LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp16 na. 6 tsa. 16
  • Kodi Baibo Imakamba Ciani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Baibo Imakamba Ciani?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Mulungu amayankha mapemphelo onse?
  • Kodi tifunika kukhala bwanji popemphela?
  • Mwayi Wa Pemphelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Yandikilani kwa Mulungu Kupitila M’pemphelo
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Muyandikileni Mulungu Kupitila m’Pemphelo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kuyankha Mafunso a M’baibo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
wp16 na. 6 tsa. 16
Mkazi apemphela

Kodi Baibo Imakamba Ciani?

Kodi Mulungu amayankha mapemphelo onse?

KODI MUNGAKAMBE KUTI AMAYANKHA MAPEMPHELO . . .

  • A munthu aliyense

  • A anthu ena

  • Sayankha

ZIMENE BAIBO IMAKAMBA

“Yehova ali pafupi ndi onse . . . amene amamuitana m’coonadi.”—Salimo 145:18.

MFUNDO ZINA ZIMENE BAIBO IMAKAMBA

  • Mulungu sayankha mapemphelo a anthu amene samumvela. (Yesaya 1:15) Koma anthu a conco ‘angakhalenso pa ubwenzi wabwino’ na Mulungu ngati asintha makhalidwe awo.—Yesaya 1:18.

  • Kuti Mulungu ayankhe pemphelo, lifunika kukhala logwilizana na zimene iye amafuna, ndipo zimene amafunazo zipezeka m’Baibo.—1 Yohane 5:14.

Kodi tifunika kukhala bwanji popemphela?

ANTHU ENA AMAKHULUPILILA kuti nthawi zonse tifunika kugwada, kuŵelama, kapena kuika manja pamodzi popemphela. Inu muganiza bwanji?

ZIMENE BAIBO IMAKAMBA

Mulungu anayankha mapemphelo a anthu amene anapemphela ali ‘cokhala pansi,’ ‘coimilila,’ ‘cogona’ kapena ‘cogwada.’ (1 Mbiri 17:16; 2 Mbiri 30:27; Ezara 10:1; Machitidwe 9:40) Iye safuna kuti tikhale mwanjila inayake yapadela popemphela.

MFUNDO ZINA ZIMENE BAIBO IMAKAMBA

  • Mulungu amamvela mapemphelo a anthu odzicepetsa.—Salimo 138:6.

  • Mungapemphele ca mumtima ndiponso m’cinenelo ciliconse.—2 Mbiri 6:32, 33; Nehemiya 2:1-6.

Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 17 m’buku ili, Zimene Baibulo Ingatiphunzitse, lofalitsidwa na Mboni za Yehova

Bukuli limapezekanso pa webusaiti ya www.jw.org

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani