Kubweleza za M’sukulu ya Ulaliki
Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki mkati mwa mlungu wa August 26, 2013. Taonetsa deti la mlungu umene tidzaphunzila mfundo iliyonse. Tacita zimenezi kuti mlungu uliwonse tizitha kufufuza mfundozo pokonzekela.
1. Kodi ndi phunzilo lofunika liti limene tingaphunzile kwa Mfumu Herode pamene anafunitsitsa kulandila citamando ndi ulemelelo wosayenela kucokela kwa anthu? (Mac. 12:21-23) [July 1, w08 5/15 tsa. 32 ndime 7]
2. Kodi Akristu acicepele angapindule bwanji pamene alingalila ndi kutsanzila citsanzo ca Timoteyo? (Mac. 16:1, 2) [July 8, w08 5/15 tsa. 32 ndime 10]
3. Kodi Akula ndi Purisikila anathandiza bwanji Apolo mwacikondi pamene anamumva akulankhula “molimba mtima” ku sunagoge wa ku Efeso? (Mac. 18:24-26) [July 15, w10 6/15 tsa. 11 ndime 4]
4. Kodi ndi mfundo ya m’Malemba iti imene imathandiza Mboni za Yehova kugwilitsila nchito malamulo a m’dziko lao kuteteza ufulu wao wolalikila? (Mac. 25:10-12) [July 22, bt tsa. 198 ndime 6]
5. Kodi mtumwi Paulo anapitiliza bwanji kupeza mipata yolalikila ngakhale pamene anali m’ndende ku Roma? Nanga atumiki a Yehova masiku ano amatsatila bwanji citsanzo cake? (Mac. 28:17, 23, 30, 31) [July 29, bt mas. 215-217 ndime 19-23]
6. N’cifukwa ciani Baibo imanena kuti kugonana amuna kapena akazi okha-okha ndi cinthu conyansa komanso cosemphana ndi cibadwa? (Aroma 1:26, 27) [Aug. 5, g 1/12 tsa. 28 ndime 7]
7. Kodi “dipo lolipilidwa ndi Kristu” mu 33 C.E. linaphimba bwanji “macimo amene anacitika kale” dipolo lisanalipilidwe? (Aroma 3:24, 25) [Aug. 5, w08 6/15 tsa. 29 ndime 6]
8. Kodi ndi makonzedwe acikondi ati amene Yehova apeleka tikamakumana ndi zinthu zothetsa nzelu ndipo sitikudziŵa conena m’pemphelo? (Aroma 8:26, 27) [Aug. 12, w08 6/15 tsa. 30 ndime 10]
9. Kodi mau akuti “Khalani oceleza” amatanthauza ciani? (Aroma 12:13) [Aug. 19, w09 10/15 mas. 5-6 ndime 12-13]
10. Monga mmene Paulo anasonyezela, kodi Akristu ‘amavala Ambuye Yesu Kristu’ m’njila yotani? (Aroma 13:14) [Aug. 26, w05 1/1 mas. 11-12 ndime 20-22]