LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 May masa. 14-19
  • Yembekezelani Mzinda Wokhalitsa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yembekezelani Mzinda Wokhalitsa
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MUZIDALILA AMENE SADZAKUSIYANI KONSE
  • MUZIMVELA AMENE AKUTSOGOLELA
  • MUZIKONDA ABALE NDIPO KHALANI OCELEZA
  • ZIMENE ZIDZACITIKA M’TSOGOLO
  • Kalata Yotithandiza Kupilila Mpaka Mapeto
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Zisankho Zimene Zimaonetsa Kuti Timadalila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Muzivomeleza Kuti Pali Zimene Simudziwa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Kuyandikila Abale ndi Alongo Athu n’Kwabwino Kwa Ife!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 May masa. 14-19

NKHANI YOPHUNZILA 21

NYIMBO 21 Pitilizani Kufuna-funa Ufumu Coyamba

Yembekezelani Mzinda Wokhalitsa

“Tikufunitsitsa mzinda umene ukubwelawo.”​—AHEB. 13:14.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Mmene lemba la Aheberi caputala 13 lingatithandizile palipano komanso m’tsogolo.

1. Kodi Yesu anati n’ciyani cidzacitikile mzinda wa Yerusalemu?

KUTATSALA masiku ocepa kuti Yesu Khristu aphedwe, iye anafotokoza mwatsatanetsatane ulosi umene unakwanilitsika koyamba kumapeto kwa dongosolo la Ciyuda. Anacenjeza kuti tsiku lina ‘magulu a nkhondo adzazungulila’ mzinda wa Yerusalemu. (Luka 21:20) Yesu anauza otsatila ake kuti akadzangoona magulu a nkhondowo, adzafunika kucoka mu mzinda nthawi yomweyo. Mawu a Yesu anakwanilitsika. Magulu a asilikali aciroma anazungulila Yerusalemu.​—Luka 21:​21, 22.

2. Ndi malangizo otani amene Paulo anapatsa Akhristu a ku Yudeya ndi ku Yerusalemu?

2 Kutatsala zaka zocepa kuti Aroma azungulile Yerusalemu, mtumwi Paulo analemba kalata yamphamvu imene tsopano imadziwika kuti buku la Aheberi. M’kalata imeneyo, Paulo anapatsa Akhristu a ku Yudeya komanso ku Yerusalemu malangizo amene anali kudzawathandiza kukonzekela zomwe zinali kubwela m’tsogolo. Kodi n’ciyani cinali kudzacitika m’tsogolo? Yerusalemu anali kudzawonongedwa. Kuti Akhristuwo apulumuke, anafunika kukhala okonzeka kusiya nyumba zawo komanso mabizinesi awo. Ponena za mzinda wa Yerusalemu, Paulo analemba kuti: “Panopa tilibe mzinda wokhazikika.” Kenako anawonjezela kuti: “Koma tikufunitsitsa mzinda umene ukubwelawo.” ​—Aheb. 13:14.

3. Kodi “mzinda wokhala ndi maziko enieni” n’ciyani? Nanga n’cifukwa ciyani timauyembekezela?

3 N’kutheka kuti Akhristu amene anasankha kucoka mu Yerusalemu ndi mu Yudeya anasekedwa komanso kunyozedwa ndi anthu ambili. Koma ngakhale n’telo cisankho cimeneco cinapulumutsa miyoyo yawo. Masiku anonso, anthu amatiseka cifukwa sitiika cidalilo cathu mwa anthu kapena mu ndalama, ndipo sitimafunafuna umoyo wawofuwofu m’dzikoli. N’cifukwa ciyani sitimatelo? Timadziwa kuti dongosolo lino la zinthu ndi losakhalitsa. Timafunafuna “mzinda wokhala ndi maziko enieni,” kutanthauza “mzinda umene ukubwelawo,” womwe ndi Ufumu wa Mulungu.a (Aheb. 11:10; Mat. 6:33) Pansi pa kamutu kalikonse m’nkhani ino tikambilana: (1) mmene uphungu wouzilidwa wa Paulo unathandizila Akhristu a m’zaka za zana loyamba kupitiliza kuyembekezela “mzinda umene ukubwelawo,” (2) zimene Paulo anacita powakonzekeletsa zocitika za m’tsogolo, ndi (3) mmene uphungu wake ungatithandizile masiku ano.

MUZIDALILA AMENE SADZAKUSIYANI KONSE

4. N’cifukwa ciyani mzinda wa Yerusalemu unali wofunika kwa Akhristu?

4 Mzinda wa Yerusalemu unali wofunika kwambili kwa Akhristu. Mpingo wa Cikhristu wa m’zaka za zana loyamba unakhazikitsidwa mu mzindawo mu 33 C.E. ndipo n’kumenenso kunali bungwe lolamulila. Kuwonjezela apo, Akhristu ambili anali ndi nyumba komanso zinthu zambili zakuthupi mu mzindawo. Komabe, Yesu anali atacenjeza otsatila ake kuti ayenela kucoka mu mzinda wa Yerusalemu ndi mu Yudeya.​—Mat. 24:16.

5. Kodi Paulo anawakonzekeletsa motani Akhristu kaamba ka zimene zinali kubwela m’tsogolo?

5 Pofuna kukonzekeletsa Akhristu kaamba ka zimene zinali kubwela m’tsogolo, Paulo anawathandiza kuona mzinda wa Yerusalemu mmene Yehova anali kuuonela. Paulo anawakumbutsa kuti kwa Yehova, kacisi, ansembe, komanso nsembe zimene zinali kupelekedwa mu Yerusalemu sizinalinso zopatulika. (Aheb. 8:13) Anthu ambili mu mzindawo anali atakana Mesiya. Kacisi wa ku Yerusalemu sanalinso cimake ca kulambila koyela ndipo anali kudzawonongedwa.​—Luka 13:​34, 35.

6. N’cifukwa ciyani malangizo a Paulo a pa Aheberi 13:​5, 6 anali apanthawi yake kwa Akhristu?

6 Pamene Paulo anali kulembela kalata Aheberi, anthu anali kusangalala kukhala mu mzinda wa Yerusalemu ndipo ambili anali kupita kukauyendela. Ponena za mzinda wa Yerusalemu, wolemba wina waciroma ananena kuti “mzindawo unali wochuka Kum’mawa konse.” Caka ciliconse, Ayuda ocokela m’malo osiyanasiyana anali kupita ku mzinda wa Yerusalemu kukacita zikondwelelo. Izi zinacititsa kuti mzindawo utukuke pa nkhani ya malonda. Mwacionekele, Akhristu ena anapindula cifukwa ca kutukuka kwa mzindawo. N’kutheka ndiye cifukwa cake Paulo anawauza kuti: “Musamakonde ndalama, koma muzikhutila ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.” Kenako iye anagwila mawu Malemba oonetsa citsimikizo camphamvu ca Yehova cakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Welengani Aheberi 13:​5, 6; Deut. 31:6; Sal. 118:6) Akhristu a mu Yerusalemu ndi Yudeya anafunikila citsimikizo cimeneci. Cifukwa ciyani? Cifukwa posakhalitsa atalandila kalatayi, anafunika kusiya nyumba zawo, mabizinesi awo, komanso katundu wawo. Ndipo anali kufunika kuyamba umoyo watsopano kumalo ena.

7. N’cifukwa ciyani tiyenela kulimbitsa cidalilo cathu mwa Yehova palipano?

7 Zimene tiphunzilapo: Kodi n’ciyani cidzacitika m’tsogolo posacedwapa? “Cisautso cacikulu” cidzayamba, ndipo dongosolo loipali la zinthu lidzawonongedwa. (Mat. 24:21) Monga anacitila Akhristu a m’zaka za zana loyamba, ifenso tiyenela kukhala maso komanso okonzeka. (Luka 21:​34-36) Panthawi ya cisautso cacikulu, tingadzafunike kusiya katundu wathu wina kapena wonse, tili ndi cidalilo cakuti Yehova sadzasiya konse anthu ake. Ngakhale palipano pomwe tikuyembekezela cisautso cacikulu, tili ndi mpata woonetsa kumene timaika cidalilo cathu. Dzifuseni kuti, ‘Kodi zocita ndi zolinga zanga, zimaonetsa kuti sindidalila cuma koma ndimadalila Mulungu amene analonjeza kuti adzandisamalila?’ (1 Tim. 6:17) Citsanzo ca Akhristu a m’nthawi yakale cingatithandize kukhalabe okhulupilika pa “cisautso cacikulu.” Komabe, “cisautso cacikulu” cimene cikubwela cidzakhala covuta kwambili kuposa cimene Akhristuwo anakumana naco. Conco tidzadziwa bwanji zoyenela kucita cikadzayamba?

MUZIMVELA AMENE AKUTSOGOLELA

8. Kodi Yesu anawapatsa malangizo otani ophunzila ake?

8 Patapita zaka zocepa, Akhristu atalandila kalata ya Aheberi imene Paulo anawalembela, anaona mzinda wa Yerusalemu utazungulilidwa ndi asilikali a Roma. Izi zinawapatsa cizindikilo cakuti nthawi yoti athawe yakwana. Mzinda wa Yerusalemu unali utatsala pang’ono kuwonongedwa. (Mat. 24:3; Luka 21:​20, 24) Koma kodi anayenela kuthawila kuti? Yesu anangokamba kuti: “Amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawila kumapili.” (Luka 21:21) Koma m’delalo munali mapili ambili. Conco akanadziwa bwanji mapili oyenela kuthawilako?

9. N’cifukwa ciyani ziyenela kuti zinali zovuta kwa Akhristu kudziwa mapili omwe akanathawilako? (Onaninso mapu.)

9 Ganizilani ena mwa mapili amene Akhristu akanathawilako. Panali mapili a ku Samariya, mapili a ku Galileya, Phiri la Herimoni, mapili a ku Lebanoni, ndiponso mapili omwe anali kutsidya lina la mtsinje wa Yorodano. (Onani mapu.) N’kutheka kuti ina ya mizinda yomwe inali m’mapilimu inali kuoneka yotetezeka. Mwacitsanzo, mzinda wa Gamla unali pamwamba pa phili ndipo zinali zovuta zedi kufikako. Ayuda ena anali kuona mzindawo monga malo abwino acitetezo. Komabe, Aroma ndi Ayuda anamenyana koopsa mumzinda umenewu wa Gamla, ndipo anthu ambili amumzindawo anaphedwa.b

Mapu ikuonetsa ena a mapili ndi mizinda ya dziko la Isiraeli ya m’nthawi ya atumwi. kumpoto kwa Yerusalemu kuli mapili a ku Lebanoni, a ku Galileya, a ku Samariya, ndi a ku Giliyadi. Kulinso Phili la Herimoni ndi Phili la Tabori. Mizinda imene ili kumpoto kwa Yerusalemu ndi Gamla, Kaisareya, ndi Pela. Kum’mwela kwa Yerusalemu kuli mapili a ku Yudeya ndi a ku Abarimu. Kulinso mzinda wa Masada. Mapuyi ikuonetsanso njila zimene Aroma anadutsa pokathila nkhondo komanso madela a Ayuda omwe Aroma analanda kucokela mu 67 C.E. mpaka mu 73 C.E.

Panali mapili ambili kumene Akhristu oyambilila akanathawilako, koma si konse kumene akanapeza citetezo. (Onani ndime 9)


10-11. (a) Kodi Yehova ayenela kuti anawatsogolela motani Akhristu? (Aheberi 13:​7, 17) (b) Kodi Akhristu anapindula bwanji kaamba komvela amene anali kuwatsogolela? (Onaninso cithunzi.)

10 Zikuoneka kuti Yehova anatsogolela Akhristuwo kudzela mwa omwe anali kutsogolela mumpingo. Pambuyo pakuti mzinda wa Yerusalemu wawonongedwa, wolemba mbili wina dzina lake Eusebius anati: “Mulungu anavumbula kwa ena mwa abale ku Yerusalemu kuti Akhristu anayenela kucoka ku Yerusalemu ndi kupita ku Pela, mzinda womwe unali ku Perea.” Kuthawila ku Pela cinali cisankho canzelu. Sikunali kutali ndi ku Yerusalemu. Conco sikunali kovuta kwambili kufikako. Pela sunali mzinda wa Ayuda ndipo sunakhudzidwe ndi kumenyana komwe kunali pakati pa Ayuda ndi Aroma.​—Onani mapu.

11 Akhristu omwe anali ‘kumvela amene anali kuwatsogolela’ mumpingo, anathawila kumadela a mapili ku Pela. (Welengani Aheberi 13:​7, 17.) Cifukwa ca kumvelaku, anapulumuka. Mbili yakale imatsimikizila kuti Mulungu sanawasiye konse anthu amene “ankayembekezela mzinda wokhala ndi maziko enieni,” womwe ndi Ufumu wa Mulungu.​—Aheb. 11:10.

Gulu la Akhristu a m’nthawi ya atumwi likudutsa m’dela lamapili litanyamula katundu wawo.

Pela anali malo acitetezo othawilako kwa Akhristu ndipo sanali kutali (Onani ndime 10-11)


12-13. Ndi motani mmene Yehova watsogolela anthu ake m’nthawi zovuta?

12 Zimene tiphunzilapo: Yehova amagwilitsa nchito amene akutsogolela popeleka malangizo acindunji kwa anthu ake. M’Malemba muli zitsanzo zambili zoonetsa mmene Yehova wagwilitsila nchito abusa potsogolela anthu ake pa nthawi zovuta. (Deut. 31:23; Sal. 77:20) Ndipo ifenso masiku ano, taona umboni wokwanila woonetsa kuti Yehova akupitiliza kugwilitsa nchito anthu amene akutsogolela.

13 Mwacitsanzo, mlili wa COVID-19 utabuka, awo “amene akutsogolela” anapeleka malangizo apanthawi yake. Akulu analandila malangizo a mmene misonkhano inayenela kucitikila n’colinga cothandiza abale ndi alongo awo kuuzimu. Pasanapite nthawi mliliwu utabuka, tinacita msonkhano wosaiwalika m’zinenelo zoposa 500 kudzela pa Intaneti, pa TV, ndi pa wailesi. Cakudya cauzimu sicinaleke kupelekedwa. Conco, tinakhalabe ogwilizana. Tisakayikile kuti kaya tikumane ndi mayeso otani m’tsogolomu, Yehova adzapitiliza kuthandiza abale amene akutsogolela kuzindikila zisankho zanzelu zimene ayenela kupanga. Kuwonjezela pa kudalila Yehova ndi kumvela malamulo ake, ndi makhalidwe ena ati omwe adzatithandiza kukonzekela cisautso cacikulu ndi kucita zinthu mwanzelu pa nthawi yovuta imeneyo?

MUZIKONDA ABALE NDIPO KHALANI OCELEZA

14. Malinga ndi Aheberi 13:​1-3, ndi makhalidwe ati amene Akhristu anayenela kuonetsa m’masiku otsiliza a dongosolo la Ciyuda?

14 Cisautso cacikulu cikadzayamba, tidzafunikila kuonetsana cikondi kuposa n’kale lonse. Pa nkhaniyi, tidzayenela kutengela citsanzo ca Akhristu amene anali ku Yerusalemu ndi ku Yudeya. Iwo anali kuonetsana cikondi nthawi zonse. (Aheb. 10:​32-34) Koma kutatsala pang’ono kuti dongosolo la Ciyuda lithe, Akhristu anayenela kukondana ndi kucelezana kuposa n’kale lonse.c (Welengani Aheberi 13:​1-3.) Ndi mmenenso zidzakhalile kwa ife dongosolo lino la zinthu likadzatsala pang’ono kuwonongedwa.

15. N’cifukwa ciyani Akhristu aciheberi anafunikila kuonetsana cikondi capaubale ndi kucelezana atathawila kumapili?

15 Asilikali aciroma atazungulila Yerusalemu, kenako n’kubwelela mosayembekezeleka, Akhristu anakhala ndi mwayi wothawa. Komabe, sakanatha kutenga katundu wambili. (Mat. 24:​17, 18) Conco atathawila kumapili n’kuyamba umoyo watsopano, anafunikila kumathandizana. Mosakayikila, abale ambili anafunikila cakudya, zovala, ndi pogona. Uwu unali mwayi kwa Akhristu woonetsana mzimu woceleza ndi cikondi ceniceni mwa kuthandizana ndi kugawana zimene anali nazo.​—Tito 3:14.

16. Kodi tingaonetse bwanji cikondi kwa alambili anzathu amene akufunikila thandizo? (Onaninso cithunzi.)

16 Zimene tiphunzilapo: Cikondi cimatisonkhezela kuthandiza abale ndi alongo athu akafunikila thandizo. Abale ambili akhala okonzeka kusamalila zosowa zakuthupi ndi zauzimu za abale ndi alongo amene athawa kwawo cifukwa ca nkhondo ndi matsoka acilengedwe amene acitika posacedwapa. Mlongo wina wa ku Ukraine amene anasiya nyumba yake cifukwa ca nkhondo anati: “Taona dzanja la Yehova likutithandiza ndi kutitsogolela kudzela mwa abale athu. Anatilandila ndi kutisamalila bwino ku Ukraine, ku Hungary, komanso kuno ku Germany.” Timaonetsa kuti ndife anchito anzake a Yehova tikamathandiza abale ndi alongo athu pa zimene akufunikila.​—Miy. 19:17; 2 Akor. 1:​3, 4.

Banja lacikulile likulandila banja lothawa kwawo m’nyumba yawo. Banja lothawalo lili ndi cola ca zovala ndi katundu wina wocepa.

Akhristu othawa kwawo masiku ano amafunikila thandizo lathu (Onani ndime 16)


17. N’cifukwa ciyani n’zofunika kukulitsa cikondi cathu pa abale komanso kuwaceleza masiku ano?

17 Mosakaikila, pa nthawi ya cisautso cacikulu tidzafunika kuthandizana mokulilapo kuposa mmene timacitila masiku ano. (Hab. 3:​16-18) Yehova akutiphunzitsa masiku ano mmene tingakulitsile cikondi cathu pa abale komanso kuwaceleza. Makhalidwe amenewa adzakhala ofunika kwambili pa nthawiyo.

ZIMENE ZIDZACITIKA M’TSOGOLO

18. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Akhristu aciheberi a m’zaka za zana loyamba?

18 Monga mmene mbili imaonetsela, Akhristu amene anathawila ku mapili anapulumuka pamene Yerusalemu anawonongedwa. Iwo anasiya mzindawo, koma Yehova sanawasiye konse. Nanga bwanji masiku ano? Sitikudziwa zonse zimene zidzacitika m’tsogolo. Komabe, Yesu anaticenjeza kuti tiyenela kukhala okonzeka kumvela. (Luka 12:40) Tilinso ndi malangizo ena othandiza amene Paulo analemba kwa Aheberi. Malangizo amenewa akali othandiza kwa ife masiku ano monga analili kwa Akhristu aciheberi. Ndipo Yehova iyemwini akutilonjeza kuti sadzatitaya konse kapena kutisiya. (Aheb. 13:​5, 6) Conco, tiyeni tipitilize kuyembekezela mzinda wokhalitsa, womwe ndi Ufumu wa Mulungu, ndipo tidzasangalala ndi madalitso osatha amene udzabweletse.​—Mat. 25:34.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’cifukwa ciyani tifunika kukulitsa cidalilo cathu mwa Yehova palipano?

  • N’cifukwa ciyani kumvela kudzakhala kofunika panthawi ya “cisautso cacikulu”?

  • N’cifukwa ciyani palipano tifunika kukulitsa cikondi pa abale komanso kuwaceleza?

NYIMBO 157 Mtendele Wosatha Pamapeto Pake!

a M’nthawi za m’Baibo, mizinda inali kulamulidwa ndi mafumu. Mzinda wa conco unali kuonedwa ngati ufumu.​—Gen. 14:2.

b Izi zinacitika mu 67 C.E. pasanapite nthawi Akhristu atathawa mu Yudeya ndi Yerusalemu.

c Mawu amene anawamasulila kuti “kukonda abale” angatanthauze cikondi cimene anthu a mimba imodzi amaonetsana. Koma Paulo anawagwilitsa nchito potanthauza cikondi cacikulu cimene timaonetsana mu mpingo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani