Mfundo Yothandiza Pofufuza
Malifalensi Opezeka mu Watchtower LAIBULALI YA PA INTANETI
Malifalensi amathandiza kuti muphunzile nkhani zosiyana-siyana. Malifalensi a pa intaneti amenewa, amaphatikizapo Glossary, Insight on the Scriptures, Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova, komanso Watch Tower Publications Index.
Danga lofufuzila la mu Watchtower LAIBULALI YA PA INTANETI ingakuthandizeni kupeza malifalensi amenewo. Mukamalemba m’danga lofufuzila limenelo, mawu amene mukufunawo amaonekela munsi mwa dangalo.
Yesani izi: Lembani liwu lakuti “Yehova” m’danga lofufuzila (A). Kenako, sankhani liwu lakuti “Yehova” limene laonekela munsi mwa dangalo (B). Pamenepo mudzaona malifalensi osiyana-siyana amene akamba za Yehova.