GAO 7
Kodi Yesu Anali Ndani?
Yehova anatumiza Yesu padziko lapansi. 1 Yohane 4:9
Ngati tifuna kukondweletsa Yehova, pali wina amene tifunika kumvetsela kwa iye. Kale kwambili Yehova akalibe kulenga Adamu, analenga mngelo wamphamvu kumwamba.
M’kupita kwa nthawi, Yehova anamutumiza kuti akabadwile ku Betelehemu kwa namwali, Mariya. Mwanayo anam’patsa dzina lakuti Yesu.—Yohane 6:38.
Pamene Yesu anali munthu padziko lapansi, anaonetsa bwino-bwino makhalidwe a Mulungu. Anali wokoma mtima, wacikondi, ndi wokonda kuceza ndi anthu. Sanaope kuphunzitsa anthu coonadi ca Yehova.
Yesu anacita zabwino koma anthu anam’zonda. 1 Petulo 2:21-24
Yesu anali kucilitsa odwala ndi kuukitsa anthu ena amene anafa.
Akulu-akulu acipembedzo anazonda Yesu cifukwa iye anali kuulula kuti ziphunzitso zawo ni zabodza ndi kuti makhalidwe awo ni oipa.
Akulu-akulu acipembedzo anasonkhezela Aroma kuti amenye Yesu ndi kumupha.