-
Yesaya 58:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Ngati chifukwa cha Sabata mukupewa* kuchita zofuna zanu* pa tsiku langa lopatulika,+
Ndipo mukanena kuti Sabata ndi tsiku losangalatsa kwambiri, tsiku lopatulika la Yehova, tsiku loyenera kulemekezedwa,+
Ndipo mukalilemekeza mʼmalo mochita zofuna zanu ndiponso mʼmalo molankhula zopanda pake,
14 Mukatero mudzasangalala kwambiri mwa Yehova,
Ndipo ine ndidzakuchititsani kuti mukwere mʼmalo apamwamba a dziko lapansi.+
-