Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • 1 Akorinto 10
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

Zimene Zili Mʼbuku la 1 Akorinto

      • Zitsanzo zotichenjeza za Aisiraeli (1-13)

      • Chenjezo pa nkhani yolambira mafano (14-22)

        • Tebulo la Yehova ndiponso tebulo la ziwanda (21)

      • Ufulu ndiponso kuganizira ena (23-33)

        • “Muzichita zinthu zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu” (31)

1 Akorinto 10:1

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Eks 13:21
  • +Eks 14:21, 22

1 Akorinto 10:3

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Eks 16:14, 15

1 Akorinto 10:4

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “linkatanthauza.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Eks 17:6
  • +Nu 20:11; Yoh 4:10, 25

1 Akorinto 10:5

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Nu 14:29, 35

1 Akorinto 10:6

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Nu 11:4, 34

1 Akorinto 10:7

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Eks 32:4, 6

1 Akorinto 10:8

Mawu a M'munsi

  • *

    MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Nu 25:1, 9

1 Akorinto 10:9

Mawu a M'munsi

  • *

    Onani Zakumapeto A5.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +De 6:16
  • +Nu 21:5, 6; Mt 4:7

1 Akorinto 10:10

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Nu 14:2
  • +Nu 14:36, 37

1 Akorinto 10:11

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aro 15:4

1 Akorinto 10:12

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Miy 28:14; Lu 22:33, 34; Aga 6:1

1 Akorinto 10:13

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Pe 5:8, 9
  • +Lu 22:31, 32; 2Pe 2:9
  • +Yes 40:29; Afi 4:13

1 Akorinto 10:14

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “thawani.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +De 4:25, 26; 2Ak 6:17; 1Yo 5:21

1 Akorinto 10:16

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mt 26:27, 28
  • +Mt 26:26; Lu 22:19; 1Ak 12:18

1 Akorinto 10:17

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aro 12:5

1 Akorinto 10:18

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “Aisiraeli akuthupi.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Le 7:15

1 Akorinto 10:20

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +De 32:17
  • +Yuda 6

1 Akorinto 10:21

Mawu a M'munsi

  • *

    Onani Zakumapeto A5.

  • *

    Onani Zakumapeto A5.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Eze 41:22; Mki 1:12

1 Akorinto 10:22

Mawu a M'munsi

  • *

    Onani Zakumapeto A5.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Eks 34:14; De 32:21

1 Akorinto 10:23

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aro 14:19; 15:2

1 Akorinto 10:24

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 10:32, 33; 13:4, 5; Afi 2:4

1 Akorinto 10:26

Mawu a M'munsi

  • *

    Onani Zakumapeto A5.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Sl 24:1; 1Ti 4:4

1 Akorinto 10:28

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 8:7, 10

1 Akorinto 10:29

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aro 14:15, 16; 1Ak 8:12

1 Akorinto 10:30

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aro 14:6; 1Ti 4:3

1 Akorinto 10:31

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mt 5:16; Akl 3:17

1 Akorinto 10:32

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aro 14:13; 1Ak 8:13; 2Ak 6:3

1 Akorinto 10:33

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aro 15:2; Afi 2:4
  • +1Ak 9:22

Malemba Ena

1 Akor. 10:1Eks 13:21
1 Akor. 10:1Eks 14:21, 22
1 Akor. 10:3Eks 16:14, 15
1 Akor. 10:4Eks 17:6
1 Akor. 10:4Nu 20:11; Yoh 4:10, 25
1 Akor. 10:5Nu 14:29, 35
1 Akor. 10:6Nu 11:4, 34
1 Akor. 10:7Eks 32:4, 6
1 Akor. 10:8Nu 25:1, 9
1 Akor. 10:9De 6:16
1 Akor. 10:9Nu 21:5, 6; Mt 4:7
1 Akor. 10:10Nu 14:2
1 Akor. 10:10Nu 14:36, 37
1 Akor. 10:11Aro 15:4
1 Akor. 10:12Miy 28:14; Lu 22:33, 34; Aga 6:1
1 Akor. 10:131Pe 5:8, 9
1 Akor. 10:13Lu 22:31, 32; 2Pe 2:9
1 Akor. 10:13Yes 40:29; Afi 4:13
1 Akor. 10:14De 4:25, 26; 2Ak 6:17; 1Yo 5:21
1 Akor. 10:16Mt 26:27, 28
1 Akor. 10:16Mt 26:26; Lu 22:19; 1Ak 12:18
1 Akor. 10:17Aro 12:5
1 Akor. 10:18Le 7:15
1 Akor. 10:20De 32:17
1 Akor. 10:20Yuda 6
1 Akor. 10:21Eze 41:22; Mki 1:12
1 Akor. 10:22Eks 34:14; De 32:21
1 Akor. 10:23Aro 14:19; 15:2
1 Akor. 10:241Ak 10:32, 33; 13:4, 5; Afi 2:4
1 Akor. 10:26Sl 24:1; 1Ti 4:4
1 Akor. 10:281Ak 8:7, 10
1 Akor. 10:29Aro 14:15, 16; 1Ak 8:12
1 Akor. 10:30Aro 14:6; 1Ti 4:3
1 Akor. 10:31Mt 5:16; Akl 3:17
1 Akor. 10:32Aro 14:13; 1Ak 8:13; 2Ak 6:3
1 Akor. 10:33Aro 15:2; Afi 2:4
1 Akor. 10:331Ak 9:22
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
  • 17
  • 18
  • 19
  • 20
  • 21
  • 22
  • 23
  • 24
  • 25
  • 26
  • 27
  • 28
  • 29
  • 30
  • 31
  • 32
  • 33
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
1 Akorinto 10:1-33

Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto

10 Tsopano abale, ndikufuna mudziwe kuti makolo athu akale, onse anali pansi pa mtambo+ ndipo onse anawoloka nyanja.+ 2 Onse anabatizidwa mwa Mose, kudzera mu mtambo ndi nyanja. 3 Onse ankadya chakudya chauzimu chofanana.+ 4 Ndipo onse ankamwa madzi auzimu ofanana.+ Chifukwa ankamwa pathanthwe lauzimu limene linkawatsatira, ndipo thanthwelo linali* Khristu.+ 5 Ngakhale zinali choncho, ambiri a iwo Mulungu sanakondwere nawo ndipo anaphedwa mʼchipululu.+

6 Zinthu zimenezi ndi zitsanzo kwa ife, kuti nafenso tisamalakelake zinthu zoipa ngati mmene iwo anachitira.+ 7 Ndipo tisamalambire mafano ngati mmene ena a iwo anachitira, mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Anthu anakhala pansi ndipo anadya ndi kumwa. Kenako anaimirira nʼkuyamba kusangalala.”+ 8 Komanso tisamachite chiwerewere,* mmene ena a iwo anachitira, nʼkufa anthu 23,000 tsiku limodzi.+ 9 Tisamamuyesenso Yehova,* mmene ena a iwo anamuyesera,+ nʼkufa atalumidwa ndi njoka.+ 10 Tisakhalenso ongʼungʼudza, ngati mmene ena a iwo anachitira,+ nʼkuphedwa ndi mngelo wowononga.+ 11 Zinthu zimene zinawachitikirazi ndi zitsanzo kwa ife ndipo zinalembedwa kuti zitichenjeze ifeyo+ amene tikukhala kumapeto a nthawi ino.

12 Choncho amene akuganiza kuti waima bwinobwino asamale kuti asagwe.+ 13 Palibe mayesero amene mwakumana nawo osiyana ndi amene anthu ena amakumana nawo.+ Koma Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire,+ koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.+

14 Choncho okondedwa anga, pewani* kulambira mafano.+ 15 Ndikulankhula nanu ngati anthu ozindikira. Weruzani nokha ngati zimene ndikunenazi nʼzoona. 16 Kodi kapu ya madalitso imene timadalitsa, sitanthauza kugawana magazi a Khristu?+ Kodi mkate umene timaugawagawa, sutanthauza kugawana thupi la Khristu?+ 17 Popeza pali mkate umodzi, ifeyo, ngakhale kuti tilipo ambiri, ndife thupi limodzi,+ chifukwa tonse tikudya nawo mkate umodziwo.

18 Taganizirani zimene Aisiraeli* amachita: Kodi amene amadya zinthu zoperekedwa paguwa la nsembe si ndiye kuti amakhala ngati akudya ndi Mulungu?+ 19 Kodi mfundo yake ndi yotani? Kodi zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano kapena mafano enieniwo ndi kanthu? 20 Ayi, koma ndikutanthauza kuti zinthu zimene anthu a mitundu ina amapereka nsembe amazipereka kwa ziwanda, osati kwa Mulungu.+ Ndipo sindikufuna kuti muzichita chilichonse chogwirizana ndi ziwanda.+ 21 Sizingatheke kuti muzimwa zamʼkapu ya Yehova* komanso zamʼkapu ya ziwanda. Sizingathekenso kuti muzidya “patebulo la Yehova”*+ komanso patebulo la ziwanda. 22 Kapena ‘kodi tikufuna kuti Yehova* achite nsanje?’+ Kodi mphamvu zathu zingapose mphamvu zake?

23 Zinthu zonse nʼzololeka, koma si zonse zimene zili zaphindu. Zinthu zonse nʼzololeka, koma si zonse zomwe zimalimbikitsa.+ 24 Aliyense asamangofuna zopindulitsa iyeyo basi, koma zopindulitsanso ena.+

25 Muzidya chilichonse chogulitsidwa pamsika wa nyama muli ndi chikumbumtima chabwino ndipo musafunse mafunso. 26 Chifukwa “dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo ndi za Yehova.”*+ 27 Ngati munthu wosakhulupirira wakuitanani ndipo mukufuna kupita, kadyeni chilichonse chimene wakupatsani muli ndi chikumbumtima chabwino ndipo musafunse mafunso. 28 Koma wina akakuuzani kuti: “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo kuopera amene wakuuzaniyo ndiponso chikumbumtima.+ 29 Sindikunena chikumbumtima chako, koma cha munthu winayo. Sindikufuna kuti ndizigwiritsa ntchito ufulu wanga kenako nʼkumaweruzidwa ndi chikumbumtima cha munthu wina.+ 30 Ngakhale nditakhala ndi ufulu wodya chakudyacho nʼkuyamika Mulungu, kodi ndi bwino kuchita zimenezo ngati zingachititse kuti anthu ena andinyoze?+

31 Choncho kaya mukudya kapena kumwa, kapena kuchita china chilichonse, muzichita zinthu zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.+ 32 Muzipewa kukhumudwitsa Ayuda, Agiriki ndiponso mpingo wa Mulungu.+ 33 Zimenezi ndi zimene inenso ndikuyesetsa kuchita. Ndikuyesetsa kusangalatsa anthu onse pa zonse zimene ndikuchita. Sindikufuna zopindulitsa ine ndekha,+ koma zopindulitsa anthu ambiri kuti apulumutsidwe.+

Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani