-
Yeremiya 39:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Choncho Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu ndi Nebusazibani amene anali Rabisarisi,* Nerigali-sarezera amene anali Rabimagi* ndi akuluakulu onse a mfumu ya Babulo anatuma anthu. 14 Iwo anatuma anthuwo kuti akatenge Yeremiya mʼBwalo la Alonda+ nʼkumupereka kwa Gedaliya+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani,+ kuti apite naye kunyumba kwake. Choncho Yeremiya anayamba kukhala ndi anthu.
-
-
Yeremiya 41:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Isimaeli mwana wa Netaniya ndi amuna 10 amene anali naye ananyamuka nʼkupha ndi lupanga Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani. Choncho Isimaeli anapha munthu amene mfumu ya Babulo inamuika kuti azilamulira dzikolo.
-