu pa Yohane 3:16 ndi pa Yohane 17:3, kuti muŵelenge zimene Yesu anakamba kuti tiyenela kucita kuti tikalandile moyo wosatha. Tsopano tiyeni tione madalitso ochulidwa m’Baibo amene anthu olandilidwa ndi Mulungu adzalandila m’dziko latsopano la Paladaiso limene lidzabwela.
17, 18. N’cifukwa ciani tiyenela kukhulupilila kuti padziko lonse lapansi padzakhala mtendele ndi cisungiko?
17 Zoipa zonse, nkhondo, upandu, ndi ciwawa zidzatha. “Woipa sadzakhalakonso . . . Koma anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi.” (Salimo 37:10, 11) Padzakhala mtendele cifukwa cakuti Mulungu ‘adzaletsa nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.’ (Salimo 46:9; Yesaya 2:4) Pamenepo, “masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendele woculuka, kufikila sipadzakhala mwezi”—kutanthauza kwamuyaya!—Salimo 72:7, Buku Lopatulika.
18 Alambili a Yehova adzakhala m’cisungiko. Nthawi zonse pamene Aisiraeli anali kumvela malamulo a Mulungu, anali kukhala m’cisungiko. (Levitiko 25:18, 19) Cidzakhala cinthu cokondweletsa kwambili, kukhala m’cisungiko ca Mulungu m’Paladaiso.—Yesaya 32:18; Mika 4:4.
19. Timadziŵa bwanji kuti m’dziko latsopano la Mulungu simudzakhala njala?
19 Sikudzakhala njala. Wamasalimo anaimba kuti: “Padziko lapansi padzakhala tiligu wambili. Pamwamba pa mapili padzakhala tiligu woculuka.” (Salimo 72:16) Yehova Mulungu adzadalitsa olungama ake, ndipo “dziko lapansi lidzapeleka zipatso zake.”—Salimo 67:6.
20. N’cifukwa ciani tiyenela kukhulupilila kuti dziko lonse lapansi lidzakhala paladaiso?
20 Dziko lonse lapansi lidzakhala paladaiso. Malo amene anthu oipa anaononga adzakhala okongola, ndipo malo amenewo adzakhala ndi manyumba atsopano abwino. (Yesaya 65:21-24; Chivumbulutso 11:18) M’kupita kwanthawi, malo amene kuli kale anthu adzafutukulidwa mpaka kumalekezelo a dziko lapansi. Ndipo dziko lonse lidzakhala lokongola ndi lobala zipatso, monga mmene munda wa Edeni unalili. Inde, Mulungu sadzalephela ‘kutambasula dzanja lake ndi kukhutilitsa zokhumba za camoyo ciliconse.’—Salimo 145:16.
21. N’ciani cionetsa kuti anthu adzakhala pamtendele ndi nyama?
21 Anthu adzakhala pamtendele ndi nyama. Nyama zakuthengo ndi nyama zoweta zidzadyela pamodzi. Ngakhale mwana wamng’ono sadzaopa nyama zimene pali pano ndi zoopsa.—Yesaya 11:6-9; 65:25.
22. N’ciani cidzacitika ndi matenda?
22 Matenda adzathelatu. Monga Mfumu ya Ufumu wa Kumwamba, Yesu adzacilitsa matenda kupambana mmene anacitila pamene anali padziko lapansi. (Mateyu 9:35; Maliko 1:40-42; Yohane 5:5-9) Panthawi imeneyo, “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanena kuti: ‘Ndikudwala’”—Yesaya 33:24; 35:5, 6.
23. Kodi Baibo imatipatsa ciyembekezo canji cokondweletsa ponena za okondedwa athu amene anafa?
23 Okondedwa athu amene anafa adzaukitsidwa. Ngati io adzamvela Mulungu, sadzafanso. Anthu onse akufa amene ali m’cikumbukilo ca Mulungu adzaukitsidwa. Kumeneku “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”—Machitidwe 24:15; Yohane 5:28, 29.
24. Kodi mumamva bwanji mukaganiza za kukhala m’Paladaiso padziko lapansi?
24 Anthu amene amasankha kuphunzila za Mlengi wathu Wamkulu, Yehova Mulungu, ndi kumutumikila, amakhala ndi tsogolo labwino kwambili. Paladaiso amene akubwela mtsogolo ndi amene Yesu anali kukambapo pamene analonjeza munthu woipa amene anapacikidwa pambali pake kuti: “Iwe udzakhala ndi ine m’Paladaiso.” (Luka 23:43) N’cinthu cofunika kwambili kuti tidziŵe zambili ponena za Yesu Kristu, cifukwa madalitso onse amenewa adzabwela kupitila mwa iye.