Kodi Mudziŵa?
Ni galeta la mtundu wanji limene nduna ya ku Itiyopiya inakwela pomwe Filipo anakamba nayo?
LIWU leni-leni limene linamasulidwa kuti “galeta” mu Baibulo la Dziko Latsopano lingatanthauze magaleta a mitundu yosiyana-siyana. (Mac. 8:28, 29, 38) Komabe, zioneka kuti nduna ya ku Itiyopiya inakwela galeta yaikulu kuposa magaleta wamba omwe anali kuwaseŵenzetsa pa nkhondo kapena pa mpikisano. Ganizilani zina mwa zifukwa zimene tanenela conco.
Mwitiyopiyayo anali munthu waudindo ndipo anayenda ulendo wautali. Anali “munthu waulamulilo pansi pa Kandake, mfumukazi ya Itiyopiya. Iye anali woyang’anila cuma conse ca mfumukaziyo.” (Mac. 8:27) Itiyopiya wakale anali kuphatikizapo dziko limene masiku ano limachedwa Sudan, komanso mbali yaikulu ya kum’mwela kwa Egypt. Ngakhale kuti mwina mwamunayo sanayendele mu galeta imodzi pa ulendo wonsewo, ayenela kuti anali na katundu wapaulendo. Magaleta ena amene anali kugwilitsa nchito kunyamula anthu mu zaka za zana loyamba, anali ngolo za mawilo anayi zokhala na mtenje. Buku lakuti Acts—An Exegetical Commentary linanena kuti, “Magaleta otelo anali kukhala na malo ambili oikapo katundu, zimene zinali kupangitsa ulendo kukhala wofewa, kapenanso kucititsa munthu kuwonjezela mtunda umene angayende.”
Mwitiyopiya uja anali kuŵelenga pomwe Filipo anam’peza. Baibo imati “Filipo anathamanga m’mbali mwa galetalo ndi kumumva akuŵelenga mokweza m’buku la Yesaya mneneli.” (Mac. 8:30) Magaleta a paulendo sanapangidwe kuti aziyenda mothamanga. Kuyenda pang’ono-pang’ono kwa galetalo, kunalola ndunayo kuŵelenga, komanso kunalola Filipo kuti apeze galetalo wapansi.
Mwitiyopiyayo “anacondelela Filipo kuti akwele ndi kukhala naye m’galetamo.” (Mac. 8:30) Okwela m’galeta loseŵenzetsa pa mpikisano anali kuimilila. Koma mu galeta la paulendo munali malo okwanila omwe ndunayo, komanso Filipo anakhalapo.
Mogwilizana na mawu ouzilidwa olembedwa mu Machitidwe caputala 8, komanso umboni wa mbili yakale umene ulipo, zofalitsa zathu za posacedwa zaonetsa nduna ya ku Itiyopiya itakwela galeta lalikulu kuposa magaleta wamba a nkhondo kapena a mpikisano.