-
2 Mafumu 25:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Mʼchaka cha 9 cha ufumu wa Zedekiya, mʼmwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera ku Yerusalemu pamodzi ndi asilikali ake onse.+ Anabwera kudzamenyana ndi anthu amumzindawo ndipo anamanga msasa komanso mpanda kuzungulira mzinda wonsewo.+ 2 Mzindawo unazunguliridwa mpaka chaka cha 11 cha Mfumu Zedekiya.
-
-
Yesaya 29:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ine ndidzamanga misasa mokuzungulira mbali zonse,
Ndidzamanga mpanda wa mitengo yosongoka mokuzungulira,
Ndipo ndidzamanga malo okwera omenyerapo nkhondo kuti ndimenyane nawe.+
-
-
Ezekieli 4:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 “Iwe mwana wa munthu, tenga njerwa ndipo uiike patsogolo pako. Panjerwapo ujambulepo mzinda wa Yerusalemu. 2 Umenye nkhondo ndi mzindawo+ ndipo umange mpanda womenyerapo nkhondo kuzungulira mzinda wonsewo.+ Umangenso malo okwera omenyerapo nkhondo+ komanso misasa ya asilikali. Uikenso zida zankhondo zogumulira mpanda wa mzindawo kuzungulira mzinda wonsewo.+
-
-
Ezekieli 21:21, 22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Chifukwa mfumu ya Babulo idzaima pamalo pamene misewu iwiriyo yagawikana kuti iwombeze maula. Mfumuyo idzagwedeza mivi, idzafunsira kwa mafano ake* komanso idzawombeza maula pogwiritsa ntchito chiwindi cha nyama. 22 Maula amene adzakhale mʼdzanja lake lamanja, adzasonyeza kuti apite ku Yerusalemu, akaike zida zogumulira mzindawo, akalamule asilikali ake kuti aphe anthu, akalize chizindikiro cha nkhondo, akaike zida zogumulira mageti a mzindawo, akamange malo okwera omenyerapo nkhondo ndiponso kuti akamange mpanda womenyerapo nkhondo.+
-