LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bhs nkhani 207-223
  • Mfundo za Kumapeto

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mfundo za Kumapeto
  • Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • 20 PEMPHELO LA AMBUYE
  • Gwilitsilani Nchito Mphamvu ya Mau a Mulungu mu Ulaliki
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Zimene Ulosi wa Danieli Unakambilatu za Kufika kwa Mesiya
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
bhs nkhani 207-223

MFUNDO ZA KUMAPETO

1 YEHOVA

Dzina la Mulungu ni Yehova, ndipo limatanthauza kuti “Amakwanitsa Kucita Ciliconse.” Yehova ni Mulungu Wamphamvuzonse, ndipo ndiye analenga zinthu zonse. Iye ali ndi mphamvu zocita ciliconse cimene afuna.

Mu Ciheberi, dzina la Mulungu anali kulilemba ndi zilembo zinayi. Zilembo zimenezo kuzilemba m’Cinyanja ni YHWH kapena JHVH. Dzina la Mulungu limapezeka m’mipukutu yoyambilila ya Malemba a m’Baibulo a m’Ciheberi. Limapezekamo pafupifupi nthawi 7,000. Zungulile dziko lapansi, anthu amalemba dzina limeneli mosiyana-siyana, ndipo amalichula mogwilizana ndi cinenelo cawo.

▸ Nkhani 1, ndime 15

2 BAIBULO ‘INAUZILIDWA NDI MULUNGU’

Mlembi weni-weni wa Baibulo ni Mulungu, koma anagwilitsila nchito anthu monga akalembela ake. Cili ngati mmene ambuye angauzile mdzukulu wawo kuti awalembele kalata, akumamuuza mau olemba. Yehova anaseŵenzetsa mzimu woyela kutsogolela anthu kuti alembe maganizo ake m’Baibulo. Mzimu wa Mulungu unawatsogolela m’njila zambili. Nthawi zina anali kuona masomphenya kapena maloto basi n’kumalemba zimene anali kuona kapena kumva.

▸ Nkhani 2, ndime 5

3 MFUNDO ZA M’BAIBULO

Izi ni ziphunzitso za m’Baibulo zimene zimafotokoza mfundo zoona. Mwacitsanzo, mfundo yakuti “kugwilizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino,” imatiphunzitsa kuti anthu amene timagwilizana nawo angatithandize kapena angatiwononge. (1 Akorinto 15:33) Ndipo mfundo yakuti “ciliconse cimene munthu wafesa adzakololanso comweco,” imatiphunzitsa kuti tikacita zinazake, tidziŵe kuti zotulukapo zake zidzatipeza.—Agalatiya 6:7.

▸ Nkhani 2, ndime 12

4 ULOSI

Ulosi ni uthenga wocokela kwa Mulungu. Uthenga umenewo ungakhale wofotokoza cifunilo ca Mulungu, wophunzitsa khalidwe labwino, wopeleka lamulo, kapena wa ciweluzo. Ulosi ungakhalenso uthenga wa zimene zidzacitika mtsogolo. M’Baibulo muli maulosi ambili amene anakwanilitsika kale.

▸ Nkhani 2, ndime 13

5 MAULOSI OKAMBA ZA MESIYA

Maulosi ambili a m’Baibulo okamba za Mesiya anakwanilitsika pa Yesu. Onani danga lakuti “Maulosi Okamba za Mesiya.”

▸ Nkhani 2, ndime 17, mau amunsi. 

MAULOSI OKAMBA ZA MESIYA

COCITIKA

ULOSI

KUKWANILITSIKA

Anabadwila m’fuko la Yuda

Genesis 49:10

Luka 3:23-33

Anabadwa kwa namwali

Yesaya 7:14

Mateyu 1:18-25

Mbadwa ya Mfumu Davide

Yesaya 9:7

Mateyu 1:1, 6-17

Yehova analengeza kuti Yesu ni mwana wake

Salimo 2:7

Mateyu 3:17

Ambili sanakhulupilile kuti Yesu ni Mesiya

Yesaya 53:1

Yohane 12:37, 38

Analoŵa mu Yerusalemu atakwela pa bulu

Zekariya 9:9

Mateyu 21:1-9

Anapelekedwa ndi mnzake wa pamtima

Salimo 41:9

Yohane 13:18, 21-30

Anapelekedwa ndi ndalama 30 za siliva

Zekariya 11:12

Mateyu 26:14-16

Pomuimba mlandu sanayankhe ciliconse

Yesaya 53:7

Mateyu 27:11-14

Anacita maele pa zovala zake

Salimo 22:18

Mateyu 27:35

Ananyozedwa ali pa mtengo wozunzikilapo

Salimo 22:7, 8

Mateyu 27:39-43

Sanathyole fupa lake lililonse

Salimo 34:20

Yohane 19:33, 36

Anamuika m’manda pamodzi ndi anthu olemela

Yesaya 53:9

Mateyu 27:57-60

Anaukitsidwa

Salimo 16:10

Machitidwe 2:24, 27

Anaukitsidwa ndi kuyenda kumwamba kukakhala ku dzanja lamanja la Yehova

Salimo 110:1

Machitidwe 7:55, 56

6 CIFUNILO CA MULUNGU CA DZIKO LAPANSI

Yehova analenga dziko lapansi kuti likhale paladaiso, mudzi wokongola wa anthu amene amam’konda. Cifunilo cake sicinasinthe. Lomba apa, Mulungu adzacotsa zoipa zonse, ndi kupatsa anthu ake moyo wosatha.

▸ Nkhani 3, ndime 1

7 SATANA MDYELEKEZI

Satana ni mngelo amene anayambitsa cipanduko. Amacedwa Satana, kutanthauza “Wotsutsa,” cifukwa cakuti amatsutsa Yehova. Amacedwanso Mdyelekezi, kutanthauza “Woneneza.” Anapatsidwa dzina limeneli cifukwa amaneneza Mulungu ndi anthu ake zabodza.

▸ Nkhani 3, ndime 4

8 ANGELO

Kale kwambili, Yehova analenga angelo asanalenge dziko lapansi. Anawalenga kuti adzikhala kumwamba. Angelo alipo opitilila pa 100 miliyoni. (Danieli 7:10) Iwo ali ndi maina osiyana-siyana, ndi maumunthu osiyana-siyana. Popeza angelo ni okhulupilika ndi odzicepetsa, amakana kulambilidwa ndi anthu. Ali pa maudindo osiyana-siyana, ndipo amagwila nchito zosiyana-siyana. Nchito zawo zina ni kutumikila ku mpando wacifumu wa Yehova, kupeleka mauthenga a Mulungu, kucinjiliza ndi kutsogolela atumiki ake pa dziko lapansi, kupeleka ziweluzo za Mulungu, ndi kuthandizila pa nchito yolalikila. (Salimo 34:7; Chivumbulutso 14:6; 22:8, 9) Kutsogoloku, iwo adzamenya nkhondo ya Aramagedo pamodzi ndi Yesu.—Chivumbulutso 16:14, 16; 19:14, 15.

▸ Nkhani 3, ndime 5; Nkhani 10, ndime 1

9 UCIMO

Kodi ucimo n’ciani? Ciliconse cili m’maganizo mwathu, kapena cimene tingacite cotsutsana ndi Yehova kapena ndi cifunilo cake. Cifukwa ucimo umawononga unansi wathu ndi Mulungu, iye watipatsa malamulo ndi mfundo zotithandiza kuti tisacimwile dala. Pa ciyambi, zonse zimene Yehova analenga zinali zangwilo. Koma pamene Adamu ndi Hava anasankha kupandukila Mulungu, iwo anacimwa, ndipo anakhala opanda ungwilo. M’kupita kwa nthawi, anakalamba ndi kufa. Ndiye popeza ife tinatengela ucimo kwa Adamu, ifenso timakalamba ndi kufa.

▸ Nkhani 3, ndime 7; Nkhani 5, ndime 3

10 ARAMAGEDO

Imeneyi ni nkhondo ya Mulungu imene idzawononga dziko la Satana ndi kucotsa zoipa zonse.

▸ Nkhani 3, ndime13; Nkhani 8, ndime 18

11 UFUMU WA MULUNGU

Ufumu wa Mulungu ni boma limene Yehova anakhazikitsa kumwamba. Yesu Khiristu ndiye amene alamulila monga Mfumu. Posacedwa, Yehova adzagwilitsila nchito Ufumu umenewu kucotsapo zoipa zonse. Ndipo Ufumu wa Mulungu udzalamulila pa dziko lonse lapansi.

▸ Nkhani 3, ndime 14

12 YESU KHIRISTU

Mulungu analenga Yesu asanalenge cina ciliconse. Yehova anatumiza Yesu pa dziko lapansi kuti adzafele anthu onse. Yesu ataphedwa, Yehova anamuukitsa. Pano tikamba, Yesu alamulila kumwamba monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.

▸ Nkhani 4, ndime 2

13 ULOSI WA MAWIKI 70

Baibulo inalosela, kapena kukambilatu za nthawi pamene Mesiya adzaonekela. Nthawi imeneyo inali pamapeto pa nyengo yochedwa masabata 69 [kapena kuti mawiki 69], imene inayamba m’caka ca  455 B.C.E., ndi kutha mu 29 C.E.

Timadziŵa bwanji kuti nyengo imeneyi inatha mu 29 C.E.? Nyengo ya mawiki 69 imeneyi inayamba mu 455 B.C.E., pamene Nehemiya anafika ku Yerusalemu ndi kuyamba kumanganso mzinda umenewo. (Danieli 9:25; Nehemiya 2:1, 5-8) Tikamvela liwu lakuti “wiki” (sabata) nambala imabwela m’maganizo ni 7. Koma wiki (sabata) ya mu ulosi umenewu si wiki a masiku 7. Ni wiki ya zaka 7, malinga ndi kaŵelengedwe ka zaulosi kamene kamati “tsiku limodzi kuŵelengela caka cimodzi.” (Numeri 14:34; Ezekieli 4:6) Ici cikutanthauza kuti wiki imodzi ni ya utali wa zaka 7. Conco, mawiki 69 amakwana zaka  483 (69 x 7). Tikaŵelengetsa zaka 483 kucokela mu 455 B.C.E., zimatifikitsa mu 29 C.E. Cimeneci ndiye caka ceni-ceni cimene Yesu anabatizika ndi kukhala Mesiya.—Luka 3:1, 2, 21, 22.

Ulosi umenewo unachulanso za wiki inanso, kutanthauza zaka zina 7. Mkati mwa wiki imeneyi, m’cakaca 33 C.E., Mesiya anali kukaphedwa. Ndipo kuyambila m’caka ca 36 C.E., uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu unakalalikidwa, osati cabe kwa Ayuda, koma ku mitundu yonse.—Danieli 9:24-27.

▸ Nkhani 4, ndime 7

Chati: Ulosi wa mawiki 70 wa mu Danieli 9 umakamba za kufika kwa Mesiya

14 CIPHUNZITSO CONAMA CA ATATU MWA MULUNGU MMODZI

Baibulo imaphunzitsa kuti Yehova ndiye analenga zinthu zonse, koma coyamba analenga Yesu. (Akolose 1:15, 16) Yesu si Mulungu Wamphamvuzonse. Ngakhale mwiniwake sanakambepo kuti ni wolingana ndi Mulungu. Ndipo anacita kukamba kuti ‘Atate ni wamkulu kuposa ine.” (Yohane 14:28; 1 Akorinto 15:28) Koma zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti alimo atatu mwa Mulungu mmodzi. Amati mwa Mulungu mmodzi muli Atate, Mwana, ndi mzimu woyela. Koma ciphunzitso cimeneci n’cabodza, sicipezeka m’Baibulo.

Mzimu woyela ni mphamvu imene Mulungu amaseŵenzetsa pocita cifunilo cake. Mzimu ulibe thupi kapena maganizo. Ni mphamvu cabe. Mwacitsanzo, m’nthawi za atumwi, Akhiristu “anadzazidwa ndi mzimu woyela.” Ndipo Yehova anakamba kuti: “Ndidzatsanulila [kupungulila] mbali ya mzimu wanga pa anthu osiyana-siyana.”—Machitidwe 2:1-4, 17.

▸ Nkhani 4, ndime 12; Nkhani 15, ndime 17

15 MTANDA

Akhristu oona sagwilitsila nchito mtanda polambila Mulungu. N’cifukwa ciani?

  1. M’zipembedzo zonama, mtanda wakhala ukugwilitsilidwa nchito kwa nthawi yaitali kwambili. M’zaka zamakedzana, anali kugwilitsila nchito mtanda polambila zinthu za cilengedwe, ndi m’miyambo ya zakugonana. M’zaka 300 pambuyo pa imfa ya Khiristu, Akhiristu sanali kugwilitsila nchito mtanda polambila. Koma pambuyo pake, Mfumu ya ulamulilo wa Roma, Kositantini, anakhazikitsa mtanda kukhala cizindikilo ca Cikhiristu. Colinga cinali kukopela anthu ku machalichi a Cikhiristu. Ngakhale n’conco, panalibiletu mgwilizano uliwonse pakati pa mtanda ndi Yesu Khiristu. Buku ina ya Akatolika inati: “Anthu anali kugwilitsila nchito mtanda ngakhale Cikhiristu cisanabwele,  komanso umapezeka m’zikhalidwe za anthu amene si Akhiristu.”—New Catholic Encyclopedia.

  2.   Yesu sanafele pa mtanda. Liu la Cigiriki lomasulidwa kuti “mtanda,” kweni-kweni limatanthauza “mtengo woongoka,” “powo” kapena “mtengo cabe.” Baibulo yakuti The Companion Bible imati: M’Malemba a Cigiliki [a Cipangano Catsopano] mulibe mau alionse oonetsa kuti panali mitengo iŵili. Yesu anafela pa mtengo woongoka.

  3.  Yehova safuna kuti tiziseŵenzetsa mafano kapena zizindikilo zilizonse pom’lambila.—Ekisodo 20:4, 5; 1 Akorinto 10:14.

▸ Nkhani 5, ndime 12

16 CIKUMBUTSO

Yesu analamula ophunzila ake kuti azicita mwambo wokumbukila imfa yake. Iwo amacita mwambo umenewu caka ciliconse pa Nisani 14, pa tsiku limene Aisiraeli anali kucita mwambo wa Pasika. Pa mwambo umenewu pamakhala mkate ndi vinyo. Zizindikilo zimenezi zimaimila thupi ndi magazi a Yesu, ndipo amazipeleka kwa aliyense amene wapezekapo pa Cikumbutso. Amene amadya mkate ndi kumwa vinyo ni aja cabe amene adzalamulila pamodzi ndi Yesu kumwamba. Koma amene ali ndi ciyembekedzo codzakhala ndi moyo wosatha pa dziko lapansi, amapezeka koma samadyako mkate kapena kumwako vinyo.

▸ Nkhani 5, ndime 21

17 “AZIMU”

  • Anthu ambili amakhulupilila kuti munthu akamwalila mzimu wake umayenda kumalo a mizimu, imene amati ni mizimu ya makolo, kapena kuti “azimu.” Amakhulupililanso kuti azimu amenewo akhoza kuwathandiza kapena kuwacita zinthu zoipa.

  • Koma Baibulo siiphunzitsako zimenezi. M’malo mwake, imaphunzitsa momveka bwino kuti munthu akafa, sakhoza kucita cinthu ciliconse. Malemba amati: ‘Pakuti amoyo amadziŵa kuti adzafa, koma akufa sadziwa ciliconse. Cikondi cawo, cidani cawo ndiponso nsanje yawo zatha kale. Alibenso gawo mpaka kalekale pa ciliconse cimene cikucitika pa dziko lapansi pano.’ (Mlaliki 9:5, 6, 10) Baibulo imakambanso kuti munthu akafa, “amabwelela ku nthaka. Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimathelatu.”—Salimo 146:4; Genesis 3:19.

  • Coonadi n’cakuti, Baibulo siigwilizana ndi cikhulupililo cakuti azimu ni makolo athu amene anamwalila. Siiphunzitsanso kuti munthu akafa mzimu wake umacoka ndi kupitiliza kukakhala ndi moyo kwina kwake. Conco, akufa sangathandize amoyo m’njila iliyonse, ndipo sangawacite coipa ciliconse.

▸ Nkhani 6, ndime 5; Nkhani 15, ndime 17

18 MZIMU

Liu la Ciheberi ndi la Cigiriki limene anamasulila kuti “mzimu” mu Baibulo la Dziko Latsopano, lingatanthauze zinthu zosiyana-siyana. Koma nthawi zambili limatanthauza cinthu cosaoneka monga mphepo, kapena mpweya umene anthu ndi nyama amapuma. Lingatanthauzenso zamoyo zamzimu, kapenanso mzimu woyela umene Mulungu amaugwilitsila nchito. Baibulo siiphunzitsa kuti munthu ali ndi mzimu umene umacoka m’thupi lake akamwalila, ndi kukapitiliza ndi moyo kwinakwake.—Ekisodo 35:21; Salimo 104:29; Mateyu 12:43; Luka 11:13.

▸ Nkhani 6, ndime 5; Nkhani 15, ndime 17

19 GEHENA

Gehena ni dzina la cigwa cimene cinali pafupi ndi Yerusalemu, kumene anali kutailako zinyalala ndi kuwocha. Palibe umboni woonetsa kuti m’nthawi ya Yesu, nyama zamoyo kapena anthu amoyo anali kuponyedwa m’cigwa cimeneci monga cilango cawo. Conco, Gehena saimila malo osaoneka kumene mizimu ya anthu amene anamwalila imazunzidwa kwamuyaya m’moto. Pamene Yesu anachula za anthu amene amaponyedwa ku Gehena, iye anali kungotanthauza ciwonongeko cotheletu.—Mateyu 5:22; 10:28.

▸ Nkhani 7, ndime 20

20 PEMPHELO LA AMBUYE

Ili ni pemphelo limene Yesu anauza ophunzila ake powaphunzitsa kupemphela. Limadziŵikanso kuti pemphelo lakuti Atate Wathu, kapena pemphelo la citsanzo. Mwacitsanzo, Yesu anatiphunzitsa kupemphela kuti:

  • “Dzina lanu liyeletsedwe”

    Timapemphela kuti Yehova ayeletse dzina lake, kapena mbili yake ku mabodza onse. Izi n’zofunika kuti angelo onse kumwamba ndi anthu onse pa dziko lapansi azilemekeza dzina la Mulungu.

  • “Ufumu wanu ubwele”

    Timapempha kuti boma la Mulungu libwele kudzawononga dziko loipa la Satana, kuti likalamulile dziko lonse lapansi, ndi kuti likakonze dziko lapansi kukhala paradaiso.

  • “Cifunilo canu cicitike . . . pansi pano”

    Timapempha kuti cifunilo ca Mulungu cikwanilitsidwe pa dziko lapansi, kuti anthu omvela ndi angwilo akalandile moyo wosatha m’Paradaiso. N’cimene Yehova anali kufuna pamene analenga anthu.

▸ Nkhani 8, ndime 2

21 DIPO

Yehova anapeleka dipo kuti apulumutse anthu ku ucimo ndi imfa. Dipo ni malipilo amene anapelekedwa cifukwa ca moyo wangwilo umene munthu woyamba Adamu anataya, ndi kuyanjanitsanso anthu kwa Yehova. Mulungu anatumiza Yesu pa dziko lapansi kuti adzafele anthu onse ocimwa. Conco, mwa imfa ya Yesu, anthu onse ali ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wangwilo pa dziko lapansi.

▸ Nkhani 8 ndime 21; Nkhani 9, ndime 13

22 N’CIFUKWA NINJI CAKA CA 1914 N’COFUNIKA KWAMBILI?

Ulosi wa mu Danieli caputala 4 unakambilatu kuti Mulungu adzakhazikitsa Ufumu wake mu 1914.

Ulosi umenewo: Yehova analotetsa Mfumu Nebukadinezara maloto aulosi, a mtengo ukulu umene unadulidwa. M’maloto amenewo, citsa ca mtengowo anacimanga ndi mkombelo wacitsulo ndi wamkuwakuti mtengowo usaphuke mpaka “nthawi zokwanila 7” zitapita. Pambuyo pa nyengoyo, mtengowo udzaphukanso ndi kuyamba kukula.—Danieli 4:1, 10-16.

Mmene ulosi umenewu umatikhudzila: Mtengo umenewo umaimila ulamulilo wa Mulungu. Kwa zaka zambili, Yehova anali kugwilitsila nchito mafumu a ku Yerusalemu kulamulila mtundu wonse wa Aisiraeli. (1 Mbiri 29:23) Koma mafumuwo anakhala osakhulupilika, ndipo ulamulilo wawo unatha. Yerusalemu anawonongedwa mu 607 B.C.E. Ndiye panayambila nyengo ya “nthawi zokwanila 7.” (2 Mafumu 25:1, 8-10; Ezekieli 21:25-27) Pamene Yesu anakamba kuti, “anthu a mitundu ina adzapondaponda Yerusalemu, kufikila nthawi zoikidwilatu za anthu a mitundu inawo zitakwanila,” anali kutanthauza “nthawi zokwanila 7” zimenezo. (Luka 21:24) Conco, “nthawi zokwanila 7” sizinathe pamene Yesu anali pa dziko lapansi. Yehova analonjeza kuti adzasankha Mfumu kumapeto kwa “nthawi zokwanila 7” zimenezo. Ulamulilo wa Mfumu yatsopano imeneyi, Yesu, unali kukabweletsa madalitso osatha kwa anthu a Mulungu zungulile dziko lapansi.—Luka 1:30-33.

Utali wa “nthawi zokwanila 7”: “Nthawi zokwanila 7” zinali zaka  2,520. Tikaŵelenga zaka 2,520 kucokela mu 607 B.C.E., zimatifikitsa m’caka ca 1914. Ndiye caka cimene Yehova anaika Yesu, Mesiya, kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kumwamba.

Nanga ciŵelengelo ca 2,520 ticipeza bwanji? Baibulo imaonetsa kuti nthawi zitatu ndi hafu kweni-kweni ni masiku  1,260. (Chivumbulutso 12:6, 14) Motelo, “nthawi zokwanila 7” ni kuŵilikiza kaŵili ciŵelengelo cimeneco, kapena kuti masiku 2,520. Conco, masiku 2,520 ni zaka  2,520,  cifukwa kaŵelengedwe kaulosi kamatenga “tsiku limodzi kuimila caka cimodzi.”—Numeri 14:34; Ezekieli 4:6.

▸ Nkhani  8, ndime 23

Chati ya madeti ndi zocitika zokhudza loto la Nebukadinezara

23 MIKAYELI MKULU WA ANGELO

Baibulo imachula “mkulu wa angelo” mmodzi cabe. Dzina lake ndi Mikayeli.—Danieli 12:1; Yuda 9.

Mikayeli ni Mtsogoleli wa asilikali akumwamba, angelo okhulupilika kwa Mulungu. Pa Chivumbulutso 12:7 timaŵelenga kuti: “Mikayeli ndi angelo ake anamenyana ndi cinjoka . . . ndi angelo ake.” Buku ya Chivumbulutso limaonetsa kuti Yesu ndiye Mtsogoleli wa asilikali akumwamba. Inde, Mikayeli ndiye dzina lina la Yesu.—Chivumbulutso 19:14-16.

▸ Nkhani 9, ndime 4

24 MASIKU OTSILIZA

Mauwa amatanthauza nthawi ya zocitika zikulu-zikulu pa dziko lapansi, kutatsala pang’ono kuti Ufumu wa Mulungu uwononge dziko la Satana. Pokamba za nthawi imodzi-modzi imeneyo, Baibulo imaseŵenzetsanso mau ena akuti, “mapeto a nthawi ino” ndi “kukhalapo kwa Mwana wa munthu.” (Mateyu 24:3, 27, 37) “Masiku otsiliza” anayamba pamene Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulila kumwamba mu  1914. Adzatha pamene dziko la Satana lidzawonongedwa pa Aramagedo.—2 Timoteyo 3:1; 2 Petulo 3:3.

▸ Nkhani 9, ndime 5

25 CIUKILILO

Ciukililo cimacitika pamene Mulungu waukitsa munthu amene anafa. Baibulo imachula ziukililo za anthu 9. Amene anacitako ziukililo zimenezi, mwa mphamvu ya Mulungu, anali Eliya, Elisa, Yesu, Petulo, ndi Paulo. Yehova analonjeza kuti adzaukitsa “olungama ndi osalungama omwe” pa dziko lapansi pano. (Machitidwe 24:15) Baibulo imachulanso za ciukililo ca oyenda kumwamba. Ciukililo cimeneci cimacitika pamene anthu osankhidwa, kapena kuti odzozedwa ndi Mulungu, amaukitsidwa ndi kuyenda kumwamba kukakhala ndi Yesu.—Yohane 5:28, 29; 11:25; Afilipi 3:11; Chivumbulutso 20:5, 6.

▸ Nkhani 9, ndime 13

26 ZAZIŴANDA (ZAMIZIMU)

Zaziŵanda kapena kuti zamizimu ni mcitidwe woipa woyesa kukambitsana ndi mizimu yoipa. Anthu amayesa kucita cimenezi mwacindunji kapena kupitila mwa munthu wina, monga ng’anga, munthu wokamba ndi mizimu, kapena wamatsenga. Anthu amacita zamizimu cifukwa amakhulupilila ciphunzitso conama cakuti munthu akafa, mzimu wake umacoka m’thupi ndi kukhala ciŵanda. Ziŵanda zimayesanso kupandutsa anthu kwa Yehova. Zamizimu zimaphatikizapo kukhulupilila nyenyezi, kuombeza, matsenga, ndi ufiti. Zinthu monga mabuku, magazini, mafilimu, zithunzi-thunzi zomatika, ngakhale ndi nyimbo, zimaonetsa monga kuti ziŵanda kapena zamatsenga zilibe vuto liliyonse, ndipo n’zinthu zokondweletsa. Miyambo ina ya malilo, monga kupeleka kwa azimu, maphwando a malilo, kuloŵa cokolo, ndi miyambo ina yambili, imaphatikizapo kukamba ndi ziŵanda. Ndipo nthawi zambili, anthu amaseŵezetsa mankhwala kuti aonetse mphamvu ya ziŵanda.—Agalatiya 5:20; Chivumbulutso 21:8.

▸ Nkhani 10, ndime 10; Nkhani 16, ndime 4

27 UCIFUMU WA YEHOVA

Yehova ni Mulungu Wamphamvuyonse, ndipo ndiye analenga zonse za m’cilengedwe. (Chivumbulutso 15:3) Ndiye cifukwa cake, iye ndiye mwiniwake wa cilengedwe conse, ali ndi mphamvu pa cilengedwe conse. (Salimo 24:1; Yesaya 40:21-23; Chivumbulutso 4:11) Iye anaika malamulo pa ciliconse cimene analenga. Alinso mphamvu zosankha anthu ena kukhala olamulila. Kuti tionetse kuti timacilikiza ucifumu wa Mulungu, tiyenela kumukonda ndi kumumvela. (1 Mbiri 29:11)

▸ Nkhani 11, ndime 10

28 KUCOTSA MIMBA

Kucotsa mimba ni kupha dala mwana amene ali m’mimba. Pano sitikamba za tsoka la kupitilila kapena kupita padela. Dziŵani kuti, kungocokela pamene mimba yakhala, mwanayo ni munthu payekha wokhala ndi moyo wake-wake. Ndiye cifukwa cake kucotsa mimba ni kupha munthu ndithu.

▸ Nkhani 13, ndime 5

29 KUIKIDWA MAGAZI

Cimeneci ni cithandizo camankhwala ku cipatala. Madokota amatenga magazi athunthu kapena imodzi mwa mbali zake zikulu-zikulu zinayi ndi kuika mwa munthu wodwala. Magazi amenewa amawatenga kwa munthu wina, kapena magazi osungidwa. Mbali zinayi zikulu-zikulu za magazi ni plasma (madzi a m’magazi), red blood cells (maselo ofiila a m’magazi), white blood cells (maselo oyela a m’magazi), ndi ma platelets (maselo othandiza magazi kugwilana).

▸ Nkhani 13, ndime 13

30 CILANGO

M’Baibulo liwu lakuti “cilango” silitanthauza kukhaulitsa cabe. Kulanga munthu kweni-kweni kumatanthauza kupatsa malango, kuphunzitsa, ndi kuwongolela. Yehova sapeleka cilango mwaukali kapena mwankhanza. (Miyambo 4:1, 2) Ndipo iye ali citsanzo cabwino kwa makolo. Yehova amapeleka cilango m’njila yothandiza kwambili, cakuti munthu amafika pocikonda cilango ca Mulungu. (Miyambo 12:1) Cifukwa cakuti Yehova amakonda anthu ake, amawapatsa ciphunzitso cofunikila. Amawapatsa malangizo owawongolela ndiponso owathandiza kuganiza ndi kucita zinthu m’njila yokondweletsa Mulungu. Conco, cilango ca makolo ciyenela kuthandiza kudziŵa zifukwa zimene afunikila kukhala ana omvela. Cilangoco ciyenela kuwaphunzitsa kukonda Yehova, ndi Mau ake, Baibulo, ndiponso kuwathandiza kumvetsa mfundo zake.

▸ Nkhani 14, ndime 13

31 ZIŴANDA

Ziŵanda ni zolengedwa zoipa zamzimu ndi zosaoneka, ndipo ni zamphamvu kwambili kupambana anthu. Ziŵanda ni angelo oipa. Angelo ameenewa anakhala oipa pamene anapandukila Mulungu . (Genesis 6:2; Yuda 6) Iwo analoŵa cipani ca Satana copandukila Yehova, titelo kukamba kwake.—Deuteronomo 32:17; Luka 8:30; Machitidwe 16:16; Yakobo 2:19.

▸ Nkhani 16, ndime 4

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani