Kubweleza za M’sukulu ya Ulaliki
Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki mkati mwa mlungu wa April 29, 2013. Taonetsa deti la mlungu umene tidzaphunzila mfundo iliyonse. Tacita zimenezi kuti mlungu uliwonse tizitha kufufuza mfundozo pokonzekela.
1. Kodi ndi cikumbutso cofunika kwambili citi conena za cikwati cimene Yesu anapeleka pa Maliko 10:6-9? [Mar. 4, w08 2/15 tsa. 30 ndime 8]
2. Kodi kutumikila Yehova ndi mtima wonse kumatanthauza ciani? (Maliko 12:30) [Mar. 4, w97 10/15 tsa. 13 ndime 4]
3. Kodi “masautso” amene achulidwa pa Maliko 13:8 n’ciani? [Mar. 11, w08 3/15 tsa. 12 ndime 2]
4. Kodi ndi mabuku ati amene Luka anafufuzamo pamene anali kulemba Uthenga wake Wabwino? (Luka 1:3) [Mar. 18, w09 3/15 tsa. 32 ndime 4]
5. Kodi mfundo yakuti Satana amayesetsa kupeza nthawi yabwino yoti atiyese, iyenela kutilimbikitsa kucita ciani? (Luka 4:13) [Mar. 25, w11 1/15 tsa. 23 ndime 10]
6. Kodi mau opezeka pa Luka 6:27, 28, tingawagwilitsile nchito bwanji? [Mar. 25, w08 5/15 tsa. 8 ndime 4]
7. N’cifukwa ciani Yesu anakhululukila mai amene anali kudziŵika monga wocimwa iye asanamwalile monga nsembe ya dipo? (Luka 7:37, 48) [Apr. 1, w10 8/15 tsa. 6-7]
8. Kodi otsatila a Kristu afunika ‘kudana’ ndi acibale ao m’njila yotani? (Luka 14:26) [Apr. 15, w08 3/15 tsa. 32 ndime 1; w92 7/15 tsa. 9 ndime 3-5]
9. Kodi “zizindikilo padzuŵa, mwezi ndi nyenyezi” zidzakhudza motani anthu? (Luka 21:25) [Apr. 22, w97 4/1 tsa. 15 ndime 8-9]
10. Kodi tingatsanzile bwanji citsanzo ca Yesu ca kupemphela pamene tikumana ndi mavuto aakulu? (Luka 22:44) [Apr. 29, w07 8/1 tsa. 6 ndime 2]