Webu Saiti yathu—Igwilitsileni Nchito pa Phunzilo Laumwini ndi la Banja
Ŵelengani Magazini Atsopano pa Inteneti: Ŵelengani Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! pa Intaneti milungu ingapo musanalandile makope ku mpingo. Mvetselani magazini akuŵelengedwa.—Pitani pa kamutu kakuti “Publications/Magazines.”
Ŵelenganinso Nkhani Zimene Zimapezeka Cabe pa Intaneti: Nkhani zina monga zakuti, “Zoti Acinyamata Acite,” “Zimene Ndikuphunzila M’Baibulo,” “Zoti Banja Likambilane,” ndi “Zimene Acinyamata Amadzifunsa,” tsopano zikuonekela pa Webu saiti yathu yokha. Pitani pa Intaneti ndi kusankha nkhani zimene mungagwilitsile nchito pocita phunzilo laumwini ndi la banja.—Pitani pa tumitu takuti “Bible Teachings/Children” kapena “Bible Teachings/Teenagers.”
Ŵelengani Nkhani Zatsopano: Ŵelengani malipoti ndi zocitika zolimbikitsa, ndiponso onani zithunzi-thunzi zoonetsa kupita patsogolo kwa nchito yathu padziko lonse lapansi. Malipoti okhudza masoka acilengedwe ndi zinzunzo, amathandiza kuti mapemphelo athu okhudza abale athu amene ali m’mavuto akhale acindunji. (Yak 5:16)—Pitani pa kamutu kakuti “News.”
Fufuzani mwa Kugwilitsila Nchito Laibulale ya pa Intaneti: Ngati muli ndi laibulale imeneyi mu cinenelo canu, gwilitsilani nchito kompyuta kapena foni yanu kuti muŵelenge lemba la tsiku kapena kufufuza nkhani mu zofalitsa zathu zina zatsopano pa intaneti.— Pitani pa kamutu kakuti “Publications/Online Library,” kapena lembani www.wol.jw.org pa malo ofufuzila Webu saiti imene mukufuna.
[Cithunzi papeji 4]
(Kuti muone mau onse, pitani ku cofalitsa)
Iyeseni
1 Dinizani pa cithunzi-thunzi kapena pa kamutu kakuti “Tengani.” Ndiyeno cithunzi-thunzi cidzaonekela mum’pangidwe wa PDF. Pulintani ndi kupatsa mwana wanu kuti apeze mayankho.
2 Dinizani pa kamutu kakuti “Lizani” kuti mupenyelele vidiyo.