Salimo
Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Davide.
124 “Yehova akanapanda kukhala nafe,”+
Tsopano Isiraeli anene kuti,
2 “Yehova akanapanda kukhala nafe,+
Pamene anthu anatiukira,+
3 Akanatimeza amoyo+
Pamene mkwiyo wawo unatiyakira.+
4 Pamenepo madzi akanatikokolola,
Mtsinje wamphamvu ukanatimiza.+
5 Madzi amphamvu akanatikokolola.
6 Yehova atamandike,
Chifukwa sanatipereke kwa iwo kuti atimbwandire ngati nyama.
7 Tili ngati mbalame imene yathawa
Pamsampha wa munthu wosaka.+
Msamphawo unathyoka,
Ndipo ife tinathawa.+
8 Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova,+
Amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.”