Kubweleza za M’sukulu ya Ulaliki
Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki mkati mwa mlungu wa February 25, 2013. Taonetsa deti la mlungu umene tidzaphunzila mfundo iliyonse. Tacita zimenezi kuti mlungu uliwonse tizitha kufufuza mfundozo pokonzekela.
1. N’cifukwa ciani Yesu anakamba kuti “anthu amene akumva cisoni” ndi odala? (Mat. 5:4) [Jan. 7, w09 2/15 tsa. 6 ndime 6]
2. Malinga ndi pemphelo lacitsanzo limene Yesu anaphunzitsa ophunzila ake, kodi iye anatanthauzanji pamene anati: “Musatilowetse m’mayeselo”? (Mat. 6:13) [Jan. 7, w04 2/1 tsa. 16 ndime 13]
3. N’cifukwa ninji Yesu anati ophunzila ake sadzamaliza gawo lao lolalikila kufikila Mwana wa munthu akabwele? (Mat. 10:23) [Jan. 14, w10 9/15 tsa. 10 ndime 12; w87 8/1 tsa. 28 ndime 6]
4. Kodi fanizo la Yesu la kanjele ka mpilu limaunika zinthu ziŵili ziti? (Mat. 13:31, 32) [Jan. 21, w08 7/15 mas. 17-18 ndime 3-8]
5. Kodi Yesu anali kuphunzitsa mfundo yanji pamene anati: “Mukapanda kutembenuka n’kukhala ngati ana aang’ono, simudzaloŵa mu ufumu wakumwamba”? (Mat. 18:3) [Jan. 28, w07 2/1 mas. 9-10 ndime 3-4]
6. Kodi mau a Yesu akuti “mwanena nokha” amatanthauza ciani? (Mat. 26:63, 64) [Feb. 11, w11 6/1 tsa. 18]
7. N’cifukwa ninji Yesu amachedwa “Mbuye wa sabata”? (Maliko 2:28) [Feb. 18, w08 2/15 tsa. 28 ndime 7]
8. N’cifukwa ciani Yesu poyankha, ananena zimene ananena zokhudza amai ndi abale ake, ndipo tiphunzilapo ciani? (Maliko 3:31-35) [Feb. 18, w08 2/15 tsa. 29 ndime 5]
9. Malinga ndi Maliko 8:22-25, n’cifukwa ciani Yesu anacilitsa munthu wakhungu pang’ono-pang’ono, ndipo tiphunzilapo ciani? [Feb. 25, w00 2/15 tsa. 17 ndime 7]
10. Kodi tiphunzilapo ciani pa zimene Yesu anacita Petulo atam’dzudzula pa Maliko 8:32-34? [Feb. 25, w08 2/15 tsa. 29 ndime 6]