NKHANI 4
Kodi Yesu Kristu Ndani?
Kodi Yesu ali ndi udindo wanji wapadela?
Kodi iye anacokela kuti?
Kodi anali ndi umunthu wabwanji?
1, 2. (a) N’cifukwa ciani kungodziŵa dzina cabe la munthu wochuka sikutanthauza kuti mumam’dziŵa bwino? (b) Kodi anthu ali ndi maganizo osiyana-siyana ati ponena za Yesu?
PADZIKO lapansi pali anthu ambili ochuka. Ena ndi odziŵika kwambili m’dela lao, mu mzinda wao, kapena m’dziko lao. Ndipo ena amadziŵika dziko lonse. Koma, kungodziŵa cabe dzina la munthu wochuka sikutanthauza kuti mumam’dziŵa bwino munthu ameneyo. Sindiye kuti mumadziŵa zambili za mmene munthuyo anakulila ndi umunthu wake.
2 Anthu ambili padziko lapansi amvapo za Yesu Kristu, ngakhale kuti iye anakhalapo zaka pafupi-fupi 2,000 zapitazo. Ngakhale zili conco, anthu ambili sadziŵa kuti Yesu anali munthu wanji kweni-kweni. Ena amakamba kuti anali cabe munthu wabwino mtima. Ena amati anali mneneli. Ndipo ena amakhulupilila kuti Yesu ndi Mulungu ndipo ayenela kulambilidwa. Kodi tiyenela kumulambila?
3. N’cifukwa ciani kuli kofunika kuti mudziŵe coonadi ponena za Yesu?
3 N’kofunika kwambili kuti mudziŵe coonadi ponena za Yesu. N’cifukwa ciani kuli kofunika? Cifukwa Baibo imati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Kristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Inde, kudziŵa coonadi ponena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu kungatitsogolele ku moyo wosatha m’paladaiso padziko lapansi. (Yohane 14:6) Ndiponso, Yesu anapeleka citsanzo cabwino kwambili ca mmene tiyenela kukhalila ndi anthu anzathu. (Yohane 13:34, 35) M’nkhani yoyamba ya buku lino, tinaphunzila coonadi ponena za Mulungu. Tsopano tiyeni tione zimene Baibo imaphunzitsa m’ceni-ceni ponena za Yesu Kristu.
MESIYA WOLONJEZEDWA
4. Kodi maina audindo akuti “Mesiya” ndi “Kristu” amatanthauza ciani?
4 Kale kwambili, Yesu akalibe kubadwa, Baibo inakambilatu kuti Mulungu adzatumiza munthu amene adzakhala Mesiya, kapena kuti Kristu. Maina audindo akuti “Mesiya” (locokela ku Ciheberi), ndi “Kristu” (locokela ku Cigiriki), onse amatanthauza “Wodzozedwa.” Munthu wolonjezedwa ameneyo anayenela kudzozedwa, kutanthauza kuti, Mulungu anali kudzam’patsa udindo wapadela. Mu nkhani zakutsogolo m’buku lino, tidzaphunzila zambili za mbali yofunika imene Mesiya akucita pa kukwanilitsidwa kwa malonjezo a Mulungu. Tidzaphunzilanso za madalitso amene tingapeze kwa Yesu ngakhale panthawi ino. Komabe Yesu asanabadwe, anthu ambili anali kufunsa kuti, ‘Kodi ndani adzabwela monga Mesiya?’
5. Kodi ophunzila a Yesu anali otsimikiza ndi mtima wonse za ciani ponena za iye?
5 M’nthawi ya Yesu, ophunzila ake anali otsimikiza ndi mtima wonse kuti iye ndiye anali Mesiya wolonjezedwa. (Yohane 1:41) Mmodzi wa ophunzila a Yesu, dzina lake Simoni Petulo, anauza Yesu poyela kuti: “Ndinu Kristu.” (Mateyu 16:16) Koma kodi ophunzila a Yesu amenewo anatsimikizila bwanji kuti Yesu analidi Mesiya wolonjezedwa? Nanga ife tingatsimikize bwanji zimenezi?
6. Pelekani fanizo la mmene Yehova wathandizila anthu okhulupilika kuti azindikile Mesiya.
6 Aneneli a Mulungu amene anakhalako Yesu asanabadwe anakambilatu zinthu zambili ponena za Mesiya. Zinthu zimene ananenelatu zinathandiza kuti anthu ena amuzindikile. Tiyeni tifanizile conco: Tinene kuti akupemphani kupita ku siteshoni ya basi kapena ya sitima, kuti mukacingamile mlendo amene simunaonanepo naye. Kodi sizingakuthandizeni ngati munthu wina angakufotokozeleni zina ndi zina za mmene munthuyo amaonekela? Mofananamo, Yehova kupitila mwa aneneli ake, anafotokoza zimene Mesiya anali kudzacita ndi zimene zinali kudzam’citikila. Kukwanilitsika kwa maulosi ambili amenewa kunali kudzathandiza anthu okhulupilika kuti amuzindikile bwino.
7. Kodi ndi maulosi aŵili ati, mwa ena, onena za Yesu amene anakwanilitsika?
7 Tiyeni tione zitsanzo ziŵili cabe. Coyamba, mneneli Mika ananenelatu kukali zaka zoposa 700 kuti munthu wolonjezedwa ameneyu adzabadwila ku Betelehemu, umene unali mzinda waung’ono m’dziko la Yuda. (Mika 5:2) Kodi Yesu anabadwila kuti? Mu mzinda waung’ono umenewo! (Mateyu 2:1, 3-9) Caciŵili, kukali zaka mazana ambili, Danieli analemba ulosi wa pa Danieli 9:25 umene unachula caka ceni-ceni cimene Mesiya anayenela kuonekela. Caka cimeneco cinali 29 C.E.a Kukwanilitsika kwa maulosi amenewa ndi ena, kumatsimikizila kuti Yesu analidi Mesiya wolonjezedwa.
Pa ubatizo wake, Yesu anakhala Mesiya, kapena Kristu
8, 9. Kodi ndi umboni uti umene unaonekela pa ubatizo wa Yesu wotsimikizila kuti anali Mesiya?
8 Umboni wina woonetsa kuti Yesu anali Mesiya unaonekela bwino cakumapeto kwa caka ca 29 C.E. M’caka cimeneci Yesu anapita kwa Yohane Mbatizi kuti akam’batize mumtsinje wa Yorodano. Yehova anali atalonjeza Yohane kuti adzamuonetsa cizindikilo com’thandiza kudziŵa Mesiya. Yohane anaona cizindikilo cimeneco pa ubatizo wa Yesu. Baibo imakamba kuti zimene zinacitika ndi izi: ‘Atabatizidwa, nthawi yomweyo Yesu anavuuka m’madzimo. Pamenepo kumwamba kunatseguka, ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda ndi kutela pa iye. Panamvekanso mau ocokela kumwamba onena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwela naye.”’ (Mateyu 3:16, 17) Pamene Yohane anaona cizindikilo ca nkhunda ndi kumva mau amenewa, sanakaikile ngakhale pang’ono kuti Yesu anatumidwa ndi Mulungu. (Yohane 1:32-34) Panthawi imene Mulungu anathila mzimu wake pa Yesu, kapena kuti mphamvu yake yogwila nchito, m’pamene Yesu anakhala Mesiya, kapena kuti Kristu, wosankhidwa kukhala Mtsogoleli ndi Mfumu.—Yesaya 55:4.
9 Kukwanilitsika kwa maulosi a m’Baibo ndiponso umboni wopelekedwa ndi Yehova Mulungu mwini wake, kumaonetsa kuti Yesu ndiye anali Mesiya wolonjezedwa. Koma Baibo imayankhanso mafunso ena aŵili ofunika ponena za Yesu Kristu akuti: Kodi iye anacokela kuti? Ndipo anali ndi umunthu wotani?
KODI YESU ANACOKELA KUTI?
10. Kodi Baibo imaphunzitsa ciani za Yesu akalibe kubwela padziko lapansi?
10 Baibo imaphunzitsa kuti Yesu anali kumwamba akalibe kubwela padziko lapansi. Mika analosela kuti Mesiya adzabadwila ku Betelehemu, ndipo anakamba kuti iye anakhalapo “kuyambila nthawi zoyambilila.” (Mika 5:2) Ngakhale Yesu mwini wake anakamba nthawi zambili kuti anali kumwamba akalibe kubadwa monga munthu padziko. (Yohane 3:13; 6:38, 62; 17:4, 5) Pamene Yesu anali kumwamba, anali pa mgwilizano wapadela ndi Yehova.
11. Kodi Baibo imaonetsa bwanji kuti Yesu ndiye mwana wa Yehova wapamtima?
11 Pa zifukwa zabwino, Yesu ndi Mwana wa Yehova wapamtima. Iye amachedwa kuti “woyamba kubadwa wa cilengedwe conse,” cifukwa cakuti anali woyambilila kulengedwa ndi Mulungu.b (Akolose 1:15) Cifukwa cina cimene Mwana ameneyu alili wapadela n’cakuti iye ndi “Mwana wake wobadwa yekha.” (Yohane 3:16) Zimenezi zitanthauza kuti ndi Yesu yekha amene analengedwa mwacindunji ndi Mulungu. Cifukwa cinanso n’cakuti Yesu ndi yekha cabe amene Mulungu anagwilitsila nchito kulenga zinthu zina zonse. (Akolose 1:16) Komanso cifukwa cina n’cakuti, Yesu amachedwa kuti “Mau.” (Yohane 1:14) Izi zimationetsa kuti iye anali wolankhulila Mulungu, kutanthauza kuti ndiye anali kupeleka mauthenga ndi malangizo kwa ana ena a Mulungu, ponse paŵili, auzimu ndi aumunthu.
12. Timadziŵa bwanji kuti Mwana woyamba ameneyu salingana ndi Mulungu?
12 Kodi Mwana woyamba kubadwa ameneyu ndi wolingana ndi Mulungu, monga mmene anthu ena amakhulupilila? Baibo siphunzitsa zimenezi. Monga mmene taonela m’ndime 11, Mwana ameneyu anacita kulengedwa. Zimenezi zionetselatu kuti iye anali ndi ciyambi, koma Yehova Mulungu alibe ciyambi kapena mapeto. (Salimo 90:2) Mwana wobadwa yekha ameneyu sanayesepo ngakhale kuganiza cabe za kukhala wolingana ndi Atate wake. Baibo imaphunzitsa momveka bwino kuti Atate ndi wamkulu kuposa mwana ameneyu. (Yohane 14:28; 1 Akorinto 11:3) Yehova yekha ndiye “Mulungu Wamphamvuyonse.” (Genesis 17:1) Conco iye alibe wolingana naye.c
13. Kodi Baibo imatanthauza ciani pamene ikamba za Mwanayo kuti ndi “cifanizilo ca Mulungu wosaonekayo”?
13 Yehova ndi Mwana wake ameneyu anali kale pamodzi mosangalala kwa zaka mabiliyoni ambili—kale kwambili akalibe kulenga nyenyezi zakumwamba ndi dziko lapansi. Kunena zoona, io anali kukondana kwambili! (Yohane 3:35; 14:31) Mwana wapamtima ameneyu anali wofanana ndi Atate wake m’kacitidwe ka zinthu. Ndiye cifukwa cake Baibo imakamba kuti Mwana ameneyu ndi “cifanizilo ca Mulungu wosaonekayo.” (Akolose 1:15) Inde, monga mmene mwana angatengele makhalidwe ndi maonekedwe a atate wake, Yesu nayenso anaonetsa makhalidwe ndi maganizo a atate wake.
14. Kodi mwana wobadwa yekha wa Yehova anadzabadwa bwanji monga munthu?
14 Mwana wobadwa yekha wa Yehova ameneyu anavomela ndi mtima wonse kucoka kumwamba ndi kubwela padziko lapansi kudzakhala ndi moyo monga munthu. Mwina mungadabwe kuti, ‘Kodi zinatheka bwanji kuti colengedwa cauzimu cidzabadwe monga munthu?’ Yehova anacita zimenezi m’njila ya cozizwitsa. Iye anasamutsa moyo wa Mwana wake kumwamba n’kuuika m’mimba mwa namwali waciyuda Mariya padziko lapansi. Conco, Mariya anakhala ndi mimba popanda mwamuna. Ndiye cifukwa cake Mariya anabeleka mwana wamwamuna wangwilo, ndipo anamucha kuti Yesu.—Luka 1:30-35.
KODI YESU ANALI NDI UMUNTHU WOTANI?
15. N’cifukwa ciani tingakambe kuti kupitila mwa Yesu timam’dziŵa bwino Yehova?
15 Zimene Yesu anakamba ndi zimene anacita pamene anali padziko lapansi zimatithandiza kuti tim’dziŵe bwino. Komanso, kupitila mwa Yesu timam’dziŵanso bwino Yehova. Kodi timam’dziŵa bwanji kupyolela mwa Yesu? Kumbukilani kuti Mwana ameneyu ndi cifanizilo ceni-ceni ca Atate wake. Ndiye cifukwa cake Yesu anauza mmodzi wa ophunzila ake kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yohane 14:9) Mabuku anai a m’Baibo ochedwa Mauthenga Abwino amene ndi Mateyu, Maliko, Luka, ndi Yohane, amatiuza zambili ponena za umoyo wa Yesu Kristu, nchito yake, ndi makhalidwe ake.
16. Kodi uthenga wa Yesu unali wonena za ciani maka-maka? Nanga zimene anali kuphunzitsa zinacokela kuti?
16 Yesu anali kudziŵika bwino monga “Mphunzitsi.” (Yohane 1:38; 13:13) Kodi anali kuphunzitsa za ciani? Iye maka-maka, anali kuphunzitsa za “uthenga wabwino wa ufumu” wa Mulungu. Ufumu umenewu ndi boma lakumwamba limene lidzalamulila padziko lonse lapansi, ndi kubweletsa madalitso osaneneka kwa anthu omvela. (Mateyu 4:23) Kodi uthenga umenewu unacokela kwa ndani? Yesu mwini wake anakamba kuti: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga ayi, koma ndi za amene anandituma,” kutanthauza Yehova. (Yohane 7:16) Yesu anadziŵa kuti Atate wake amafuna kuti anthu amve za uthenga wabwino wa Ufumu. M’nkhani 8, tidzaphunzila zambili za Ufumu wa Mulungu ndi zimene udzacita.
17. Kodi Yesu anali kuphunzitsa kuti? N’cifukwa ciani anali wodzipeleka kwambili pa kuphunzitsa ena?
17 Kodi Yesu anali kuphunzitsa kuti? Kulikonse kumene anapeza anthu—m’madela a kumidzi, m’mizinda, m’misika, ndi m’manyumba a anthu. Yesu sanali kuyembekezela anthu kuti azibwela kwa iye. M’malo mwake, iye ndi amene anali kulondola anthu. (Maliko 6:56; Luka 19:5, 6) Koma n’cifukwa ciani Yesu anali wodzipeleka conco ndi kutaila nthawi yake yambili pa kulalikila ndi kuphunzitsa? N’cifukwa cakuti, kwa iye kucita zimenezi kunali kucita cifunilo ca Mulungu. Yesu anali kucita cifunilo ca Atate wake nthawi zonse. (Yohane 8:28, 29) Koma panalinso cifukwa cina cimene iye anali kulalikilila. Cinali cifundo cimene anali naco kwa anthu amene anali kubwela kwa iye. (Mateyu 9:35, 36) Anthu amenewo anali onyalanyazidwa ndi abusa ao acipembedzo, amene anayenela kuwaphunzitsa coonadi conena za Mulungu ndi colinga cake. Yesu anadziŵa kuti kunali kofunika kuti anthu amve uthenga wa Ufumu.
18. Kodi ndi makhalidwe ati a Yesu amene amakukondweletsani?
18 Yesu anali munthu wacikondi amene anali kusamalila za anthu ena. Mwa ici, anthu ena anamuona kukhala wofikilika ndi wokoma mtima. Ngakhale tuŵana tunali kumva bwino kukhala naye. (Maliko 10:13-16) Yesu analibe tsankho. Iye anali kudana ndi cinyengo ndi kupanda cilungamo. (Mateyu 21:12, 13) Ngakhale panthawi imene akazi sanali kupatsidwa ulemu kweni-kweni, ndipo anali ndi ufulu wocepa, Yesu anali kuwacitila mwaulemu. (Yohane 4:9, 27) Yesu anali wodzicepetsa m’ceni-ceni. Panthawi ina, anasambitsa mapazi a atumwi ake, nchito imene nthawi zambili inali kucitidwa ndi kapolo.
Yesu analalikila kulikonse kumene anapeza anthu
19. Kodi n’citsanzo citi cimene cionetsa kuti Yesu anali kuzindikila zosoŵa za anthu ena?
19 Yesu anali kuzindikila zosoŵa za anthu ena. Izi zinaonekela maka-maka pamene anacilitsa anthu mozizwitsa mwa mphamvu ya mzimu woyela wa Mulungu. (Mateyu 14:14) Mwacitsanzo, munthu wakhate anabwela kwa Yesu ndi kunena kuti: “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeletsa.” Yesu anamva ngati kuti nayenso akumva ululu ndi kuvutika kwa munthu ameneyu. Pakumva cifundo, Yesu anatambasula dzanja lake ndi kugwila munthu ameneyu, ndi kumuuza kuti: “Ndikufuna. Khala woyela.” Ndipo munthu wakhate ameneyo anacila. (Maliko 1:40-42) Ganizilani cabe mmene munthuyo anamvelela!
ANAKHULUPILIKA MPAKA IMFA
20, 21. Kodi Yesu anapeleka citsanzo canji pa kukhala wokhulupilika kwa Mulungu?
20 Yesu anapeleka citsanzo cabwino kwambili ca kukhulupilika kwa Mulungu. Anakhalabe wokhulupilika kwa Atate wake wakumwamba m’mikhalidwe yosiyana-siyana, potsutsidwa ndi anthu osiyana-osiyana, ndi pokumana ndi zovuta zosiyana-siyana. Iye anakwanitsa kulimbana ndi ziyeso zonse za Satana. (Mateyu 4:1-11) Panthawi ina, ena mwa acibale ake eni-eni sanakhulupilile mwa iye, cakuti anafika ponena kuti “wacita misala.” (Maliko 3:21) Koma Yesu sanalole kuti io amufooketse, m’malo mwake anapitiliza kugwila nchito ya Mulungu. Ngakhale kuti adani ake anali kumunyoza ndi kumuvutitsa, Yesu anakhalabe wodziletsa, ndipo sanayese kuwabwezela m’njila iliyonse.—1 Petulo 2:21-23.
21 Yesu anakhalabe wokhulupilika mpaka imfa. Anacita kuphedwa mwankhanza ndi adani ake. (Afilipi 2:8) Ganizilani zimene anapilila patsiku lomaliza la umoyo wake monga munthu. Anam’manga, anamunamizila ndi umboni wabodza, oweluza acinyengo anam’patsa mlandu, magulu a anthu aciwawa anamuseka, ndipo asilikali anamuzunza. Pamene anakhomeledwa pamtengo, anapuma komaliza, ndi kulila kuti: “Ndakwanilitsa cifunilo canu!” (Yohane 19:30) Komabe, patsiku lacitatu pambuyo pa imfa yake, Atate wake wakumwamba anamuukitsa kukhala ndi moyo wauzimu. (1 Petulo 3:18) Patapita masiku 40, iye anabwelela kumwamba. Kumeneko, anakhala “pansi kudzanja lamanja la Mulungu” kuyembekezela kupatsidwa mphamvu zolamulila monga mfumu.—Aheberi 10:12, 13.
22. Kodi Yesu anatsegula mwai wanji pamene anakhala wokhulupilika mpaka imfa?
22 Kodi Yesu anatsegula mwai wanji pamene anakhala wokhulupilika mpaka imfa? Imfa ya Yesu m’ceni-ceni imatitsegulila mwai wodzakhala ndi moyo wamuyaya m’paladaiso padziko lapansi, mogwilizana ndi colinga ca Yehova ca poyambilila. M’nkhani yotsatila tidzakambitsilana mmene imfa ya Yesu imatsegulila mwai umenewu.
a Kuti mumve zambili za ulosi wa Danieli umene unakwanilitsika mwa Yesu, onani Zakumapeto, pamapeji 198 mpaka 199.
b Yehova amachedwa kuti Atate cifukwa iye ndiye Mlengi. (Yesaya 64:8) Popeza kuti Yesu analengedwa ndi Mulungu, amachedwa Mwana wa Mulungu. Pa cifukwa cimodzi-modzi, zolengedwa zinanso zauzimu zimachedwa ana a Mulungu. Koma Adamu nayenso amachedwa mwana wa Mulungu.—Yobu 1:6; Luka 3:38.
c Kuti muone umboni wina wakuti Mwana woyamba ameneyu salingana ndi Mulungu, onani Zakumapeto, pamapeji 201 mpaka 204.