Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
134 Tamandani Yehova,
Inu nonse atumiki a Yehova,+
Inu amene mumaimirira mʼnyumba ya Yehova usiku.+
2 Muzikhala oyera mukamapemphera mutakweza manja anu+
Ndipo muzitamanda Yehova.
3 Yehova, amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi,
Akudalitseni ali ku Ziyoni.