-
Numeri 35:33, 34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Musamadetse dziko limene mukukhalamo, chifukwa magazi ndi amene amadetsa dziko.+ Ndipo dziko limene ladetsedwa ndi magazi silingayeretsedwe ndi china chilichonse, kupatulapo magazi a munthu amene anakhetsa magaziyo.+ 34 Musamadetse dziko limene mukukhalamo, limene inenso ndikukhalamo, chifukwa ine Yehova ndikukhala pakati pa Aisiraeli.’”+
-
-
2 Mbiri 33:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Manase anapitiriza kusocheretsa Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu ndipo anawachititsa kuti azichita zinthu zoipa kuposa zimene ankachita anthu a mitundu yomwe Yehova anaiwononga pamaso pa Aisiraeli.+
-
-
Yeremiya 3:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Anthu amafunsa kuti: “Ngati mwamuna wathetsa ukwati ndi mkazi wake, ndipo mkaziyo akachokadi nʼkukakwatiwa ndi mwamuna wina, kodi mwamunayo angabwererenso kwa mkaziyo?”
Kodi dzikoli silaipitsidwa kale kwambiri?+
Yehova wanena kuti: “Iwe wachita uhule ndi amuna ambirimbiri.+
Ndiye kodi pano ukufuna ubwererenso kwa ine?
-
-
Yeremiya 23:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Dzikoli ladzaza ndi anthu achigololo.+
Chifukwa cha matemberero, dziko likulira maliro+
Ndipo malo amʼchipululu odyetserako ziweto auma.+
Zochita za anthuwa ndi zoipa ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika.
11 “Aneneri ndi ansembe, onse aipitsidwa.*+
Ndipo ngakhale mʼnyumba mwanga ndapezamo zoipa zimene akuchita,”+ akutero Yehova.
-