Salimo
BUKU LA 4
(Masalimo 90-106)
Pemphero la Mose, munthu wa Mulungu woona.+
90 Inu Yehova, mwakhala malo athu okhalamo+ ku mibadwo yonse.
2 Mapiri asanabadwe,
Kapena musanakhazikitse dziko lapansi komanso nthaka,+
Inu ndinu Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.+
3 Mumabwezera munthu kufumbi,
Mumanena kuti: “Bwererani kufumbi, inu ana a anthu.”+
4 Chifukwa kwa inu zaka 1,000 zili ngati dzulo lapitali,+
Zili ngati ulonda umodzi wa usiku.
6 Mʼmawa umaphuka ndipo umabiriwira,
Koma madzulo umafota kenako nʼkuuma.+
7 Chifukwa ife tawonongedwa ndi mkwiyo wanu,+
Ndipo tikuchita mantha kwambiri ndi ukali wanu.
8 Mumaika zolakwa zathu patsogolo panu,*+
Zinsinsi zathu zaululika chifukwa cha kuwala kwa nkhope yanu.+
9 Moyo wathu ukutha chifukwa cha mkwiyo wanu.
Timafa msanga ngati mpweya umene umatha mofulumira.
Koma zimakhala zodzaza ndi mavuto komanso chisoni.
Zimatha mofulumira ndipo moyo wathu umachoka.+
11 Ndi ndani angadziwe kuchuluka kwa mphamvu za mkwiyo wanu?
Ukali wanu ndi waukulu mofanana ndi mantha amene tikuyenera kukusonyezani.+
13 Bwererani, inu Yehova!+ Kodi zinthu zikhala chonchi mpaka liti?+
Timvereni chisoni ife atumiki anu.+
14 Mʼmawa, muzitisonyeza chikondi chanu chokhulupirika,+
Kuti tizifuula mokondwera komanso kukhala mosangalala+ masiku onse a moyo wathu.
15 Tichititseni kuti tisangalale kwa masiku ofanana ndi masiku amene mwatisautsa,+
Kwa zaka zofanana ndi zaka zimene takumana ndi masoka.+
16 Atumiki anu aone ntchito zanu,
Ndipo ana awo aone ulemerero wanu.+
17 Yehova Mulungu wathu atikomere mtima.
Chititsani kuti ntchito ya manja anthu iyende bwino.*