-
1 Mafumu 21:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Ndiyeno Ahabu anafunsa Eliya kuti: “Wandipeza kodi mdani wanga?”+ Eliya anayankha kuti: “Inde ndakupezani. Mulungu wanena kuti, ‘Chifukwa watsimikiza mtima kuti uchite zoipa pamaso pa Yehova,+ 21 ndikubweretsera tsoka ndipo ndidzaseseratu nyumba yako ndi kupha mwamuna* aliyense wa mʼbanja la Ahabu,+ ngakhalenso ooneka onyozeka ndi ofooka mu Isiraeli.+
-
-
1 Mafumu 22:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Mfumu ya Isiraeli inayankha Yehosafati kuti: “Patsala munthu mmodzi amene tingathe kufunsira kwa Yehova+ kudzera mwa iye, koma ndimadana naye kwambiri,+ chifukwa salosera zabwino zokhudza ine, koma zoipa zokhazokha.+ Dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imula.” Koma Yehosafati anati: “Mfumu siyenera kulankhula choncho.”
-
-
2 Mbiri 25:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Choncho Yehova anakwiyira kwambiri Amaziya ndipo anatumiza mneneri kukamʼfunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukutsatira milungu yomwe sinapulumutse anthu awo mʼmanja mwanu?”+ 16 Mneneriyo atanena zimenezi, mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi tinakuika kuti ukhale mlangizi wa mfumu?+ Usiyiretu kunena zimenezi.+ Ukufuna kuti akuphe?” Choncho mneneriyo anasiya, koma anati: “Ndikudziwa kuti Mulungu wakonza zoti akuwonongeni chifukwa cha zimene mwachitazi ndiponso chifukwa simunamvere malangizo anga.”+
-