LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 6/15 tsa. 7
  • Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
Utimiki Wathu wa Ufumu—2015
km 6/15 tsa. 7

Kubweleza za m’Sukulu ya Ulaliki

Tidzakambilana mafunso otsatilawa pa Sukulu ya Ulaliki mkati mwa mlungu wa June 29, 2015. Deti limene lili mu mkutilamau kapena kuti mabulaketi ndi la mlungu umene mfundoyo inakambidwa.

  1. Kodi cinalakwika n’ciani ndi mmene Mikala analankhulila ndi Davide? Nanga anthu okwatilana angaphunzilepo ciani pa nkhani imeneyi? (2 Sam. 6: 20- 23) [May 11, w11 8/1 tsa. 12 ndime 1]

  2. Kodi mneneli Natani anacita ciani pamene Yehova anamuongolela atauza Davide kuti apitilize kumangila Yehova kacisi? (2 Sam. 7: 2, 3) [May 11, w12 2/15 tsa. 24 ndime 6-7]

  3. N’cifukwa ciani Natani anayamba ndi fanizo la pa 2 Samueli 12: 1-7 polankhula ndi Davide m’malo momuuza mwacindunji kuti anacita chimo loopsa? Nanga nkhani imeneyi ingatithandize bwanji kukhala aphunzitsi abwino? [May 18, w12 2/15 tsa. 24 ndime 2-3]

  4. N’cifukwa ciani Aisiraeli anakopeka mosavuta ndi Abisalomo? Nanga tingadziteteze bwanji kwa a Abisalomo amasiku ano? (2 Sam. 15:6) [May 25, w12 7/15 tsa. 13 ndime 7]

  5. Kodi Yehova anamuthandiza bwanji Davide panthawi ya mavuto? Nanga tikuphunzilapo ciani pamenepa? (2 Sam. 17:27- 29) [June 1, w08 9/15 tsa. 6 ndime 15-16]

  6. Tingaphunzile ciani pa citsanzo ca Davide tikaona mmene anacitila zinthu ndi Itai mlendo? (2 Sam. 18:2) [June 1, w09 5/15 tsa. 27 ndime 7]

  7. Kodi acikulile mumpingo angatengele bwanji citsanzo ca Barizilai? (2 Sam. 19:33-35) [June 8, w07 7/15 tsa. 15 ndime 1-2]

  8. Kodi mau okhudza kukhulupilika amene Davide anakamba ndi olimbikitsa bwanji kwa atumiki a Yehova masiku ano? (2 Sam. 22:26) [June 15, w10 6/1 tsa. 26 ndime 6-7]

  9. Kodi Natani anaonetsa bwanji kuti anali wokhulupilika kwa Mulungu? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cake masiku ano? (1 Maf. 1: 11- 14) [June 22, w12 2/15 tsa. 25 ndime 1, 4-5]

  10. Ndi zocitika ziti zimene zingacititse mtumiki wa Mulungu kunyalanyaza malamulo a Mulungu monga mmene Solomo anacitila? (1 Maf. 3:1) [June 29, w11 12/15 tsa. 10 ndime 12-14]

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani