-
Numeri 26:7-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Amenewa anali mabanja a anthu a fuko la Rubeni ndipo amuna onse amene anawerengedwa analipo 43,730.+
8 Mwana wamwamuna wa Palu anali Eliyabu. 9 Ana aamuna a Eliyabu anali Nemueli, Datani ndi Abiramu. Awiriwa, Datani ndi Abiramu, ndi amene anasankhidwa pa gululo ndipo anagwirizana ndi gulu la Kora+ pokangana ndi Mose+ komanso Aroni pamene ankatsutsana ndi Yehova.+
-