-
2 Mafumu 25:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Akasidi anaphwanyaphwanya zipilala zakopa+ zomwe zinali mʼnyumba ya Yehova, zotengera zokhala ndi mawilo+ ndiponso thanki ya kopa yosungira madzi+ zimene zinali mʼnyumba ya Yehova, nʼkutenga kopa wake kupita naye ku Babulo.+ 14 Akasidiwo anatenganso ndowa, mafosholo, zozimitsira nyale, makapu ndi ziwiya zonse zakopa zimene ansembe ankagwiritsa ntchito potumikira mʼkachisi.
-
-
2 Mbiri 36:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Mfumuyo inatenga ziwiya zonse, zazikulu ndi zazingʼono, zamʼnyumba ya Mulungu woona. Inatenganso chuma cha mʼnyumba ya Yehova, chuma cha mfumu ndi cha akalonga ake. Inatenga chilichonse nʼkupita nacho ku Babulo.+
-
-
Yeremiya 52:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Akasidi anaphwanyaphwanya zipilala zakopa+ zapanyumba ya Yehova, zotengera zokhala ndi mawilo+ ndiponso thanki yakopa yosungira madzi+ zimene zinali mʼnyumba ya Yehova nʼkutenga kopa yense kupita naye ku Babulo.+ 18 Akasidiwo anatenganso ndowa, mafosholo, zozimitsira nyale, mbale zolowa,+ makapu+ ndi ziwiya zonse zakopa zimene ansembe ankagwiritsa ntchito potumikira mʼkachisi.
-
-
Danieli 5:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ndiyeno anabweretsa ziwiya zagolide zimene anazitenga mʼkachisi, mʼnyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Kenako mfumuyo, nduna zake, adzakazi ake ndi akazi ake ena anayamba kumwera mʼziwiyazo.
-