Salimo
118 Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.+
Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.
2 Isiraeli anene kuti:
“Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”
3 Anthu amʼnyumba ya Aroni tsopano anene kuti:
“Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”
4 Anthu amene amaopa Yehova tsopano anene kuti:
“Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”
6 Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa.+
Munthu angandichite chiyani?+
8 Kuthawira kwa Yehova nʼkwabwino
Kusiyana ndi kudalira anthu.+
9 Kuthawira kwa Yehova nʼkwabwino
Kusiyana ndi kudalira akalonga.+
11 Mitunduyo inandizungulira, ndithu inandizungulira kumbali zonse.
Koma mʼdzina la Yehova
Ndinaithamangitsira kutali.
12 Inandizungulira ngati njuchi,
Koma inathimitsidwa mwamsanga ngati moto umene uli pakati pa minga.
Mʼdzina la Yehova,
Ndinaithamangitsira kutali.+
13 Ndinakankhidwa kwambiri kuti ndigwe,
Koma Yehova anandithandiza.
14 Ya ndi malo anga obisalapo komanso mphamvu yanga,
Iye wakhala chipulumutso changa.+
15 Phokoso lachisangalalo komanso chipulumutso*
Likumveka mʼmatenti a anthu olungama.
Dzanja lamanja la Yehova likusonyeza mphamvu zake.+
16 Dzanja lamanja la Yehova lakwera mʼmwamba chifukwa wapambana.
Dzanja lamanja la Yehova likusonyeza mphamvu zake.+
17 Sindidzafa, koma ndidzakhala ndi moyo,
Kuti ndilengeze ntchito za Ya.+
19 Nditsegulireni mageti achilungamo.+
Ndidzalowa mmenemo ndipo ndidzatamanda Ya.
20 Ili ndi geti la Yehova.
Olungama adzalowa pamenepo.+
21 Ndidzakutamandani, chifukwa munandiyankha+
Ndipo munakhala chipulumutso changa.
24 Ili ndi tsiku limene Yehova wapanga.
Tidzakondwera ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
25 Yehova tikukupemphani, chonde tipulumutseni.
Yehova, chonde tithandizeni kuti tipambane.
26 Wodalitsidwa ndi amene akubwera mʼdzina la Yehova.+
Tikupempha kuti Yehova akudalitseni mʼnyumba yake.
27 Yehova ndi Mulungu.
Iye amatipatsa kuwala.+
Tiyeni tikhale limodzi ndi gulu la anthu amene akupita kuchikondwerero atanyamula nthambi mʼmanja mwawo,+
Mpaka kukafika panyanga za guwa lansembe.+
28 Inu ndinu Mulungu wanga ndipo ndidzakutamandani.
Ndinu Mulungu wanga ndipo ndidzakukwezani.+