Salimo
Ndipulumutseni kwa munthu wachinyengo komanso wochita zinthu zopanda chilungamo.
2 Inu ndinu Mulungu wanga, ndinu malo anga achitetezo.+
Nʼchifukwa chiyani mwanditaya?
Kodi ndiziyenda wachisoni chifukwa chiyani? Nʼchifukwa chiyani adani anga akundipondereza?+
3 Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu.+
4 Kenako ndidzapita paguwa lansembe la Mulungu,+
Kwa Mulungu amene amandisangalatsa kwambiri.
Ndipo ndidzakutamandani ndi zeze+ inu Mulungu, Mulungu wanga.
5 Nʼchifukwa chiyani ndataya mtima?
Nʼchifukwa chiyani ndikuvutika mumtima mwanga?