Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Masikili.* Salimo la Davide. Pa nthawi imene amuna a ku Zifi anabwera kudzauza Sauli kuti: “Davide akubisala kwathu.”+
2 Inu Mulungu, imvani pemphero langa.+
Tcherani khutu ku mawu ochokera mʼkamwa mwanga.
3 Chifukwa anthu achilendo andiukira,
Ndipo anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga.+
Iwo salemekeza Mulungu.*+ (Selah)
4 Taonani! Mulungu ndi amene amandithandiza.+
Yehova amadalitsa anthu amene akundithandiza.
5 Iye adzabwezera adani anga+ zoipa zimene akuchitira anthu ena.
Inu Mulungu wanga, awonongeni* chifukwa ndinu wokhulupirika.+
6 Ndidzapereka nsembe kwa inu+ mofunitsitsa.
Inu Yehova, ndidzatamanda dzina lanu chifukwa ndi labwino.+