Salimo
Nyimbo ya Davide.
15 Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti yanu?
Ndi ndani amene angakhale mʼphiri lanu lopatulika?+
2 Ndi amene akuyenda mosalakwitsa zinthu,*+
Amene amachita zinthu zabwino+
Komanso kulankhula zoona mumtima mwake.+
4 Iye sagwirizana ndi munthu aliyense wonyansa,+
Koma amalemekeza anthu amene amaopa Yehova.
Sasintha zimene walonjeza* ngakhale zinthu zitakhala kuti sizili bwino kwa iye.+