22 Ndiyeno Nebukadinezara mfumu ya Babulo, anasankha Gedaliya+ mwana wa Ahikamu+ mwana wa Safani,+ kuti akhale mtsogoleri wa anthu amene anawasiya ku Yuda.+
10 Koma Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu, anasiya mʼdziko la Yuda ena mwa anthu amene anali osauka kwambiri omwe analibe kalikonse. Pa tsiku limenelo anawapatsanso minda ndi minda ya mpesa kuti azilima.*+