-
Danieli 5:31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Dariyo+ Mmedi anapatsidwa ufumuwo ndipo anali ndi zaka pafupifupi 62.
-
-
Danieli 6:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Ndiyeno Dariyo anaona kuti ndi bwino kuti aike masatarapi* 120 oti aziyangʼanira zigawo zonse za ufumu wake.+ 2 Anaikanso nduna zapamwamba zitatu kuti ziziyangʼanira masatarapiwo ndipo Danieli anali mmodzi wa ndunazo.+ Masatarapiwo+ ankayenera kuuza nduna zimenezi chilichonse chimene chikuchitika nʼcholinga chakuti zinthu za mfumu zisawonongeke.
-