-
Yeremiya 28:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Ndiyeno mʼchaka chomwecho, chaka cha 4, mʼmwezi wa 5, kumayambiriro kwa ulamuliro wa Zedekiya+ mfumu ya Yuda, mneneri Hananiya mwana wa Azuri, wa ku Gibiyoni,+ anauza Yeremiya mʼnyumba ya Yehova pamaso pa ansembe ndi anthu onse kuti: 2 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ndithyola goli la mfumu ya Babulo.+
-
-
Yeremiya 28:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Kenako Hananiya anauza anthu onse amene anali pamenepo kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Mofanana ndi mmene ndathyolera goli ili, zaka ziwiri zisanathe,+ ndidzathyola goli la Nebukadinezara mfumu ya Babulo limene waveka mitundu yonse ya anthu.’” Zitatero, mneneri Yeremiya anachokapo.
-
-
Yeremiya 37:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Tsopano ali kuti aneneri anu amene ankalosera kwa inu kuti, ‘Mfumu ya Babulo sidzabwera kudzamenyana ndi inu ndiponso dzikoliʼ?+
-