-
Numeri 16:5-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Ndiyeno Mose anauza Kora ndi anthu onse amene ankamutsatira kuti: “Mawa mʼmamawa, Yehova adzasonyeza munthu amene ali wake+ ndiponso amene ali woyera, amene ali woyenera kuyandikira pamaso pake.+ Ndipo amene ati adzamusankheyo+ adzayandikira pamaso pake. 6 Mudzachite izi: Iweyo Kora ndi anthu onse amene akukutsatira+ mudzatenge zofukizira.+ 7 Mʼzofukizirazo mudzaikemo moto komanso zofukiza nʼkubwera nazo pamaso pa Yehova mawa. Munthu amene Yehova adzamusankhe,+ ndi amene ali woyera. Inu ana a Levi+ mwawonjeza kwambiri.”
-