-
2 Mafumu 25:13-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Akasidi anaphwanyaphwanya zipilala zakopa+ zomwe zinali mʼnyumba ya Yehova, zotengera zokhala ndi mawilo+ ndiponso thanki ya kopa yosungira madzi+ zimene zinali mʼnyumba ya Yehova, nʼkutenga kopa wake kupita naye ku Babulo.+ 14 Akasidiwo anatenganso ndowa, mafosholo, zozimitsira nyale, makapu ndi ziwiya zonse zakopa zimene ansembe ankagwiritsa ntchito potumikira mʼkachisi. 15 Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenga zopalira moto ndi mbale zolowa, zomwe zinali zagolide+ komanso zasiliva weniweni.+ 16 Koma sanathe kuyeza kulemera kwa kopa wa zipilala ziwiri zija, thanki yosungira madzi ndiponso zotengera zokhala ndi mawilo zimene Solomo anapanga kuti zizigwira ntchito panyumba ya Yehova.+
-