Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
20 Yehova akuyankheni pa tsiku la mavuto.
Dzina la Mulungu wa Yakobo likutetezeni.+
3 Akumbukire nsembe zanu zonse zimene munapereka monga mphatso.
Alandire mosangalala* nsembe zanu zopsereza. (Selah)
5 Tidzafuula mosangalala chifukwa cha mmene mwatipulumutsira,+
Tidzakweza mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu.+
Yehova akwaniritse zopempha zanu zonse.
6 Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake.+
Amamuyankha kuchokera kumwamba kwake koyera,
Pomupulumutsa modabwitsa ndi dzanja lake lamanja.+
7 Ena amadalira magaleta ndipo ena amadalira mahatchi,+
Koma ife timadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.+
8 Anthu amenewo akomoka ndipo agwa,
Koma ife tadzuka ndipo taimirira.+
9 Inu Yehova, pulumutsani mfumu!+
Tsiku limene tidzapemphe kuti atithandize, Mulungu adzatiyankha.+