PHUNZILO 26
Kodi Zoipa Komanso Mavuto Zinakhalako Bwanji?
Coipa cikacitika, mwacibadwa timafunsa kuti, “N’cifukwa ciyani zacitika?” Koma ubwino wake ni wakuti, Baibo imapeleka yankho lomveka bwino pa funso limeneli.
1. Kodi Satana anaziyambitsa bwanji zinthu zoipa padziko?
Satana Mdyelekezi anapandukila Mulungu. Pofuna ulamulilo, Satana ananyengelela anthu oyambawo, Adamu na Hava, kuti agwilizane naye pa kupanduka kwake. Satana anacita izi mwa kuuza Hava bodza. (Genesis 3:1-5) Iye anapangitsa Hava kuganiza kuti Yehova anali kum’mana cinacake cabwino. Cimene Satana anatanthauza n’cakuti anthu akhoza kupeza cimwemwe cacikulu ngati angaleke kumvela Mulungu. Iye ananama bodza loyamba pouza Hava kuti sadzafa. Pa cifukwa cimeneci, Baibo imachula Satana “kuti wabodza komanso tate wake wa bodza.”—Yohane 8:44.
2. Kodi Adamu na Hava anasankhapo kucita ciyani?
Yehova anali wowolowa manja kwambili kwa Adamu na Hava. Iye anawalola kudya zipatso za mtengo uliwonse m’munda wa Edeni kupatulapo mtengo umodzi wokha basi. (Genesis 2:15-17) Koma iwo anasankhabe kudya zipatso za mtengo woletsedwa umenewo. Conco Hava “anathyola cipatso ca mtengowo n’kudya.” Pambuyo pake, Adamu “nayenso anadya” (Genesis 3:6) Onse aŵili anapandukila Mulungu. Adamu na Hava pokhala angwilo, iwo analibe cikhotelelo cofuna kucita zoipa. Conco pamene anapandukila Mulungu, anacita kupanga cisankho cakuti asamumvele. Mwa kutelo, iwo anacimwa na kukana ulamulilo wa Mulungu. Cisankho cimeneco cinawabweletsela mavuto aakulu.—Genesis 3:16-19.
3. Kodi cisankho ca Adamu na Hava cinatikhudza motani?
Adamu na Hava atacimwa, anakhala opanda ungwilo. Mwa kutelo, anapatsila mbadwa zawo zonse kupanda ungwilo kwawo. Kunena za Adamu, Baibo imanena kuti: ‘Ucimo unaloŵa m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo n’kufalikila kwa anthu onse.’—Aroma 5:12.
Anthufe timakumana na mavuto pa zifukwa zosiyana-siyana. Nthawi zina timagwela m’mavuto cifukwa ca zosankha zathu zosaganiza bwino. Nthawi zinanso timakumana na mavuto cifukwa ca zosankha zoipa za anthu ena. Koma nthawi zina timapezeka m’mavuto cifukwa ca tsoka basi.—Ŵelengani Mlaliki 9:11.
KUMBANI MOZAMILAPO
Onani cifukwa cake si Mulungu amene amacititsa zoipa kapena mavuto padziko lapansi, komanso mmene iye amamvela tikamavutika.
4. Amene anacititsa kuti tizikumana na mavuto
Anthu ambili amakhulupilila kuti Mulungu ni amene amalamulila dziko lapansi. Kodi zimenezi n’zoona? Tambani VIDIYO.
Ŵelengani Yakobo 1:13, komanso 1 Yohane 5:19, kenako kambilanani funso ili:
Kodi Mulungu ndiye amacititsa mavuto komanso zoipa?
5. Onani zotulukapo za ulamulilo wa Satana
Ŵelengani Genesis 3:1-6, na kukambilana mafunso aya:
Kodi Satana anakamba bodza lakuti ciyani?—Onani vesi 4 na 5.
Mwa zimene Satana anakamba, kodi anatanthauza bwanji kuti Yehova anafuna kumana anthu cinacake cabwino?
Malinga n’kunena kwa Satana, kodi iye amaona kuti anthu amafunikila Ulamulilo wa Yehova kuti akhale acimwemwe?
Ŵelengani Mlaliki 8:9, na kukambilana funso ili:
Cifukwa Yehova si ndiye akulamulila dzikoli, kodi cacitika n’ciyani?
Adamu na Hava anali anthu angwilo m’Paradaiso. Koma cifukwa comvela zokamba za Satana, iwo anapandukila Yehova
Pambuyo pa cipanduko cimeneco, padziko lapansi panadzala macimo, mavuto, komanso imfa
Yehova adzacotsapo macimo, mavuto onse, ngakhale imfa. Pa nthawi imeneyo, anthu adzakhalanso angwilo m’Paradaiso
6.Yehova amatidela nkhawa tikakhala pa mavuto
Kodi n’zoona kuti Mulungu amatidela nkhawa tikakhala pa mavuto? Onani zimene Mfumu Davide komanso mtumwi Petulo analemba. Ŵelengani Salimo 31:7, komanso 1 Petulo 5:7, na kukambilana funso ili:
Kodi mukumva bwanji podziŵa kuti tikakhala pa mavuto, Yehova amaona komanso amatidela nkhawa?
7. Mulungu adzacotsapo mavuto onse amene timakumana nawo
Ŵelengani Yesaya 65:17, komanso Chivumbulutso 21:3, 4, na kukambilana funso ili:
N’cifukwa ciyani n’zokhazika mtima pansi kudziŵa kuti Yehova adzacotsapo mavuto onse amene anthu amakumana nawo?
Kodi mudziŵa?
Pamene Satana anakamba bodza loyamba, ananenela Yehova misece. Kutanthauza kuti anawononga mbili ya Yehova monga Wolamulila wolungama komanso wacikondi. Posacedwa, Yehova akadzacotsapo mavuto onse amene anthu amakumana nawo. Adzacotsanso citonzo pa dzina lake. Kunena kwina, iye adzatitsimikizila kuti ulamulilo wake ndiwo wabwino kopambana. Kuyeletsedwa kwa dzina la Yehova ndiyo nkhani yofunika kopambana m’cilengedwe conse.—Mateyu 6:9, 10.
ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Mavuto amene amatigwela, ni Mulungu amene anakonzelatu.”
Nanga inu muona bwanji?
CIDULE CAKE
Satana Mdyelekezi komanso anthu aŵili oyambilila ndiwo anayambitsa zoipa padziko lapansi. Yehova zimamukhudza kwambili pamene tikukumana na mavuto, n’cifukwa cake adzawacotsapo posacedwa.
Mafunso Obweleza
Kodi Satana Mdyelekezi anauza Hava bodza lakuti ciyani?
Kodi kupanduka kwa Adamu na Hava kunatikhudza bwanji ife tonse?
Tidziŵa bwanji kuti Yehova amatidela nkhawa tikamakumana na mavuto?
FUFUZANI
Dziŵani tanthauzo la m’Baibo la ucimo.
Ŵelengani zowonjezela zokhudza nkhani imene Satana Mdyelekezi anayambitsa m’munda wa Edeni.
“N’cifukwa Ciyani Mulungu Amalola Kuti Anthufe Tizivutika?” (Nsanja ya Mlonda, January 1, 2014)
Mvetsetsani mayankho okhazika mtima pansi pa funso lovuta ili.
Onani zimene munthu wina anaphunzila cifukwa coona mavuto ambili.