Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zoimbira za zingwe pa Sheminiti.* Nyimbo ya Davide.
6 Inu Yehova, musandidzudzule mutakwiya,
Musandilangize mutapsa mtima.+
2 Ndikomereni mtima,* inu Yehova, chifukwa ndayamba kufooka.
Ndichiritseni, inu Yehova,+ chifukwa mafupa anga akunjenjemera.
3 Ine ndasokonezeka* kwambiri,+
Ndipo ndikufunseni, inu Yehova, kodi ndipitiriza kuvutika mpaka liti?+
4 Bwererani, inu Yehova, mudzandipulumutse.+
Ndipulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika.+
6 Ndafooka chifukwa cha kuusa moyo kwanga.+
Usiku wonse ndimanyowetsa bedi langa* ndi misozi,
Ndimalira ndipo misozi imadzaza pabedi panga.+
7 Maso anga afooka chifukwa cha chisoni changa.+
Maso anga achita mdima* chifukwa cha anthu onse amene akundizunza.
8 Ndichokereni pamaso panga inu nonse amene mumachita zoipa,
Chifukwa Yehova adzamva mawu a kulira kwanga.+
9 Yehova adzamva pempho langa loti andikomere mtima.+
Yehova adzayankha pemphero langa.
10 Adani anga onse adzachititsidwa manyazi ndipo adzataya mtima.
Iwo adzathawa mwadzidzidzi komanso mwamanyazi.+