-
2 Mafumu 24:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Mfumuyo inatenga anthu onse a ku Yerusalemu, akalonga onse,+ asilikali onse amphamvu, amisiri onse ndiponso anthu osula zitsulo*+ nʼkupita nawo ku Babulo. Anthu onse amene inawatenga analipo 10,000. Palibe amene anatsala, kupatulapo anthu osauka kwambiri a mʼdzikolo.+ 15 Choncho iye anatenga Yehoyakini+ nʼkupita naye ku Babulo.+ Ku Yerusalemu anatenganso mayi a mfumuyo, akazi ake, nduna za panyumba yake komanso akuluakulu a mʼdzikolo, nʼkupita nawo ku Babulo.
-
-
Yeremiya 24:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Kenako Yehova anandionetsa madengu awiri a nkhuyu amene anali patsogolo pa kachisi wa Yehova. Anandionetsa madenguwo pambuyo poti Nebukadinezara* mfumu ya Babulo watenga Yekoniya*+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, pamodzi ndi akalonga a Yuda, amisiri komanso anthu osula zitsulo,* kuchoka ku Yerusalemu nʼkupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+
-
-
Danieli 1:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Kenako Yehova anapereka Mfumu Yehoyakimu ya Yuda mʼmanja mwake,+ limodzi ndi zina mwa ziwiya za mʼnyumba ya* Mulungu woona. Nebukadinezara anatenga ziwiyazo nʼkupita nazo kudziko la Sinara,*+ kunyumba* ya mulungu wake ndipo anakaziika mʼnyumba yosungiramo chuma ya mulungu wake.+
3 Ndiyeno mfumu inalamula Asipenazi, mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumu kuti abweretse ena mwa Aisiraeli,* kuphatikizapo a mʼbanja lachifumu komanso anthu olemekezeka.+
-