- 
	                        
            
            Deuteronomo 15:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
- 
                            - 
                                        21 Koma ngati nyamayo ili ndi vuto, monga kulumala kapena khungu, kapena chilema chilichonse chachikulu, musamaipereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu.+ 
 
- 
                                        
- 
	                        
            
            Malaki 1:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
- 
                            - 
                                        14 “Wotembereredwa ndi aliyense wochita zachinyengo, amene ali ndi nyama yabwinobwino yamphongo pa ziweto zake koma amalonjeza nʼkupereka nsembe nyama yachilema kwa Yehova. Ine ndine Mfumu yaikulu+ ndipo dzina langa lidzaopedwa pakati pa anthu a mitundu ina,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+ 
 
-