Salimo
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
2 Udzadya zinthu zimene wapeza utagwira ntchito mwakhama.
Udzakhala wosangalala ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.+
3 Mkazi wako adzakhala ngati mtengo wa mpesa wobereka zipatso mʼnyumba mwako.+
Ana ako adzakhala ngati mphukira za mtengo wa maolivi kuzungulira tebulo lako.
4 Mwamuna aliyense amene amaopa Yehova
Adzadalitsidwa mwa njira imeneyi.+
5 Yehova adzakudalitsa ali ku Ziyoni.
Uone zinthu zikuyenda bwino mu Yerusalemu masiku onse a moyo wako,+
6 Ndipo uone ana a ana ako.
Mtendere ukhale pa Isiraeli.