Kubweleza za M’sukulu ya Ulaliki
Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki mkati mwa mlungu wa June 30, 2014.
Taonetsa deti la mlungu umene tidzaphunzila mfundo iliyonse. Tacita zimenezi kuti mlungu uliwonse tizifufuza mfundozo pokonzekela.
N’cifukwa ciani mfundo ya pa Ekisodo 23:2 ndi yofunika kwambili posankha zosangulutsa? [May 5, w11 7/15 mas. 10 mpaka 11 ndime 3-7]
Kodi lamulo lakuti ansembe azisamba popeleka nsembe kwa Yehova linali lofunika motani? Nanga masiku ano lamulo limeneli litikumbutsa ciani monga atumiki a Mulungu? (Eks. 30:18-21) [May 19, w96 7/1 tsa. 9 ndime 9]
N’cifukwa ciani Aroni sanalangidwe pamene anapanga mwana wa ng’ombe wagolide? (Eks. 32:1-8, 25-35) [May 19, w04 3/15 tsa. 27 ndime 4]
Kodi lamulo la Mulungu kwa Aisiraeli loletsa kukwatilana ndi mitundu ina limafanana bwanji ndi mmene Mkristu amaonela cisumbali ndi cikwati? (Eks. 34:12-16) [May 26, w89 11/1 mas. 20-21 ndime 11-13]
N’cifukwa ciani zocitika paumoyo wa Bezaleli ndi Oholiabu n’zolimbikitsa kwa ife? (Eks. 35:30-35) [May 26, w10 9/15 tsa. 10 ndime 13]
“Cizindikilo copatulika ca kudzipeleka” pa nduwila imene mkulu wansembe anali kuvala ndi cikumbutso ca n’ciani? Nanga cizindikilo cimeneci cimatikumbutsa ciani pa kudzipeleka kwathu? (Eks. 39:30) [June 2, w01 2/1 tsa. 14 ndime 2-3]
Kodi Akristu onse ali ndi udindo wotani ponena za kuulula macimo aakulu amene Mkristu wina wacita? (Lev. 5:1) [June 9, w97 8/15 tsa. 27]
M’nthawi ya Aisiraeli kodi nsembe zacinyanjo zinali zofunika motani? Nanga zili ndi tanthauzo lanji kwa ife masiku ano? (Lev. 7:31-33) [June 16, w12 1/15 tsa. 19 ndime 11-12]
Kodi chimo la ana a Aroni, Nadabu ndi Abihu, lingakhale kuti linaphatikizapo ciani? Nanga nkhani imeneyi itiphunzitsa ciani? (Lev. 10:1, 2, 9) [June 23, w04 5/15 tsa. 22 ndime 6-8]
N’cifukwa ciani mkazi anali kukhala “wodetsedwa” akabeleka mwana? (Lev. 12:2, 5) [June 23, w04 5/15 tsa. 23 ndime 2]