NKHANI YA PACIKUTO | MASOMPHENYA A ZINTHU ZA KUMWAMBA
N’ndani Amene Akhala Kumwamba?
Munayamba mwadzifunsapo kuti ‘Kodi kumwamba n’kwabwanji nanga kumakhala ndani?’ Ngati n’conco, simuli mwekha. Kwa zaka zambili, anthu akhala akukhulupilila zosiyana-siyana pankhani imeneyi. Ena amakhulupilila kuti kumwamba kumakhala mizimu ya makolo akale amene afunika kulemekezedwa. Enanso amati ni malo a bata ni mtendele kumene kumakhala angelo na anthu abwino amene anafa. Komanso ena amati kumwamba kumakhala milungu yambili-mbili.
Anthu ambili amakamba kuti sitingadziŵe za kumwamba cifukwa kulibe aliyense wocokela kumwamba amene anabwela padziko lapansi kudzatiuza mmene kulili. Koma zimenezi si zoona. Yesu Khiristu anali kumwamba akalibe kubwela padziko lapansi. Iye anafotokozela atsogoleli acipembedzo a m’nthawi yake kuti: “Ndinatsika kucokela kumwamba kudzacita cifunilo ca iye amene anandituma, osati cifunilo canga.” Conco, pamene Yesu anauza atumwi ake kuti: “M’nyumba ya Atate wanga muli malo ambili okhalamo,” anali kukamba zinthu zimene anadzionela yekha.—Yohane 6:38; 14:2.
Atate ŵake a Yesu ni Mulungu, amene dzina lake ni Yehova, ndipo “nyumba” yake ili kumwamba. (Salimo 83:18) Motelo, kulibe wina amene angafotokoze momveka bwino mmene kumwamba kulili kuposa Yehova Mulungu na Yesu Khiristu. Iwo anapangitsa anthu okhulupilika kuona masomphenya ocititsa cidwi. Masomphenya amenewa amatithandiza kudziŵa zambili za mmene kumwamba kulili.
Nkhani yotsatila idzafotokoza Malemba ena amene amakamba zimene anthu anaona m’masomphenya. Pamene muŵelenga za masomphenya amenewa, kumbukilani kuti kumwamba kumene tikamba pano ni malo auzimu, amene kulibe zinthu zooneka kapena zogwilika. M’malo motifotokozela zinthu za kumwamba m’njila imene sitingamvetsetse, Mulungu anaonetsa atumiki ake masomphenya a zinthu zakumwamba m’njila yosavuta kumva. Masomphenya amenewa adzakuthandizani kudziŵa amene ‘amakhala’ kumwamba.