Salimo
149 Tamandani Ya!*
2 Isiraeli asangalale ndi Mlengi wake Wamkulu.+
Ana a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yawo.
3 Atamande dzina lake akuvina+
Komanso kumuimbira nyimbo zomutamanda pogwiritsa ntchito maseche ndi zeze.+
4 Chifukwa Yehova amasangalala ndi anthu ake.+
Iye amakongoletsa anthu ofatsa ndi chipulumutso.+
5 Anthu okhulupirika asangalale chifukwa Mulungu amawalemekeza.
Iwo aimbe mosangalala ali pamabedi awo.+
6 Pakamwa pawo patuluke nyimbo zotamanda Mulungu,
Ndipo lupanga lakuthwa konsekonse likhale mʼmanja mwawo,
7 Kuti abwezere anthu a mitundu ina,
Komanso kupereka chilango kwa mitundu ya anthu,
8 Ndiponso kuti amange mafumu awo maunyolo,
Komanso kumanga anthu awo olemekezeka mʼmatangadza achitsulo.
9 Kuti awalange mogwirizana ndi chigamulo chimene chinalembedwa.+
Ulemerero umenewu ndi wa anthu onse okhulupirika a Mulungu.
Tamandani Ya!*